Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g 12/10 tsamba 29
  • Zochitika Padzikoli

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zochitika Padzikoli
  • Galamukani!—2010
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Zivomezi “Zikupha Kwambiri Anthu Kuposa Tsoka Lililonse”
  • Ntchito Yoopsa Kwambiri
  • Katundu Wotsika Mtengo Akuchepetsa Umbava
  • N’chifukwa Chiyani Masoka Achilengedwe Achuluka Chonchi?
    Nsanja ya Olonda—2011
  • Kodi Baibulo Limanena Zotani pa Nkhani ya Ngozi Zadzidzidzi?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Mmene Zivomezi ndi Maulosi a Baibulo Zimakukhudzirani
    Galamukani!—2002
  • Masoka Achilengedwe—Kodi Ali Chizindikiro cha Nthaŵi?
    Nsanja ya Olonda—1993
Onani Zambiri
Galamukani!—2010
g 12/10 tsamba 29

Zochitika Padzikoli

Dipatimenti ya boma yoona za zipembedzo m’dziko la Serbia yalandira chikalata cha Mboni za Yehova chopempha kuti ntchito yawo ikhale yovomerezedwa ndi boma. Malinga ndi kaundula wa boma, Mboni za Yehova zakhala zili m’dzikoli kuyambira m’chaka cha 1930.

Akuti pa nyimbo 100 zilizonse zimene anthu anakopera pa Intaneti m’chaka cha 2009, pafupifupi 95 zinakopedwa mophwanya lamulo.—TIME, U.S.A.

Zivomezi “Zikupha Kwambiri Anthu Kuposa Tsoka Lililonse”

Bungwe lina loona za mmene anthu angachepetsere masoka, lomwe likulu lake lili ku Geneva m’dziko la Switzerland, linanena kuti “pa masoka onse amene akhala akuchitika pa zaka 10 zapitazi, zivomezi n’zimene zikupha kwambiri anthu kuposa tsoka lililonse.” Pa anthu onse amene aphedwa ndi masoka pa zaka zimenezi, anthu pafupifupi 60 pa anthu 100 alionse anafa ndi zivomezi. Zivomezi, zomwe zili m’gulu la “masoka achilengedwe,” zikuoneka kuti zipitirizabe kupha anthu chifukwa pa mizinda 10 imene ili ndi anthu ambiri padziko lonse, 8 ili pamalo oti pakhoza kuchitika chivomezi nthawi ina iliyonse. Pa zaka 10 zapitazi, anthu oposa 780,000 anafa pa masoka osiyanasiyana okwana 3,852.

Ntchito Yoopsa Kwambiri

Bungwe loona za atolankhani padziko lonse, lomwe likulu lake lili ku Vienna m’dziko la Austria, linati: “M’chaka cha 2009, atolankhani okwana 110 anaphedwa pogwira ntchito yawo. Zimenezi zikutanthauza kuti m’chaka chimenechi atolankhani anaphedwa kwambiri kuposa chaka china chilichonse pa zaka 10 zapitazi.” Bungwelo linanena kuti m’zaka zaposachedwapa, m’mayiko amene muli nkhondo, monga ku Afghanistan, Iraq, Pakistan, ndi Somalia, anthu “akumachita kuchalira kuti aphe atolankhani.” Zimenezi zachititsa kuti nkhani zambiri zochitika m’mayiko amenewa zisamalembedwe. Pa chifukwa chimenechi, “anthu sakudziwa nkhani zoopsa zimene zikuchitika” m’mayikowa. Dziko la Iraq ndi limene linali loopsa kwambiri kwa atolankhani pa zaka 10 zapitazi. Lotsatira linali la Philippines, kenako Colombia, Mexico, ndi Russia.

Katundu Wotsika Mtengo Akuchepetsa Umbava

Nkhani ina imene inalembedwa ndi bungwe lolemba nkhani la Reuters ku London, inagwira mawu mphunzitsi wina wa nkhani zokhudza umbava, wa pa yunivesite ya Leicester, ku England, dzina lake James Treadwell. Iye anati: “Chifukwa cha kuchuluka kwa katundu wotchipa wamagetsi amene akulowa m’dziko la Britain,” mwina mbava sizizibanso kwambiri katundu m’nyumba za anthu. Mwachitsanzo, chifukwa chakuti mawailesi atsopano a DVD ndi otchipa kwambiri masiku ano, munthu sangapange ndalama zilizonse atagulitsa wailesi ya DVD yakuba. Treadwell anati masiku ano, zinthu ngati zimenezi “n’zopanda phindu lililonse kwa mbava.” Komabe, kutsika mtengo kwa zinthu sikunachititse kuti umbava utheretu. M’malomwake mbava zayamba kumaba zinthu zodula komanso zimene sizingavute kuzipezera msika, monga ‘mafoni a m’manja ndi timawailesi tamakono tam’manja, timene anthu amayenda nato.’ Choncho anthu amene kale ankaba katundu m’nyumba za anthu ayamba kuchita umbava wamtundu wina, monga kubera anthu m’misewu.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena