Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g 1/14 tsamba 2-4
  • Webusaiti Yothandiza Kwambiri

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Webusaiti Yothandiza Kwambiri
  • Galamukani!—2014
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • NDI YOTHANDIZA ANTHU APABANJA
  • NDI YOTHANDIZA KWA MAKOLO
  • NDI YOTHANDIZA ACHINYAMATA
  • NDI YOTHANDIZA KWA ANTHU AMENE AKUFUNA KUPHUNZIRA BAIBULO
  • Zamkatimu
    Galamukani!—2015
  • Mukhoza Kumvetsa Zimene Baibulo Limanena
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Mmene Tingagwiritsire Ntchito Kapepala Kodziwitsa Anthu za Webusaiti Yathu
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2014
  • Zamkatimu
    Galamukani!—2016
Onani Zambiri
Galamukani!—2014
g 1/14 tsamba 2-4
Mtsikana watsegula webusaiti ya jw.org/ny

NKHANI YA PACHIKUTO

Webusaiti Yothandiza Kwambiri

  • WERENGANI Baibulo m’zinenero pafupifupi 50 komanso werengani mabuku othandiza kuphunzira Baibulo m’zinenero zoposa 500.

  • ONERANI mavidiyo a chinenero chamanja m’zinenero pafupifupi 70.

  • SANKHANI chinenero chimene mukufuna pa zinenero zambirimbiri zimene zikupezeka.

  • MVETSERANI masewero a nkhani za m’Baibulo.

  • ONANI zithunzi zofotokoza nkhani za m’Baibulo n’kuwerenga mawu ake.

  • ONERANI masewero komanso mavidiyo a nkhani za m’Baibulo amene angakuthandizeni kuthana ndi mavuto pa moyo wanu.

  • PANGANI DAWUNILODI mabuku, magazini, nkhani komanso zinthu zomvetsera, ndipo zonsezi ndi zaulere.

  • FUFUZANI nkhani zosiyanasiyana pogwiritsa ntchito LAIBULALE YA PA INTANETI ya Watchtower. Mungapeze nkhani zambiri zothandiza zomwe zikupezeka m’zinenero pafupifupi 100.

NDI YOTHANDIZA ANTHU APABANJA

“Ndikufuna kuti banja langa liziyenda bwino. Ine ndi mkazi wanga takhala tisakugwirizana makamaka kuyambira pamene tinayamba kukhala ndi ana. Tikufuna kupeza malangizo amene angatithandize kuti banja lathu liziyenda bwino”

ZIMENE BAIBULO LIMANENA:

“Nzeru zimamanga banja la munthu, ndipo kuzindikira kumachititsa kuti lilimbe kwambiri.”—Miyambo 24:3.

NKHANI ZIMENE MUNGAPEZE PA WEBUSAITIYI

Mwamuna ndi mkazi wake atsegula tsamba la Anthu Apabanja Ndiponso Makolo pa webusaiti ya jw.org/ny

Mbali yakuti “Anthu Apabanja Ndiponso Makolo” ingakuthandizeni pa nkhani ngati izi:

  • Zimene Mungachite Kuti Mukhale Wosangalala M’chaka Choyamba cha Ukwati

  • Zimene Mungachite Kuti Muzigwirizana ndi Apongozi Anu

  • Kulangiza Ana

  • Kodi Mungatani Kuti Musamakangane ndi Mwana Wanu?

  • Kugwiritsa Ntchito Ndalama Mwanzeru

(Pitani pamene palembedwa kuti, ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA > ANTHU APABANJA NDIPONSO MAKOLO)

Buku lakuti Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja lili ndi nkhani zosiyanasiyana zokhudza banja, kuyambira pamene munthu akukonzekera kulowa m’banja ndiponso zokhudza kusamalira makolo okalamba.

(Pitani pamene palembedwa kuti MABUKU > MABUKU)

NDI YOTHANDIZA KWA MAKOLO

“Ana anga ndi ofunika kwambiri kwa ine kuposa chilichonse. Ndimafuna kuti akule bwino kuti asadzandichititse manyazi”

ZIMENE BAIBULO LIMANENA:

“Phunzitsa mwana m’njira yomuyenerera. Ngakhale akadzakalamba sadzapatukamo.”—Miyambo 22:6.

