Kodi Zolinga Zimene Muli Nazo N’zotheka Kuzikwaniritsa?
● Kodi pa moyo wanu mumafuna mutachita chiyani? Kodi zimene mumafunazo n’zotheka kuzikwaniritsa, kapena mumangolakalaka zinthu zomwe simungazikwanitse? Munthu wina amene ankadziwa bwino zimene zimachitika pa moyo wa munthu anapereka malangizo anzeru awa: “Kuona ndi maso kuli bwino kuposa kulakalaka ndi mtima. Izinso n’zachabechabe ndipo zili ngati kuthamangitsa mphepo.”—Mlaliki 6:9.
Mawu akuti “kuona ndi maso” akutanthauza mmene zinthu zilili pa moyo wathu. Kunena zoona, si kulakwa kufuna kukhala ndi moyo wabwino. Komabe, mfundo imene ili pa vesili ndi yakuti, anthu anzeru sataya nthawi n’kufunafuna zinthu zimene sangathe kuzikwaniritsa. Zinthu zake zikhoza kukhala kufuna kutchuka, kulemera, kupeza mkazi kapena mwamuna wopanda vuto lililonse, kapena kufuna kukhala ndi thanzi labwino kwambiri.
Komanso, munthu akakwanitsa kupeza chinthu chinachake chimene amafuna, monga chuma, amafunabe zinthu zina zowonjezereka. Baibulo limanena mosapita m’mbali kuti: “Munthu wokonda siliva sakhutira ndi siliva, ndipo wokonda chuma sakhutira ndi phindu limene amapeza. Zimenezinso n’zachabechabe.” (Mlaliki 5:10) Choncho, anthu amene amayendera nzeru za Mulungu amayesetsa kukhala okhutira ndi zimene ali nazo, kapena kuti zinthu zimene ‘amaona ndi maso.’ Iwo amavomereza mfundo yosatsutsika yakuti: “Sitinabwere ndi kanthu m’dziko, ndipo sitingatulukemo ndi kanthu.”—1 Timoteyo 6:7.
Malinga ndi mmene tinalengedwera, anthufe timasangalala kwambiri tikamakwaniritsa zosowa zathu zauzimu. (Mateyu 5:3) Kodi tingazikwaniritse bwanji? Yesu Khristu anati: “Munthu sangakhale ndi moyo ndi chakudya chokha, koma ndi mawu onse otuluka pakamwa pa Yehova.” (Mateyu 4:4) Mawu otuluka pakamwa pa Yehova amapezeka m’Baibulo, ndipo tikhoza kuwawerenga n’kuwagwiritsa ntchito.
Ena mwa mawu amenewa amapezeka pa Salimo 37:4. Lembali limati: “Sangalala mwa Yehova, ndipo adzakupatsa zokhumba za mtima wako.” Popeza kuti Yehova ndi Mulungu Wamphamvuyonse, adzapatsa atumiki ake okhulupirika zinthu zimene anthu sangathe kupereka, monga thanzi labwino, zonse zimene munthu amafunikira pa moyo, ndiponso moyo wosatha m’Paradaiso padziko lapansi. (Luka 23:43; Chivumbulutso 21:3, 4) Kukhulupirira mawu amenewa si kulakalaka zinthu zosatheka.