Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g 9/13 tsamba 6-9
  • Kodi Halowini Ndi Chiyani?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Halowini Ndi Chiyani?
  • Galamukani!—2013
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Mwambo wa Halowini Unayamba Bwanji?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Zoona Zake za Zikondwerero Zotchuka
    Galamukani!—2001
  • Kodi Zikondwerero Zotchuka Zilibe Vuto Lililonse?
    Galamukani!—2001
  • Chifukwa Chimene Sindikondwerera Halowini
    Galamukani!—2006
Onani Zambiri
Galamukani!—2013
g 9/13 tsamba 6-9
[Chithunzi patsamba 6]

NKHANI YA PACHIKUTO

Kodi Halowini Ndi Chiyani?

Ku United States komanso ku Canada, mwambo wa Halowini ndi wotchuka kwambiri ndipo umachitika chaka chilichonse pa 31 October. Koma zimene zimachitika pa mwambowu zimachitikanso m’madera ena padziko lonse ngakhale kuti umadziwika ndi dzina lina. Pa nthawi ya mwambowu anthu amakhala ndi maholide ndipo amachita zinthu zosonyeza kuti akulankhulana ndi akudziko la mizimu kuphatikizapo mizimu ya anthu akufa, afiti, ziwanda ndi mizukwa.—Onani bokosi lakuti “Zikondwerero Zofanana ndi Mwambo wa Halowini.”

[Chithunzi]

ANTHU ena samakhulupirira mizimu koma amachita nawo mwambo umenewu kuti angopeza mpata wosangalala. Koma ena amaona kuti mwambo umenewu siwabwino pa zifukwa zotsatirazi:

  1. Buku lina linanena kuti “Mwambo wa Halowini umakhudzana kwambiri ndi kulankhulana ndi mizimu imene imaopseza anthu.” (Onani bokosi lakuti “Mmene Halowini Inayambira.”) Zikondwerero zambiri zofanana ndi Halowini zinayamba ndi anthu osalambira Mulungu ndipo zimakhudzana kwambiri ndi kulambira anthu akufa. Masiku anonso, anthu akamachita zikondwerero zimenezi amaganiza kuti akulankhulana ndi mizimu ya akufa.—Encyclopedia of American Folklore.

  2. Ngakhale kuti mwambo wa Halowini umaoneka kuti ndi wa ku America kokha, mayiko ambiri ayamba kuchita mwambo umenewu. Koma anthu ambiri sadziwa mmene mwambowu unayambira. Sadziwanso zimene zizindikiro, zokongoletsera komanso miyambo imene imachitika pa mwambowu zimatanthauza. Ndipo miyambo imene imachitika pa mwambowu imakhudzana ndi za mizimu.—Onani bokosi lakuti “Kodi Zimaimira Chiyani?”

  3. Anthu ambiri okhulupirira za ufiti, omwe amatsatirabe miyambo ya Aselote, amatchulabe mwambo wa Halowini ndi dzina lake loyambirira lakuti Samhain. Iwo amaona kuti tsikuli ndi lapadera kwambiri pachaka chonse. Nyuzipepala ina, yotchedwa USA Today, inalemba zimene munthu wina, yemwe ankati ndi mfiti ananena. Munthuyo anati: “Akhristu sadziwa kuti akamachita nawo zikondwerero zimenezi, amakhala akuthandiza afiti kuchita mwambo umenewu. . . . Zimenezi zimatisangalatsa kwambiri.”

  4. Zikondwerero zimenezi sizigwirizana ndi zimene Baibulo limaphunzitsa. Baibulo limatichenjeza kuti: “Pakati panu pasapezeke munthu . . . wolosera, wochita zamatsenga, woombeza, wanyanga, kapena wolodza ena, aliyense wofunsira kwa wolankhula ndi mizimu, wolosera zam’tsogolo kapena aliyense wofunsira kwa akufa.”—Deuteronomo 18:10, 11; onaninso Levitiko 19:31; Agalatiya 5:19-21.

[Chithunzi patsamba 9]

Mabanja akhoza kumasangalala popanda kuchita nawo miyambo yolakwika

Malinga ndi zimene takambiranazi, tsopano mwadziwa mmene mwambo wa Halowini ndi zikondwerero zina, zofanana ndi mwambowu, zinayambira. Zimenezi zingakuthandizeni kupewa kuchita nawo zikondwerero zimenezi.

“Akhristu sadziwa kuti akamachita nawo zikondwerero zimenezi, amakhala akuthandiza afiti kuchita mwambo umenewu. . . . Zimenezi zimatisangalatsa kwambiri.”—Mawu amenewa analembedwa m’nyuzipepala ina, yotchedwa USA Today, omwe munthu wina, yemwe ankati ndi mfiti ananena

ZIKONDWERERO ZOFANANA NDI MWAMBO WA HALOWINI

Ngakhale kuti mwambo wa Halowini umadziwika kuti umachitika kwambiri ku America, mayiko ambiri ayamba kuchita mwambo umenewu. Palinso miyambo ina yofanana ndi Halowini imene pamachitika zinthu zosonyeza kuti akulankhana ndi mizimu. Mapu ali pambaliwa akusonyeza zina mwa zikondwerero zimenezi.

  • North America - Tsiku la Anthu Akufa

  • South America - Kawsasqanchis

  • Europe - Tsiku la Anthu Akufa komanso miyambo ina yofanana ndi Halowini

  • Africa - Gule wa Egunguns

  • Asia - Mwambo wa Bon

KODI ZIMAIMIRA CHIYANI?

Zimene Miyambo Komanso Zizindikiro za pa Halowini Zimaimira

MIZUKWA KOMANSO AFITI: Zinthu zimenezi zimakhudzana kwambiri ndi mizimu yoipa.

MASWITI: Aselote ankanyengerera mizimu yoipa ndi maswiti. Kenako matchalitchi anayamba kulimbikitsa kuti anthu akamachita mwambo umenewu azipita ku nyumba iliyonse kukapempha zakudya kuti akazigwiritsire ntchito popempherera akufa. M’kupita kwa nthawi anthu anangozolowera kuchita zimenezi pa mwambo wa Halowini.

ZOVALA: Aselote ankavala zophimba kumaso zoopsa kuti mizimu yoipa izipusitsika n’kumawaona ngati nawonso ndi mizimu n’cholinga choti isawavulaze. Pang’ono ndi pang’ono matchalitchi anayamba kutsatira miyambo yachikunja pochita zikondwerero za Tsiku la Anthu Akufa komanso Tsiku la Oyera Mtima. Kenako anthu ankati akamachita zikondwerero zimenezi amayendera nyumba iliyonse atavala zovala zojambula oyera mtima, angelo komanso ziwanda.

MAWUNGU: Pochita zikondwererozi, amaboola mawungu n’kupanga nkhope ngati ya munthu. Kenako amayatsa kendulo n’kuika mkati mwa dzungulo. Ena amakhulupirira kuti kandulo yemwe ali mkati mwa dzungulo akuimira mzimu wa munthu womwe uli ku purigatoriyo.

MMENE HALOWINI INAYAMBIRA

ZAKA ZA M’MA 400 B.C.E.

Aselote ankachita mwambo wa Samhain cha kumapeto kwa October. Iwo ankakhulupirira kuti nthawi imeneyi ndi imene mizukwa komanso mizimu yoipa imayendayenda kwambiri padziko lapansi kuposa nthawi zina.

ZAKA ZA M’MA 100 C.E.

[Chithunzi]

Aroma anagonjetsa Aselote ndipo Aroma anayamba kuchita mwambo wa Samhain.

ZAKA ZA M’MA 600 C.E.

Papa Boniface Wachinayi anayambitsa chikondwerero cha Tsiku la Oyera Mtima kuti azikumbukira anthu onse amene anaphedwa chifukwa cha chikhulupiriro chawo.a

ZAKA ZA M’MA 1000 C.E.

2 November ndi tsiku limene linasankhidwa kuti anthu azikumbukira oyera mtima amene anamwalira.

ZAKA ZA M’MA 1700 C.E.

Holide imene ankachita pokumbukira akufa inayamba kudziwika kuti Halowini.

ZAKA ZA M’MA 1800 C.E.

[Chithunzi]

Anthu ambiri amene anasamuka ku Ireland kupita ku United States ankachitabe miyambo ya Halowini. M’kupita kwa nthawi, miyambo imeneyi inasakanikirana ndi miyambo ya anthu ochokera ku Britain, Germany, Africa komanso ochokera m’madera osiyanasiyana.

ZAKA ZA M’MA 1900

Holide ya Halowini inatchuka kwambiri ndipo inayamba kuchitika m’dziko lonse la United States.

ZAKA ZA M’MA 2000

[Chithunzi]

Makampani a padziko lonse a zamalonda anayamba kupanga ndalama zambiri chifukwa cha mwambo wa Halowini.

a Mawu akuti “Halo” ankatanthauza “oyera.” Tsiku la Oyera Mtima ndi tsiku limene ankakumbukira oyera mtima amene anamwalira. Madzulo a tsiku limeneli ndi amene anayamba kutchedwa kuti Halowini.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena