Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g20 No. 1 tsamba 3
  • Kodi Mumavutika Kwambiri ndi Nkhawa?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mumavutika Kwambiri ndi Nkhawa?
  • Galamukani!—2020
  • Nkhani Yofanana
  • Kupanikizika Maganizo Kwabwino ndi Koipa
    Galamukani!—1998
  • Zimene Tingachite Kuti Tisamapanikizike Kwambiri
    Galamukani!—2010
  • Kodi Ndingatani Ngati Ndimapanikizika Kwambiri Kusukulu?
    Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Loyamba
  • Zimene Zimachititsa Moyo Kukhala Wopanikizika ndi Zotsatirapo Zake
    Galamukani!—2005
Onani Zambiri
Galamukani!—2020
g20 No. 1 tsamba 3
Mayi wina ali kuntchito koma ali ndi nkhawa ndipo akuoneka wokhumudwa kwambiri.

MUNGATANI KUTI MUCHEPETSE NKHAWA?

Kodi Mumavutika Kwambiri ndi Nkhawa?

“Ndimadziwa kuti aliyense amakhala ndi nkhawa, koma zanga ndiye zawonjeza. Munthune mavuto andichulukira. Mwachitsanzo, nthawi zonse ndimafunika kusamalira mwamuna wanga yemwe sangakwanitse kuchita chilichonse payekha komanso ali ndi vuto la muubongo.”—Jill.a

“Mkazi wanga anandithawa, ndipo ndinkafunika kulera ndekha ana athu awiri. Kuchita zimenezi sikunali kophweka. Kuwonjezera pamenepo, ndinachotsedwa ntchito moti ndinalibe ndalama zokwanira zoti n’kukonzetsera galimoto yanga. Sindinkadziwa choti ndichite moti ndinkada nkhawa kwambiri. Pa nthawiyi ndinaganiza zoti ndingodzipha. Ndinkadziwa kuti kuchita zimenezi n’kulakwa choncho ndinapempha Mulungu kuti andithandize kuthana ndi mavuto angawa.”​—Barry.

Kodi nthawi zina nanunso mumakhala ndi nkhawa ngati mmene zinalili ndi Jill komanso Barry? Ngati ndi choncho, nkhani zotsatirazi zikuthandizani. Nkhanizi zikufotokoza zimene zimachititsa kuti anthu azikhala ndi nkhawa, mmene nkhawa zimakhudzira thanzi lathu komanso zimene tingachite kuti tisamakhale ndi nkhawa kwambiri.

a Mayina asinthidwa.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena