Mawu Oyamba
N’chifukwa chiyani tiyenera kukonzekera ngozi zadzidzidzi?
Baibulo limati: “Wochenjera amene waona tsoka amabisala. Koma anthu osadziwa zinthu amene amangopitabe amalangidwa.”—Miyambo 27:12.
Magaziniyi ikufotokoza zomwe tingachite ngozi yadzidzidzi isanachitike, ikamachitika komanso pambuyo poti yachitika.