Buku Lakale Lokhala ndi Mfundo Zothandiza Masiku Ano
Anthu ambiri amaona kuti Baibulo ndi buku lofunika kwambiri pa nkhani zachipembedzo. Komabe, si kuti ndi lothandiza pa nkhani zachipembedzo zokha. Lilinso ndi malangizo othandiza pa mbali zonse za moyo wathu.
Mwachitsanzo, taonani zimene ena ananena pa nkhani ya mmene kuphunzira ndi kugwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo kwawathandizira kuti akhale ndi moyo wabwino.
“Ndimaona kuti ndili ndi mtendere wamumtima. Sindivutika kwambiri ndi nkhawa moti ndimakhala wosangalala.”—Fiona.
“Kuphunzira Baibulo kwandithandiza kudziwa chifukwa chake ndili ndi moyo.”—Gnitko.
“Panopo ndili ndi moyo wabwino kwambiri. Ndimapeza nthawi yocheza ndi banja langa ndipo sindikhalanso ndi moyo wongodzipanikiza ndi ntchito.”—Andrew.
Palinso anthu ambiri padziko lonse omwe amavomereza kuti mfundo za m’Baibulo zimawathandiza pamoyo wawo.
Tsopano tiyeni tione mmene Baibulo lingatithandizire . . .
Kukhala ndi moyo wathanzi
Kukhala ndi mtendere wa m’maganizo
Kukhala ndi banja komanso mabwenzi abwino
Kugwiritsa ntchito bwino ndalama
Kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu
Magaziniyi ikuthandizani kuona kuti Baibulo si buku lothandiza pa nkhani zachipembedzo zokha, koma lingakuthandizeninso pamoyo wanu.