Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g19 No. 2 tsamba 12-13
  • Ana Amafunika Munthu Woti Aziwalangiza

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ana Amafunika Munthu Woti Aziwalangiza
  • Galamukani!—2019
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • ZINTHU ZINANSO ZOFUNIKA POLANGIZA ANA
  • N’CHIFUKWA CHIYANI MALANGIZO A ACHIKULIRE ALI OFUNIKA?
  • MUNGATHANDIZE BWANJI ANA ANU KUTI AZIMVERA MALANGIZO?
  • Mmene Mungalangizire Ana Anu
    Mfundo Zothandiza Mabanja
  • Kuthandiza Achinyamata Kuti Akule Bwino
    Galamukani!—2011
  • Malangizo Odalirika Olerera Ana
    Nsanja ya Olonda—2006
  • Zakumapeto
    Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Loyamba
Onani Zambiri
Galamukani!—2019
g19 No. 2 tsamba 12-13
Mzimayi akuonetsa mtsikana zithunzi zake zakale

PHUNZIRO 5

Ana Amafunika Munthu Woti Aziwalangiza

ZINTHU ZINANSO ZOFUNIKA POLANGIZA ANA

Ana amafunika kulangizidwa ndi anthu achikulire. Monga makolo muyenera kuzindikira kuti muli ndi udindo wolangiza ana anu. Komabe pali anthu enanso achikulire omwe angakuthandizeni kulangiza anawo.

N’CHIFUKWA CHIYANI MALANGIZO A ACHIKULIRE ALI OFUNIKA?

M’mayiko ambiri ana sakhala ndi nthawi yokwanira yocheza ndi achikulire. Mwachitsanzo taganizirani izi:

  • Pafupifupi tsiku lonse ana amakhala ali kusukulu. Kusukuluko, anawo ndi amene amakhala ambiri kuposa aphunzitsi ndi anthu ena aakulu.

  • Akaweruka ambiri amabwerera kunyumba n’kukapeza kuti makolo onse adakali kuntchito.

  • Kafukufuku wina anasonyeza kuti ku United States kokha, ana a zaka zapakati pa 8 ndi 12 amatha maola 6 akuonera TV kapena kusewera magemu apakompyuta.a

Buku lina linati: “Ana ambiri masiku ano, m’malo mofunsira malangizo kwa amayi, abambo, aphunzitsi kapena anthu ena achikulire, . . . amakafunsa ana anzawo.”​—Hold On to Your Kids.

MUNGATHANDIZE BWANJI ANA ANU KUTI AZIMVERA MALANGIZO?

Muzicheza nawo.

MFUNDO YA M’BAIBULO: “Phunzitsa mwana m’njira yomuyenerera. Ngakhale akadzakalamba sadzapatukamo.”​—Miyambo 22:6.

Mwachibadwa ana amafuna kuti makolo awo aziwapatsa malangizo komanso kuwathandiza. Moti akatswiri ena amanena kuti ana a zaka 13 mpaka 19, amaonabe kuti malangizo a makolo awo ndi abwino poyerekeza ndi amene anzawo angawapatse. Dr. Laurence Steinberg analemba m’buku lina kuti: “Ana amaonabe kuti malangizo a makolo awo ndi ofunika ngakhale pamene afika potha msinkhu. Iwo amafuna kumva maganizo a makolo awo ngakhale kuti nthawi zambiri sangagwirizane ndi zimene makolowo akunena.”​—You and Your Adolescent.

Choncho popeza mwachibadwa ana amafuna kumva maganizo a makolo awo, mungachite bwino kumawapatsa malangizo pamsinkhu umenewu. Muzipeza nthawi yocheza nawo n’kumawauza mmene mumamvera, zinthu zimene mumaziona kuti n’zofunika kutsatira komanso zimene mwaphunzira pamoyo wanu.

Apezereni munthu wodalirika kuti aziwathandiza.

MFUNDO YA M’BAIBULO: “Munthu woyenda ndi anthu anzeru adzakhala wanzeru.”​—Miyambo 13:20.

Kodi pali munthu wina wodalirika amene mukuona kuti angakhale chitsanzo chabwino kwa mwana wanu? Mungamupemphe kuti azicheza ndi mwana wanuyo. Koma simuyenera kumusiyira udindo woti akhale ngati kholo lake. Malangizo a munthu wachikulire amene mwamudalira, angakhale ofunika pamene mukuphunzitsa mwana wanuyo. M’Baibulo muli chitsanzo cha Timoteyo, yemwe ngakhale atakula anapitirizabe kupindula ndi malangizo amene Paulo ankamupatsa. Ndipo nayenso Paulo anapindula kwambiri chifukwa chochita zinthu limodzi ndi Timoteyo.​—Afilipi 2:20, 22.

Masiku ano, mabanja ambiri amakhala kutali ndi achibale awo. Izi zimachititsa kuti ana asazolowerane ndi agogo, amalume, azakhali ndi achibale awo ena. Ngati umu ndi mmenenso zilili ndi inuyo, mungachite bwino kupeza munthu wachikulire wodalirika amene ali ndi makhalidwe amene mumafuna kuti ana anu aphunzire.

a Kafukufukuyu anasonyezanso kuti ana a zaka zapakati pa 13 ndi 19, amatha maola pafupifupi 9 tsiku lililonse akuonera TV komanso kusewera magemu apakompyuta. Nthawiyi siikuphatikizapo nthawi imene amagwiritsa ntchito intaneti pofufuza zinthu kusukulu kapena akamalemba homuweki.

Mzimayi akuonetsa mtsikana zithunzi zake zakale

YAMBANI PANOPO KUWAPHUNZITSA

Mwana amene amadalira achikulire kuti azimupatsa malangizo, amakhala wanzeru komanso amayamba kuchita zinthu ngati munthu wamkulu

Muziwapatsa Chitsanzo Chabwino

  • Kodi ndimapereka chitsanzo chabwino kwa ana anga?

  • Kodi ana anga amadziwa kuti nanenso ndimafunika kulangizidwa ndi anthu ena odziwa zambiri?

  • Kodi ndimasonyeza kuti ana anga ndi ofunika kwambiri moti ndimapeza nthawi yocheza nawo?

Zimene Makolo Ena Ananena . . .

“Nthawi zina mwana wanga amandipempha kuti tikambirane zinthu zina nditatanganidwa. Ndimaona kuti mwana wangayo ndi wofunika kwambiri moti ndimasiya kaye zomwe ndikuchitazo kapena ndimamupempha kuti andidikire pang’ono kuti ndimumvetsere bwinobwino. Komanso ine ndi mkazi wanga timayesetsa kutsatira zimene timamuphunzitsa kuti aziona kuti nafenso timayendera mfundo zomwezo.”—David.

“Mwana wathu atangobadwa, ine ndi mwamuna wanga tinakambirana zoti ineyo ndisiye ntchito kuti ndizimusamalira. Sindinong’oneza bondo ndi zimene tinasankhazi. Ndimaona kuti n’zofunika kwambiri kuchita zonse zimene ndingathe posamalira mwana wathu kuti akule bwino. Komanso mwana wanga amadziwa kuti ndimamuona kukhala wofunika kwambiri chifukwa ndimakhala naye nthawi zonse.”​—Lisa.

AZICHEZA NDI ACHIKULIRE

“Ana anga akula akucheza ndi anthu achikulire a misinkhu komanso zokonda zosiyanasiyana. Zimenezi zawathandiza kuti aphunzire zambiri poona zimene anthuwa anakumana nazo. Mwachitsanzo, anadabwa kwambiri agogo anga atawauza kuti ali mtsikana, banja lawo ndi limene linali loyambirira kukhala ndi nyumba yamagetsi. Anawauza kuti pa nthawiyo, anthu a nyumba zapafupi ankabwera kudzangoonerera akuyatsa komanso kuzimitsa magetsi. Nkhaniyi inathandiza ana anga kudziwa kuti kalelo moyo unali wosiyana kwambiri ndi masiku ano. Zimenezi zinawathandiza kuti azilemekeza agogowo komanso anthu ena achikulire. Ana akamakonda kucheza ndi anthu achikulire, m’malo momangokhalira kucheza ndi ana anzawo, amaphunzira zambiri.”​—Maranda.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena