Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g 1/12 tsamba 27-30
  • Zoti Banja Likambirane

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zoti Banja Likambirane
  • Galamukani!—2012
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Chithunzichi Chalakwika Pati?
  • Sungani Kuti Muzikumbukira
  • Anthu ndi Mayiko
  • Zithunzi Zoti Ana Apeze
  • MAYANKHO A MAFUNSO A PATSAMBA 30 NDI 31
  • Zoti Banja Likambirane
    Galamukani!—2012
  • Zoti Banja Likambirane
    Galamukani!—2012
  • Zoti Banja Likambirane
    Galamukani!—2012
  • Zoti Banja Likambirane
    Galamukani!—2012
Onani Zambiri
Galamukani!—2012
g 1/12 tsamba 27-30

Zoti Banja Likambirane

Kodi Chithunzichi Chalakwika Pati?

Werengani Genesis 24:1-4, 10–23. Tchulani zinthu zitatu zimene zalakwika pachithunzichi. Lembani mayankho anu m’mizere ili m’munsiyi, ndipo malizitsani kujambula zithunzizi pozikongoletsa ndi chekeni.

1. ․․․․․

2. ․․․․․

3. ․․․․․

KAMBIRANANI:

Kodi Rabeka anali ndi makhalidwe abwino ati?

ZOKUTHANDIZANI: Werengani Miyambo 31:17, 27, 29-31; 1 Petulo 4:9.

Kodi mungatsanzire bwanji Rabeka?

ZOKUTHANDIZANI: Werengani Miyambo 11:25; Aroma 12:11.

ZOTI BANJA LICHITIRE PAMODZI:

Lembani dzina la munthu amene mukufuna kumuthandiza. Kenako, lembani zinthu zimene mungachite kuti muthandize munthuyo. Onetsani anthu a m’banja lanu zimene mwalembazo. Kambiranani zimene nonse mungachite kuti muthandize munthu ameneyo komanso nthawi imene mudzamuthandize. Mukamuthandiza, kambirananinso ndi banja lanu mmene munamvera mutathandiza munthuyo.

Sungani Kuti Muzikumbukira

Dulani, pindani pakati n’kusunga

KHADI LA BAIBULO 13 YOBU

MAFUNSO

A. Ana onse a Yobu aamuna anali ․․․․․ ndi ana onse a Yobu aakazi anali ․․․․․.

B. Kodi Satana anawononga chiyani cha Yobu?

C. Malizitsani mawu amene Yobu ananena akuti: “Mpaka ine kumwalira, sindidzasiya kukhala ndi . . . “

[Tchati]

4026 B.C.E. Kulengedwa kwa Adamu

Anakhala ndi moyo cha m’ma 1600 B.C.E.

1 C.E.

98 C.E. Baibulo linamalizidwa kulembedwa

[Mapu]

Ankakhala ku Uzi

DZIKO LOLONJEZEDWA

IGUPUTO

UZI?

YOBU

ANALI NDANI?

Anali “munthu wopanda cholakwa ndi wowongoka mtima” pamaso pa Mulungu. (Yobu 1:8) Yobu sanasiye kutumikira Mulungu ngakhale kuti mkazi wake komanso anthu ena ankamukakamiza kuti asiye. (Yobu 1:20-22; 2:9, 10) Chitsanzo chake pa nkhani ya kupirira komanso madalitso amene anapeza zimatilimbikitsa kuti nafenso tizipirira mokhulupirika tikakumana ndi mavuto.—Yobu 42:12-17; Yakobo 5:11.

MAYANKHO

A. 14, 6.—Yobu 1:2; 42:13.

B. Ziweto zake, antchito ake, ana ake komanso thanzi lake.—Yobu 1:13-19; 2:4-7.

C. “. . . mtima wosagawanika.”—Yobu 27:5.

Anthu ndi Mayiko

4. Dzina langa ndine Lukas. Ndili ndi zaka 7 ndipo ndimakhala ku Germany. Kodi mukudziwa kuti ku Germany kuli Mboni za Yehova zingati? Kodi ziliko 60,000; 100,000 kapena 160,000?

5. Kodi ndi kadontho kati kamene kakusonyeza dziko limene ineyo ndimakhala? Lembani mzere wozungulira kadonthoko. Kenako jambulani kadontho kosonyeza kumene inuyo mumakhala kuti muone kuyandikana kwa dziko lanu ndi la Germany.

A

B

C

D

Zithunzi Zoti Ana Apeze

Pezani zithunzi izi m’magazini ino. Fotokozani zimene zikuchitika pa chithunzi chilichonse.

Nkhani zina zakuti “Zoti Banja Likambirane” mungazipeze pa adiresi yathu ya pa Intaneti ya www.jw.org.

● Mayankho a “ZOTI BANJA LIKAMBIRANE” ali patsamba 27

MAYANKHO A MAFUNSO A PATSAMBA 30 NDI 31

1. Payenera kukhala ngamila 10 osati 11.

2. Rabeka anathira madzi m’chomweramo ziweto osati m’migolo itatu.

3. Kapoloyo anapatsa Rabeka ndolo ya pamphuno ndi zibangili za pamkono ziwiri, osati tcheni cha m’khosi.

4. 160,000.

5. C.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena