6 Muzidalira Mulungu Kuti Azikuthandizani
“Pamene mwamuna wanga anandithawa n’kundisiyira ana, ndinapempha Mulungu kuti atithandize ndipo anandiyankha. Kuyambira nthawi imeneyo sindisowa kanthu. Tikuona kuti Mulungu wakhala akutithandiza komanso kutitsogolera.”—ANATERO MAKI WA KU JAPAN.
MASIKU ano, anthu ambiri saganizira kwambiri za Mulungu. Komabe zoona zake n’zakuti Mulungu yemwe ndi Mlengi wathu amatidera nkhawa ndipo amafuna kuti zinthu zizitiyendera bwino pa moyo wathu. Timadziwa zimenezi chifukwa cha zimene ananena pa Yesaya 41:10, pomwe pamati: “Usachite mantha, pakuti ndili nawe. . . . ndithu ndikuthandiza.”
Nkhani yapita ija taona mmene Mulungu amatithandizira pogwiritsa ntchito malangizo a m’Baibulo. (2 Timoteyo 3:16) Koma sikuti Baibulo ndi buku lamalamulo basi. Limatiuzanso za makhalidwe a Mulungu komanso limatisonyeza kuti iye amatikonda. Makolo ambiri achikhristu, omwe ali pa banja kapena amene akulera okha ana, akamachita zimene Baibulo limaphunzitsa, amamvetsa mfundo yakuti Mulungu amatiganizira. Taonani zimene Akhristu ena ananena:
Robert, Austria: “Yehova Mulungu ali ngati bambo kapena mayi wabwino kwambiri kuposa anthufe. Iye amadziwa zimene ana athu amafunikira komanso amadziwa mmene angawatetezere. N’chifukwa chake ine ndi mwana wanga wamkazi timakonda kupemphera kwa Mulungu.”
Ayusa, Japan: “Ndimasangalala kwambiri mwana wanga akamanena kuti: ‘Tisadere nkhawa, zonse zikhala bwino chifukwa Yehova alinafe.’ Zimenezi zimandithandiza kudziwa kuti iye amadalira Mulungu.”
Cristina, Italy: “Ndikaona kuti mavuto andikulira, ndimapemphera kwa Yehova kuti andithandize. Ndikangomaliza kupemphera, mtima wanga umakhazikika chifukwa ndimadziwa kuti Yehova apeza njira yabwino yothetsera vutolo.”
Laurentine, France: “Sindikukayikira kuti Yehova wandithandiza kuti ndilere bwino ndekha ana anga. Ndaona kuti iye amapulumutsadi anthu osautsika ndi ana amasiye.”
Keiko, Japan: “Mulungu alibe tsankho ndipo amafunitsitsa kuthandiza makolo onse, kaya akulera okha ana kapena ayi.”—Machitidwe 10:34.
Yesu ananena kuti: “Bwerani kwa ine nonsenu ogwira ntchito yolemetsa ndi olemedwa, ndipo ndidzakutsitsimutsani . . . , chifukwa ndine wofatsa ndi wodzichepetsa, ndipo mudzatsitsimulidwa.” (Mateyu 11:28-30) Popeza kuti Yesu anatengera makhalidwe a Atate wake, mawu amene ananenawa amasonyeza kuti Yehova amatikonda komanso amatidera nkhawa. Kunena zoona, Yesu komanso Atate wake wakumwamba amafuna kuti tiziwadalira. Pa Salimo 34:8 timawerenga kuti:“Talawani ndipo muone kuti Yehova ndi wabwino.” Mulungu amafuna kuti muone nokha kuti malangizo ake ndi othandiza ndipo amatipatsa malangizowo n’cholinga choti zinthu zitiyendere bwino. Kodi inuyo mungakonde kuyamba kutsatira malangizo ake?