Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g 7/10 tsamba 17-31
  • Zoti Banja Likambirane

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zoti Banja Likambirane
  • Galamukani!—2010
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Pachithunzipa Pakusoweka Chiyani?
  • KODI MUKUDZIWA CHIYANI ZOKHUDZA MTUMWI YUDASI ISIKARIYOTI?
  • ZITHUNZI ZOTI ANA APEZE
  • KUCHOKERA M’MAGAZINI INO
  • MAYANKHO A MAFUNSO A PATSAMBA 31
  • Zoti Banja Likambirane
    Galamukani!—2010
  • Kodi Mungayankhe Bwanji?
    Galamukani!—2008
  • Kodi Mungayankhe Bwanji?
    Galamukani!—2009
  • Kodi Mungayankhe Bwanji?
    Galamukani!—2009
Onani Zambiri
Galamukani!—2010
g 7/10 tsamba 17-31

Zoti Banja Likambirane

Kodi Pachithunzipa Pakusoweka Chiyani?

Werengani Maliko 1:9-11. Ndiyeno onani chithunzichi. Kodi pakusoweka chiyani? Lembani mayankho anu pamizere ili m’munsiyi. Kenako malizitsani kujambula chithunzichi pojambula zinthu zimene zikusowekapo komanso kuchichekenira.

1. ․․․․․

2. ․․․․․

KAMBIRANANI:

Kodi zifukwa zina zimene Akhristu amabatizidwira n’zotani?

ZOKUTHANDIZANI: Werengani Maliko 8:34; 1 Petulo 2:21; 3:21.

Kodi mukuganiza kuti munthu ayenera kubatizidwa ali ndi zaka zingati? N’chifukwa chiyani mukuyankha choncho?

KODI MUKUDZIWA CHIYANI ZOKHUDZA MTUMWI YUDASI ISIKARIYOTI?

3. Kodi Yudasi anapatsidwa ntchito yotani imene atumwi ena sanapatsidwe?

ZOKUTHANDIZANI: Werengani Yohane 13:29.

․․․․․

4. Kodi Yudasi anachita tchimo lotani?

ZOKUTHANDIZANI: Werengani Yohane 12:6.

․․․․․

KAMBIRANANI:

Kodi mukuganiza kuti Yudasi anachita tchimo limeneli chifukwa chiyani? Kodi ndi pazochitika zotani zimene inuyo mungayesedwe kuti muchite tchimo ngati limeneli? Kodi kuganizira nkhani ya Yudasi kungakuthandizeni bwanji kuti musachite tchimo?

ZITHUNZI ZOTI ANA APEZE

Pezani zithunzi izi m’magazini ino. Kenako fotokozani zimene zikuchitika pa chithunzi chilichonse.

KUCHOKERA M’MAGAZINI INO

Yankhani mafunsowa, ndipo lembani vesi kapena mavesi a m’Baibulo omwe akusowapo.

TSAMBA 4 Kodi tsiku lililonse limakhala ndi chiyani chokwanira pa tsikulo? Mateyo 6:․․․

TSAMBA 9 Kodi Atate wathu wakumwamba analonjeza kuti mulimonse sadzatani? Aheberi 13:․․․

TSAMBA 10 Kodi kuchokera pa chiyambi Mulungu anafuna kuti mwamuna azichita chiyani? Maliko 10:․․․

TSAMBA 29 Kodi akazi achikulire angathandize akazi ocheperapo kuchita chiyani? Tito 2:․․․

● Mayankho ali patsamba 17

MAYANKHO A MAFUNSO A PATSAMBA 31

1. Yohane M’batizi.

2. Nkhunda.

3. Ankasunga bokosi la ndalama.

4. Ankafuna ndalama ndipo anayamba kuba.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena