Zoti Banja Likambirane
KODI TIKUPHUNZIRA CHIYANI KWA . . . Nowa?
KODI MUNAGANIZIRAPO CHIFUKWA CHAKE TIYENERA KUMVERA MULUNGU?
• Kongoletsani zithunzizi ndi chekeni. • Werengani mavesiwa ndipo muwafotokoze pomalizitsa mawu amene akusoweka. • Pezani zinthu zimene zikusoweka: (1) makwerero ndi (2) kangaude.
N’chifukwa chiyani tinganene kuti Nowa anachita bwino kumvera Mulungu?
ZOKUTHANDIZANI: Yeremiya 7:23; 2 Petulo 2:5.
N’chiyani chingatithandize kuti tizimvera Mulungu?
ZOKUTHANDIZANI: 1 Mbiri 28:9; Yesaya 48:17,18; 1 Yohane 5:3.
Kodi mwaphunzirapo chiyani mu nkhaniyi?
Kodi inuyo mukuganiza bwanji?
Kuti musonyeze kuti mumamvera Mulungu muyeneranso kumvera ndani?
ZOKUTHANDIZANI: Aefeso 6:1-3; Aheberi 13:7,17.
Sungani Kuti Muzikumbukira
KHADI LA BAIBULO 22 NEHEMIYA
MAFUNSO
A. Nehemiya ankagwira ntchito ngati ․․․․․ kwa mfumu ya ku Perisiya, dzina lake ․․․․․.
B. Kodi dzina lakuti Nehemiya limatanthauza kuti chiyani?
C. Iye anapemphera kuti: “Inu Mulungu wanga, mundikumbukire ․․․․․.”
MAYANKHO
A. Woperekera chikho, Aritasasita.—Nehemiya 1:11; 2:1.
B. “Ya Amatonthoza.”
C. “. . . pa zabwino zimene ndinachita.”—Nehemiya 13:31.
Anthu ndi Mayiko
Mayina athu ndi Taonga ndi Mwelwa, ndipo tili ndi zaka 6 ndi 8. Timakhala ku Zambia. Kodi mukudziwa kuti ku Zambia kuli Mboni za Yehova zingati? Kodi ziliko 90,000; 152,000, kapena 196,000?
Kodi ndi kadontho kati kamene kakusonyeza dziko limene ifeyo timakhala? Lembani mzere wozungulira kadonthoko. Kenako jambulani kadontho kosonyeza kumene inuyo mumakhala, kuti muone kuyandikana kwa dziko lanu ndi la Zambia.
Zithunzi Zoti Ana Apeze
Pezani zithunzi izi m’magazini ino. Fotokozani zimene zikuchitika pa chithunzi chilichonse.
MAYANKHO A MAFUNSO
Makwerero pachithunzi chachitatu.
Kangaude pachithunzi chachiwiri.
152,000.
C.