Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g 3/10 tsamba 9
  • Zinalipo Kale M’chilengedwe

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zinalipo Kale M’chilengedwe
  • Galamukani!—2010
  • Nkhani Yofanana
  • Zipangizo Zolozera Malo
    Galamukani!—2010
  • Kamba Wam’madzi Amalondola Njira Mogometsa Kwambiri
    Galamukani!—2011
  • Zimene Tingaphunzire kwa Mbalame
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2016
  • Mmene Gulugufe Amadziwira Komwe Akupita
    Galamukani!—2008
Onani Zambiri
Galamukani!—2010
g 3/10 tsamba 9

Zinalipo Kale M’chilengedwe

“Inde, chumba cha mlengalenga chidziwa nyengo zake.”—Yeremiya 8:7.

YEREMIYA analemba za mbalame imeneyi, yotchedwa chumba, zaka 2,500 zapitazo. Masiku anonso, anthu amagoma ndi zamoyo zimene zimayenda maulendo aatali popanda kusochera. Mwachitsanzo, nsomba ya salimoni imatha kuyenda ulendo wamakilomita masauzande ambiri n’kubwereranso kumalo amene inabadwira. Palinso akamba enaake am’madzi amene amayenda makilomita 20,000 kuchokera ku Indonesia kukafika kugombe la ku Oregon, ku United States, ndipo amabwereranso ku Indonesia kukabereka.

Koma pali zamoyo zinanso zimene zili ndi luso lotha kulondola malo kuposa nyama zimene tafotokozazi. Mwachitsanzo, anthu ena anatenga pa ndege mbalame zinazake zam’madzi zooneka ngati abakha zokwana 18, kuchokera pakachilumba kenakake ka m’nyanja ya Pacific n’kukazisiya m’madera osiyanasiyana akutali kwambiri. Koma patangopita milungu yochepa, mbalame zambiri zinabwerera kwawo.

Anthu ena anayesapo kusamutsa nkhunda n’kukazisiya dera lina pa mtunda wa makilomita 150. Pozinyamulapo anazipatsa mankhwala ogonetsa kapena kuziika m’migolo kuti zisadziwe komwe zikupita. Koma atazisiya, m’nthawi yochepa chabe zinazindikira kwawo ndipo zinabwerera. Popeza kuti nkhunda zimatha kulondola malo ngakhale zitaphimbidwa kumaso, akatswiri akukhulupirira kuti nkhunda zimatha kuzindikira malo amene zili ndiponso amene zikufuna kupita chifukwa chakuti mwachibadwa zimatha kudziwa malo.

Pali agulugufe enaake omwe amakhala kudera lalikulu kwambiri la ku North America amene amayenda ulendo wa makilomita masauzande ambiri kupita ku kadera kenakake kakang’ono ka ku Mexico. Ngakhale kuti agulugufewa sanakhalepo ku Mexico, iwo amakwanitsa kubwerera ndipo chaka chotsatira amakafika pamtengo weniweni umene makolo awo ankakhala. Akatswiri samvetsa kuti zimatheka bwanji kuti agulugufewa azikwanitsa kuchita zimenezi.

Tizipangizo tolozera malo timadalira setilaiti kuti tisonyeze malo oyenerera. Koma zamoyo zambiri zimadalira zinthu monga mapiri, dzuwa, fungo, phokoso komanso mphamvu yokoka ya dziko lapansi kuti zilondole malo. Pulofesa wina wa zinthu zamoyo dzina lake James L. Gould analemba kuti: “Zamoyo zonse zimene zimatha kuyenda mtunda wautali osasochera, zinapangidwa modabwitsa kwambiri. . . . Zimagwiritsa ntchito zinthu zosiyanasiyana kuti zisasochere. Njira imodzi ikalephera zimagwiritsa ntchito ina mpaka zimakafika kumene zikupita.” Akatswiri ambiri amagoma akaganizira mmene zamoyo zimalondolera malo.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena