Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g 4/15 tsamba 3-5
  • N’chifukwa Chiyani Ana a Masiku Ano Safuna Kuuzidwa Zochita?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • N’chifukwa Chiyani Ana a Masiku Ano Safuna Kuuzidwa Zochita?
  • Galamukani!—2015
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mphamvu za Makolo Zikuchepa
  • Malangizo Olerera Ana Amasinthasintha
  • Makolo Phunzitsani Ana Anu Mwachikondi
    Nsanja ya Olonda—2007
  • Kodi Malangizo Abwino Olerera Ana Mungawapeze Kuti?
    Galamukani!—2015
  • Mmene Mungalerere Ana Anu Kuti Asakhale Odzikonda
    Galamukani!—2013
  • Makolo, Muzithandiza Ana Anu Kuti Azikonda Yehova
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2022
Onani Zambiri
Galamukani!—2015
g 4/15 tsamba 3-5
1. Kamnyamata kazaka 4 kanyamula kagalimoto koseweretsa, 2. Kamtsikana kazaka 5 kapinda manja, 3. Mnyamata wa zaka 12 wagwira m’chiuno

NKHANI YA PACHIKUTO

N’chifukwa Chiyani Ana a Masiku Ano Safuna Kuuzidwa Zochita?

Masiku ano, mabanja ambiri asintha mmene amalerera ana, makamaka ku Europe. Poyamba makolo ndi amene ankauza ana zochita ndipo anawo ankatsatira malamulo awo. Koma masiku ano, m’mabanja ambiri ana ndi amene akumauza makolo zochita. Taonani zitsanzo zotsatirazi.

  • Mayi ena ali mu shopu ndi mwana wawo wamwamuna wazaka 4. Mwanayo akutenga kagalimoto koseweretsa n’cholinga choti mayi akewo am’gulire. Koma mayiwo akumuletsa n’kumuuza kuti: “Ayi, uli kale ndi zoseweretsa zambiri.” Mayiwo asanamalize n’komwe kulankhula, mwanayo akuyamba kulira akunena kuti, “Nono, ine ndikuifunabe.” Poopa kuti mwanayo apitiriza kulira komanso kuvutitsa, mayiwo akungomugulira kagalimoto komwe akufunako.

  • Bambo ena akulankhula ndi munthu wina, mwana wawo wamkazi wazaka 5 akuyamba kusonyeza kuti zikumunyansa ndipo akuti: “Ndatopa ine, tiyeni tizipita kunyumba.” Bambowo akusiya kaye kulankhula ndi munthuyo n’kunyonyomala ndipo akuuza mwana wawoyo momunyengerera kuti: “Ungotidikira pang’ono wamva, tipita posachedwapa.”

  • Mnyamata wina wazaka 12, dzina lake James, amakonda kuchitira mwano aphunzitsi ake ndipo bambo ake amadziwa zimenezi. Tsiku lina bambowa amva kuti mwana wawo wakangananso ndi aphunzitsi ake, ndipo akukwiya kwambiri. Sikuti akukwiya chifukwa cha khalidwe la mwana wawoyo. Koma akukwiyira aphunzitsiwo ndipo akuuza James kuti: “Aphunzitsi amenewa amakupezerera kwambiri. Ndikawanenera kwa akuluakulu a sukulu yanu.”

Ngakhale kuti izi ndi zitsanzo chabe, zoterezi zikuchitika m’mabanja ambiri. Makolo ambiri amalekerera ana awo akamachita mwano, amawapangira chilichonse chimene akufuna komanso amawaikira kumbuyo akachita zoipa. Buku lina linanena kuti: “Makolo ambiri asiya udindo wawo ndipo akumangolamuliridwa ndi ana. Poyamba ana ankadziwa kuti makolo ndi amene amafunika kuwauza zochita, osati iwowo kuuza makolo zochita.”—The Narcissism Epidemic.

Komabe pali makolo ena amene amayesetsa kuphunzitsa ana awo makhalidwe abwino. Amachita zimenezi powapatsa chitsanzo chabwino komanso kuwalangiza akalakwitsa. Koma buku lija linanena kuti makolo amene amachita zimenezi, amaonedwa ngati “akuchita zosemphana ndi chikhalidwe.”

Kodi chachititsa n’chiyani kuti zinthu zisinthe chonchi? N’chifukwa chiyani masiku ano ana ambiri sakufuna kuuzidwa zochita?

Mphamvu za Makolo Zikuchepa

Anthu ena amati mphamvu za makolo zinayamba kuchepa kuyambira m’zaka za m’ma 1960. Pa nthawiyi anthu ena omwe ankaonedwa ngati akatswiri opereka malangizo olerera ana, anayamba kulimbikitsa makolo kuti azipereka ufulu wambiri kwa ana. Ankauza makolo kuti: “Muzikhala mnzawo osati bwana wawo. Muzikonda kunena mawu owachemerera m’malo mowadzudzula. Akachita zoipa muzingozinyalanyaza, koma akachita zabwino muziwayamikira.” Apa akatswiriwa sankathandiza makolo kudziwa kufunika koyamikira ana akachita zabwino ndi kuwadzudzula akalakwitsa zinazake. Koma ankangolimbikitsa makolo kuti azipewa kulanga kapena kudzudzula ana awo chifukwa anawo angakhumudwe ndipo akadzakula sazidzakonda makolo awowo.

Kenako akatswiriwa anayamba kuuza makolo kuti azichita zinthu zomwe zingathandize kuti ana awo azidziona kuti ndi ofunika kwambiri. Ankaganiza kuti apa atulukira chinsinsi cha njira yabwino yolerera ana. N’zoona kuti sikulakwa kuthandiza ana kuti azidziona kuti ndi ofunika. Koma zimene akatswiriwa ankauza makolo sizinali zabwino. Ankawauza kuti: ‘Muzipewa kuuza mwana wanu mawu akuti, “ayi” ndi akuti “wachita zoipa.” Muzimuuza kuti ndi wofunika kwambiri kuposa aliyense ndipo angathe kuchita chilichonse chomwe akufuna.’ Apa akatswiriwa ankangolimbikitsa kuti ana azidziona kuti ndi ofunika kwambiri. Anaiwala kuti chofunika n’kuwathandiza kuti azidziwa zoyenera kuchita kuti akhaledi anthu abwino.

Mwana wakhala pampando ngati mfumu ndipo makolo ake agwada posonyeza kumugonjera

Kulera ana m’njira yoti azidziona kuti ndi ofunika kwambiri, kumapangitsa kuti asamafune kuuzidwa zochita

Koma anthu ena ayamba kuona kuti zimene akatswiri ankachitazi zabweretsa mavuto. Zapangitsa kuti ana asamafune kuuzidwa zochita koma aziona ngati iwowo ndiye ayenera kuuza ena zochita. Buku lina linanena kuti izi zimapangitsa kuti “anawo akadzakula, azidzakhumudwa kwambiri akalephera kuchita zinazake kapena akadzudzulidwa ndi anthu ena.” (Generation Me) Bambo wina ananena m’bukuli kuti: “Kuntchito anthu sangataye nthawi n’kumakuchitirani zinthu zoti muzidziona kuti ndinu wofunika kwambiri ngati zomwe makolo anu ankachita. . . . Mwachitsanzo, ngati mwapereka lipoti la ntchito yanu ndipo likusonyeza kuti ntchito sikuyenda bwino, abwana anu akhoza kukukalipirani. Iwo sangakuyamikireni n’cholinga chongofuna kukusangalatsani monga kunena kuti, ‘Pepala limene mwalembapo lipotili ndi lokongola bwanji!’ Choncho kulera mwana m’njira yoti azidziona ngati ndi wofunika kwambiri kuposa aliyense, n’kumuwononga chifukwa akadzakula adzavutika.”

Malangizo Olerera Ana Amasinthasintha

Malangizo olerera ana omwe akatswiri amapereka, amasinthasintha. Izi zimachititsa kuti makolo azisinthasinthanso mmene amalerera ana. Zimene amachitazi n’zofanana ndi zomwe Baibulo limanena kuti anthu ena ‘amatengekatengeka ngati akukankhidwa ndi mafunde, n’kupita uku ndi uku ndi mphepo iliyonse ya chiphunzitso.’ (Aefeso 4:14) Katswiri wina dzina lake Ronald G.Morrish, anati kusinthasintha kwa malangizo olerera ana “kukuchititsa kuti zinthu m’dzikoli zizisinthanso.”a

Apatu n’zoonekeratu kuti malangizo a akatswiri, oti makolo azipereka ufulu wambiri kwa ana, abweretsa mavuto ambiri. N’chimodzimodzinso ndi malangizo akuti, makolo azichititsa ana awo kudziona kuti ndi ofunika kwambiri. Izi zapangitsa kuti makolo asakhalenso ndi mphamvu zouza ana zochita. Zachititsanso kuti ana akakula asamathe kusankha bwino zochita ndiponso kuti azilephera kuchita zinthu ngati munthu wamkulu.

Ndiye kodi makolo angapeze kuti malangizo abwino olerera ana?

a Zachokera m’buku lakuti, Secrets of Discipline: 12 Keys for Raising Responsible Children.

Kodi Mukuwaphunzitsa Zabwino Kapena Zoipa?

  • Tiyerekeze kuti muli ndi ana awiri. Ana anuwo akaweruka kusukulu komanso kumapeto kwa mlungu, mumapita nawo kumalo osiyanasiyana kuti akasangalale. Nthawi zina mumaona kuti mwatopa kwambiri. Komabe mumaganiza kuti, ‘Ana anga amadziwa kuti ndimawakonda kwambiri ndipo ndiyenera kuwachitira chilichonse. Zimenezi n’zimene mayi aliyense wabwino ayenera kuchita.’

    Taganizirani izi: Kodi ana anu akuphunzira chiyani akamaona kuti inuyo ngakhale mutope bwanji mumawachitira zinthu zoti asangalale? Kodi zimenezi sizingachititse anawo kuganiza kuti nthawi zonse anthu akuluakulu, makamaka makolo awo, amafunika kuwachitira iwowo zinthu?

    Zimene mungachite: Thandizani ana anu kudziwa kuti nanunso mumafunika nthawi yoti mupange zanu. Zimenezi zingawathandize kuti aphunzire kuganizira ena, kuphatikizapo inuyo.

  • Tiyerekeze kuti ndinu bambo ndipo muli ndi ana awiri aamuna. Munaleredwa ndi bambo wankhanza ndi waukali. Simukufuna kuti mulere ana anu ngati mmene bambo anu anakulererani. Mumayamikira ana anu ngakhale pa nthawi yomwe sanachite zinthu zoyenera kuwayamikira. Mumaganiza kuti: ‘Ndikamawayamikira zithandiza kuti azidziona kuti ndi ofunika komanso kuti angakwanitse kuchita zambiri pa moyo wawo.’

    Taganizirani izi: Kodi mukamayamikira ana anu n’cholinga chongofuna kuwasangalatsa, mukuwaphunzitsa chiyani? Ngati nthawi zonse mumachita zinthu zoti ana anuwo azidziona kuti ndi ofunika kwambiri, kodi zingawabweretsere mavuto otani panopa komanso akadzakula?

    Zimene mungachite: Musamangokhalira kukalipira ana anu, koma si bwinonso kumangowayamikira chilichonse n’cholinga chongofuna kuwasangalatsa.

  • Tiyerekezenso kuti ndinu mayi wa ana aakazi awiri, wazaka 6 ndi wazaka 5. Wamkuluyo sachedwa kupsa mtima ndipo amachita zinthu mopupuluma. Dzulo anamenya mng’ono wakeyo, ndipo atachita zimenezi, munaona kuti njira yabwino ndi kukambirana naye m’malo momudzudzula. Munaona kuti akhoza kukhumudwa mukamuuza kuti wachita zoipa.

    Taganizirani izi: Kodi mukuganiza kuti kungokambirana ndi mwana wazaka 6 kungamuthandize kudziwa kuti walakwa? Kodi n’zoona kuti si bwino kumuuza kuti walakwa kumenya mng’ono wake?

    Zimene mungachite: Muuzeni mwana wanuyo chilango chomwe mungam’patse akachita zolakwika. Chilango choyenera chingathandize mwanayo kusintha khalidwe loipa.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena