Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g 5/14 tsamba 16
  • ‘Nzeru Ikufuula’ Kodi Inuyo Mukuimva?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • ‘Nzeru Ikufuula’ Kodi Inuyo Mukuimva?
  • Galamukani!—2014
  • Nkhani Yofanana
  • ‘Wodala Munthu Wopeza Nzeru’
    Nsanja ya Olonda—2001
  • Nzeru Yeniyeni Ikufuula
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2022
  • ‘Nzeru za Mulungu N’zozama’
    Yandikirani Yehova
  • Yehova Akugwiritsira Ntchito “Chopusa” Kupulumutsa Okhulupirirawo
    Nsanja ya Olonda—1992
Onani Zambiri
Galamukani!—2014
g 5/14 tsamba 16
A Mboni za Yehova akupatsa mzimayi magazini ofotokoza mfundo za m’Baibulo

‘Nzeru Ikufuula’ Kodi Inuyo Mukuimva?

“Nzerutu ikungokhalira kufuula, ndipo kuzindikira kukungokhalira kutulutsa mawu. Imaima pamwamba pa zitunda, m’mbali mwa njira ndi pamphambano za misewu. Imafuula mokweza . . . polowera kuzipata.”—MIYAMBO 8:1-3.

NZERU ndi yofunika kwambiri. Popanda kuchita zinthu mwanzeru, munthu angamangokhalira kupalamula. Koma kodi nzeru yeniyeni tingaipeze kuti? Munthu amene analemba buku la Miyambo ankaganizira za nzeru zopanda malire za Mlengi wathu. Ndipotu nzeru zimenezi ndi zoti aliyense angathe kuzidziwa, chifukwa zimapezeka m’buku lapadera kwambiri, lomwe ndi Baibulo. Taganizirani mfundo zotsatirazi.

  • Buku lina linanena kuti: “Baibulo ndi buku lomwe lafalitsidwa komanso kumasuliridwa kambirimbiri m’zinenero zambiri kuposa buku lililonse.” (The World Book Encyclopedia) Baibulo lonse kapena mbali yake likupezeka m’zinenero pafupifupi 2,600. Izi zikusonyeza kuti anthu 90 pa 100 alionse angathe kukhala nalo m’chinenero chawo. Pamenepatu tingati nzeru ikufuula.

  • Koma nzeru ‘imafuula mokweza’ m’njira inanso. Lemba la Mateyu 24:14 limati: “Uthenga wabwino uwu wa ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukhale umboni ku mitundu yonse, kenako mapeto [a dziko loipali] adzafika.”

Tingati “uthenga wabwino” umenewo ndi nzeru yeniyeni, chifukwa umatiuza za njira yanzeru imene Mulungu wakonza yodzathetsera mavuto a anthu. Mulungu adzagwiritsa ntchito Ufumu wake kuthetsa mavuto onse a anthu. Ufumu umenewu ndi boma lokhazikitsidwa ndi Mulungu, ndipo lidzalamulira dziko lonse lapansi. Izi zikusonyeza kuti padziko lonse padzakhala boma limodzi lokha. (Danieli 2:44; 7:13, 14) N’chifukwa chake Yesu Khristu anapemphera kuti: “Ufumu wanu ubwere. Chifuniro chanu chichitike, monga kumwamba, chimodzimodzinso pansi pano.”—Mateyu 6:9, 10.

A Mboni za Yehova amalengeza za Ufumu wa Mulunguwu m’mayiko okwana 239, ndipo amaona kuti kugwira nawo ntchito imeneyi ndi mwayi waukulu zedi. Apatu tingatidi nzeru yeniyeni yochokera kwa Mulungu ‘ikufuula mokweza.’ Kodi inuyo mukuimva?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena