Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g 12/10 tsamba 25
  • Nsomba za Salimoni Zimasambira Mogometsa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Nsomba za Salimoni Zimasambira Mogometsa
  • Galamukani!—2010
  • Nkhani Yofanana
  • Dziko Lathuli Likusakazidwa Kwabasi
    Galamukani!—2005
  • Mbalame N’zaluso pa Usodzi
    Galamukani!—2011
  • Gulu la Nsomba Losambira Mogometsa
    Galamukani!—2012
  • Nsomba Zikakudwalitsani
    Galamukani!—2006
Onani Zambiri
Galamukani!—2010
g 12/10 tsamba 25

Panagona Luso!

Nsomba za Salimoni Zimasambira Mogometsa

● Nsomba zambiri za mtundu wa salimoni zikafuna kuikira mazira, zimasambira mumtsinje molowera kumene madzi akuchokera. Zikamasambira zimapezana ndi madzi owinduka amene amakhala ovuta kusambira. Kodi nsombazi zimatha bwanji kuyenda ulendo wovutawu koma osatopa? M’malo movutika ndi madzi owindukawa, nsombazi zimawagwiritsira ntchito mwanzeru. Kodi zimachita zimenezi motani?

Taganizirani izi: Nsombazi sizilimbana ndi madzi owinduka. M’malomwake zikamasambira, zimakonda kudutsa m’malo amene madzi akuyenda mozungulira chifukwa chakuti madziwo amamenya miyala, nthambi za mitengo, kapena zinthu zina. Zimenezi zimathandiza kuti zisawononge mphamvu zambiri. Popeza madzi amayenda mozungulira kumbali zonse ziwiri za chinthu chomwe amenyacho, nazonso nsombazi zimapindapinda matupi awo potsatira madzi amene akuyenda mozungulirawo. (Onani chithunzi.) Magulu ena a nsomba amasambira m’madzi amene amayenda mozungulira atavundulidwa ndi nsomba zimene zikusambira patsogolo pawo. Nsombazi zimathanso kusambira m’madzi amene akuyenda mozungulira chifukwa chovundulidwa ndi matupi awo omwe.

Anthu ochita kafukufuku akuganizira zotengera zimene nsombazi zimachita kuti azitha kupanga magetsi pogwiritsa ntchito madzi oyenda pang’onopang’ono. Nthawi zambiri anthu akafuna kupanga magetsi pogwiritsa ntchito madzi, madziwo amafunika kuti azithamanga makilomita 9.3 pa ola limodzi, kapena kuposa pamenepa. Koma panopa apanga makina enaake amene amatha kugwiritsira ntchito mphamvu ya kuwinduka kwa madzi n’kupanga magetsi pogwiritsa ntchito madzi amene akuyenda pang’onopang’ono kwambiri, mwina makilomita 3.7 okha pa ola limodzi.a Komabe, luso limene anthu akugwiritsira ntchito panopa n’lotsalira kwambiri poyerekezera ndi luso la nsomba ngati salimoni. Pulofesa Michael Bernitsas wa pa yunivesite ya Michigan, ku U.S.A. anati: “Pa nkhani imeneyi, tili m’mbuyo kwambiri poyerekezera ndi nsomba.”

Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi zinangochitika zokha kuti nsomba za salimoni zisamavutike kusambira m’madzi owinduka, kapena alipo amene anazipanga mwanjira imeneyi?

[Mawu a M’munsi]

a Luso limeneli lingathandize kwambiri, chifukwa madzi ambiri padzikoli amayenda pang’onopang’ono kwambiri, osafika makilomita 5.6 pa ola limodzi.

[Mawu a Chithunzi patsamba 25]

Top: © photolibrary. All rights reserved

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena