Pakadutsa miyezi iwiri ali ndi bere, mphakayu amatha kuswa ana atatu
TAYEREKEZANI kuti ndi usiku ndipo muli kudera lachipululu. Kenako mukuona mphaka wa m’tchire akutuluka kuphanga n’kuima. Mphakayo akuyang’ana uku ndi uku ataimika makutu. Ndiyeno akuyamba kuyenda monyang’ama mu mchenga.
Mwadzidzidzi mphaka uja akudumpha n’kumbwandira mbewa. Zimenezi ndi zimene mphaka wa m’tchire wa kuchipululu amakonda kuchita. Mphakayu amasaka mbewa usiku wonse. Akakhuta amatenga mbewa zotsala n’kuzikwirira mu mchenga. Akatero amabwerera kuphanga kwake mam’mawa kwambiri ndipo saoneka masana onse. Onani zina zokhudza mphaka ameneyu.