Kuvomereza Kuti Zachitika
“Nditamva zoti bambo anga amwalira, ndinali ndi chisoni chachikulu ndipo ndinkaona kuti chilichonse chasokonekera. Ndinkadziimba mlandu kwambiri chifukwa pa nthawi imene ankamwalira n’kuti ine ndili kwina. Palibe chinthu chinanso chopweteka kwambiri kuposa imfa ya munthu amene umamukonda. Ndimawasowa kwambiri bambo anga.”—Anatero Sara.
ANTHU ambiri, kaya akhale achikhalidwe kapena chipembedzo chanji, sakonda kulankhula za imfa. Ndipo m’zinenero zina muli mawu amene anthu amalankhula n’cholinga choti munthu amene akuuzidwa uthenga wa maliro asachite mantha kwambiri. Mwachitsanzo, mu Chichewa m’malo monena kuti uje “wamwalira,” anthu amanena kuti uje “watisiya,” “wapita,” kapena “wagona.”
Komabe, ngakhale titayesetsa kwambiri kugwiritsa ntchito mawu abwino, anthu amene aferedwa amakhalabe ndi chisoni chachikulu. Ena zimawavuta kuvomereza kuti munthuyo wamwaliradi.
Ngati munthu amene munkamukonda kwambiri wamwalira, mwina inunso zikukuvutani kuvomereza kuti munthuyo kulibenso. Mwina pamaso pa anthu mungamasonyeze kuti zinthu zili bwinobwino pamene mumtima mungakhale ndi chisoni chachikulu. Komabe muyenera kudziwa kuti anthu amasonyeza chisoni mosiyanasiyana. Ngati munthu sakulira, si ndiye kuti alibiretu chisoni.a Komabe pangakhale vuto ngati munthu akuziumiriza kuti asalire n’cholinga chofuna kusonyeza anthu ena, monga achibale, kuti iye ndi wolimba mtima.
“Ndinalibiretu Mpata Wolira”
Taganizirani zimene ananena Nathaniel, yemwe mayi ake anamwalira iye ali ndi zaka 24. Nathaniel anati: “Mayi anga atamwalira, ndinasokonezeka kwambiri maganizo. Ndinkaona kuti ndili ndi udindo wotonthoza bambo anga komanso anzawo ambirimbiri a mayi anga. Ndinalibiretu mpata wolira.”
Patadutsa chaka chimodzi, Nathaniel ankaonabe kuti zikumuvuta kuiwala imfa ya mayi ake. Iye anati: “Mpaka pano bambo amaimba foni n’cholinga chondiuza nkhawa zawo. Ndimaona kuti amachita bwino kufotokoza mmene akumvera, ndipo ineyo ndimasangalala kuwathandiza. Koma vuto ndi lakuti ineyo ndikafuna kulimbikitsidwa, ndimasowa kopita.”
Anthu amene amasamalira odwala, kuphatikizapo madokotala ndi manesi, nthawi zambiri amaona anthu akumwalira. Zikatero amakhala ndi chisoni chachikulu, ngakhale kuti nthawi zina amadzikakamiza kuti asalire. Mwachitsanzo, taganizirani za Heloisa, yemwe wakhala akugwira ntchito ya udokotala kwa zaka zoposa 20. Mayiyu ankagwira ntchito m’dera limene anthu ake anali ogwirizana kwambiri ndipo iye ankakondana kwambiri ndi odwala ake. Iye anati: “Ambiri mwa anthuwa ankamwalira ine ndikuwaona ndipo ena mwa iwo anali anzanga apamtima.”
Heloisa ankadziwa kuti kulira kumathandiza kuti chisoni chichepe. Komabe iye anati: “Ineyo zinkandivuta kulira. Ndinkaona kuti ndifunika kukhala wolimba kuti ndithe kulimbikitsa ena. Ndinkakhulupirira kuti zimenezi n’zimene enawo akuyembekezera kwa ine.”
“Panyumba Sipankasangalatsanso”
Vuto lalikulu limene anthu oferedwa amakumana nalo ndi kusungulumwa. Mwachitsanzo, mtsikana wina dzina lake Ashley, amene mayi ake anamwalira ndi matenda a khansa iye ali ndi zaka 19, anati: “Mayi anga atamwalira, ndinkasowa wocheza naye chifukwa pa nthawi imene iwo anali moyo, tinkagwirizana kwambiri moti nthawi zambiri tinkachitira zinthu limodzi.”
Tsiku lililonse, Ashley akabwerera kunyumba n’kupeza kuti mayi ake kulibe, ankamva chisoni kwambiri. Iye anati: “Panyumba sipankasangalatsanso. Nthawi zambiri ndinkangolowa kuchipinda kwanga n’kuyamba kulira kwinaku ndikuyang’ana zithunzi zawo komanso kuganizira zinthu zimene tinkachitira limodzi.”
Ngati mnzanu kapena wachibale wanu anamwalira, dziwani kuti pali zimene mungachite kuti musakhale ndi chisoni kwambiri. Monga mmene tionere m’nkhani yotsatira, pali anthu enanso ambiri amene achibale awo anamwalira koma panopa apeza njira zochepetsera chisoni chawo.
[Mawu a M’munsi]
a Popeza anthu amasonyeza chisoni mosiyanasiyana, kungakhale kulakwa kunena kuti munthu amene sakulira ndiye kuti sakukhudzidwa ndi imfayo.
[Mawu Otsindika patsamba 5]
“Mayi anga atamwalira, ndinkasowa wocheza naye chifukwa pa nthawi imene iwo anali moyo, tinkagwirizana kwambiri”—Anatero Ashley