NKHANI ZIMENE MUNGAPEZE PA WEBUSAITIYI

Bambo ndi mwana wake atsegula tsamba la Ana pa webusaiti ya jw.org/ny

Mbali yakuti “Ana” ili ndi zithunzi zofotokoza nkhani za m’Baibulo zimene zikhoza kukuthandizani kuphunzitsa ana anu kuti akhale . . .

  • omvera

  • okoma mtima

  • ogwirizana

  • oyamikira

(Pitani pamene palembedwa kuti ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA > ANA)

Pali buku la mutu wakuti, Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo ndiponso lakuti Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso. Mabukuwa ndi abwino kwambiri kuwerenga limodzi ndi ana anu.

(Pitani pamene palembedwa kuti MABUKU > MABUKU)

NDI YOTHANDIZA ACHINYAMATA

“Ndikufuna nditapeza malangizo othandiza pa nkhani zokhudza sukulu, makolo anga, anzanga komanso atsikana. Si inenso mwana woti ndizingouzidwa zochita”

ZIMENE BAIBULO LIMANENA:

“Sangalala ndi unyamata wako.”—Mlaliki 11:9.

NKHANI ZIMENE MUNGAPEZE PA WEBUSAITIYI

Wachinyamata watsegula tsamba la Achinyamata pa webusaiti ya jw.org/ny

Mbali yakuti “Achinyamata” ili ndi nkhani komanso mavidiyo amene angakuthandizeni ngati . . .

  • mumasowa ocheza nawo

  • mukukumana ndi mavuto kusukulu

  • mwaphwanya malamulo a makolo anu

  • anzanu a kusukulu amakuvutitsani

(Pitani pamene palembedwa kuti ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA > ACHINYAMATA)

Buku lakuti Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Lachiwiri lili ndi mayankho a mafunso ambiri amene achinyamata amakhala nawo.

(Pitani pamene palembedwa kuti MABUKU > MABUKU)

NDI YOTHANDIZA KWA ANTHU AMENE AKUFUNA KUPHUNZIRA BAIBULO

“Ndikufuna nditamvetsa bwino zimene Baibulo limaphunzitsa. Kodi ndingayambire pati?”

ZIMENE BAIBULO LIMANENA:

“Malemba onse anauziridwa ndi Mulungu, ndipo ndi opindulitsa pa kuphunzitsa.”—2 Timoteyo 3:16.

ZIMENE MUNGAPEZE PA WEBUSAITIYI

Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika ndi lolondola komanso ndi losavuta kumva.

(Pitani pamene palembedwa kuti MABUKU > BAIBULO)

Mbali yakuti “Kuyankha Mafunso a M’Baibulo” ili ndi mayankho a mafunso osiyanasiyana.

(Pitani pamene palembedwa kuti ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA > KUYANKHA MAFUNSO A M’BAIBULO)

Mungathe kugwiritsa ntchito mbali yakuti “Pemphani Munthu Woti Aziphunzira Nanu Baibulo Kwaulere” kuti mupemphe munthu wina wa Mboni kuti aziphunzira nanu Baibulo kwaulere.

(Mukafika patsamba loyamba, pitani pamene palembedwa kuti “Pemphani Munthu Woti Aziphunzira Nanu Baibulo Kwaulere”)

“Ndinasiya kuwerenga Baibulo chifukwa sindinkalimvetsa. Koma nditayamba kuliphunzira pogwiritsa ntchito buku lakuti, ‘Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?’ ndinadabwa kuona kuti Baibulo ndi losavuta kumva.”—Christina.

KODI MULI NDI MAFUNSO OKHUDZA MBONI ZA YEHOVA?

Mbali yakuti “Mafunso Ofunsidwa Kawirikawiri” ili ndi mafunso okhudza Mboni za Yehova amene anthu amakonda kufunsa monga akuti, “N’chifukwa chiyani mumalalikira anthu amene ali kale ndi chipembedzo chawo?” ndi “Kodi ndalama zoyendetsera ntchito yanu zimachokera kuti?”

(Pitani pamene palembedwa kuti ZOKHUDZA IFEYO > MAFUNSO OFUNSIDWA KAWIRIKAWIRI)

Tsiku lililonse anthu okwana 700,000 amatsegula webusaiti ya jw.org. Inunso mungathe kuwerenga nkhani zosiyanasiyana pa webusaitiyi.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena