Mawu Oyamba
Masiku ano, anthu ambiri amakhala otanganidwa moti mpaka nthawi zina sacheza ndi anzawo ngakhalenso anthu a m’banja lawo.
Ndiye kodi tingatani kuti tizigwiritsa ntchito bwino nthawi yathu?
Munthu wina wanzeru analemba kuti: “Kupuma pang’ono kuli bwino kuposa kugwira ntchito mwakhama ndi kuthamangitsa mphepo.”—Mlaliki 4:6.
Galamukani! iyi ikufotokoza mfundo zimene zingatithandize kuti tizigwiritsa ntchito nthawi mwanzeru komanso kuika zinthu zofunika pamalo oyamba.