Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g20 No. 1 tsamba 5-7
  • Zimene Zimachitika Munthu Akakhala ndi Nkhawa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zimene Zimachitika Munthu Akakhala ndi Nkhawa
  • Galamukani!—2020
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • MANTHA ABWINO NDI OIPA
  • Kupanikizika Kumayambitsa Mavuto Aakulu
    Galamukani!—2010
  • Kupanikizika Maganizo Kwabwino ndi Koipa
    Galamukani!—1998
  • Zimene Zimachititsa Moyo Kukhala Wopanikizika ndi Zotsatirapo Zake
    Galamukani!—2005
  • Zimene Tingachite Kuti Tisamapanikizike Kwambiri
    Galamukani!—2010
Onani Zambiri
Galamukani!—2020
g20 No. 1 tsamba 5-7
Bambo akuthamanga pamasitepe popita ku ofesi.

MUNGATANI KUTI MUCHEPETSE NKHAWA?

Zimene Zimachitika Munthu Akakhala ndi Nkhawa

Munthu akapanikizika kapena akakhala ndi mantha, ubongo umachititsa kuti thupi litulutse mahomoni osiyanasiyana. Zimenezi zimachititsa kuti mtima uyambe kugunda kwambiri, magazi ayambe kuthamanga, kapumidwe kasinthe komanso kuti minofu ikungike. Izi zikamachitika, thupi limakhala litakonzekera kuchita chilichonse. Manthawo akachepa, thupi limayambanso kubwerera m’chimake.

MANTHA ABWINO NDI OIPA

Tonsefe mwachibadwa timachita mantha ndipo zimenezi zimatithandiza kuti tikonzekere kulimbana ndi zina zake. Mantha amayambira muubongo. Mantha abwino amatithandiza kuti tichite zinthu mwamsanga. Angatithandizenso kukwaniritsa zolinga zathu komanso kuchita bwino zinazake, monga kukhoza mayeso, intavyu kapena kuchita bwino masewera ena ake.

Komabe kukhala ndi mantha komanso wopanikizika kwa nthawi yaitali n’koopsa. Thupi likamangokhala lokonzeka kulimbana ndi mavuto nthawi zonse, munthu akhoza kumakhala wotopa, wokhumudwa komanso akhoza kusokonekera maganizo. Akhozanso kusintha khalidwe komanso mmene amachitira zinthu ndi ena. Kukhala wopanikizika kungachititsenso kuti munthu ayambe kumwa mowa mwauchidakwa, kusuta fodya, kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo komanso kuchita zinthu zina zoipa. Kupanikizika kukhozanso kupangitsa munthu kudwala matenda a maganizo, kutopa kwambiri komanso kufuna kudzipha.

Kukhala wopanikizika komanso wamantha kwa nthawi yaitali, kungayambitse nkhawa ndipo kungakhudze mmene thupi lanu limagwirira ntchito.

MMENE NKHAWA INGAKHUDZIRE THANZI LANU

Ubongo.

Bambo akuthamanga pamasitepe popita ku ofesi.

Ubongo umachititsa kuti thupi lanu lizitulutsa mahomoni osiyanasiyana. Ena mwa mahomoniwa amapangitsa kuti mtima uzigunda kwambiri, magazi azithamanga komanso kuti shuga wa m’thupi achuluke m’magazi. Zinthu zimenezi ndi zomwe zimachititsa kuti thupi likhale lokonzeka kulimbana ndi vuto limene likubwera. Choncho nkhawa kapena kupanikizika kwambiri kungachititse kuti munthu

  • azinyong’onyeka, azida nkhawa, adwale matenda a maganizo, azimva kupweteka kwa mutu komanso azivutika kugona

Minofu ndi Mafupa.

Minofu yanu imakungika kuti ikutetezeni kuti musavulale. Choncho nkhawa kapena kupanikizika kwambiri kungachititse kuti munthu

  • azimva kuphwanya kwa thupi, kupweteka kwa mutu komanso kunjenjemera

Mapapo.

Mungamapume mofulumira kwambiri kuti mulowetse mpweya wokwanira m’mapapo anu. Choncho nkhawa kapena kupanikizika kwambiri kungachititse kuti munthu

  • azichita phuma komanso kubanika

Mtima.

Mtima wanu umagunda mwamphamvu komanso mofulumira kuti utumize magazi kumbali zonse zathupi lanu. Mitsempha imakula kapena kuchepa kuti ithe kutumiza magazi m’malo omwe akufunikira kwambiri monga m’minofu. Choncho nkhawa kapena kupanikizika kwambiri kungachititse kuti munthu

  • adwale matenda othamanga magazi, mtima komanso matenda ofa ziwalo

Mahomoni.

Mahomoni amachititsa thupi kuti likonzekere kuchita zinazake. Pa nthawiyi kapamba amachititsa kuti m’magazi anu mukhale shuga wambiri kuti thupi lanu likhale ndi mphamvu. Choncho nkhawa kapena kupanikizika kwambiri kungachititse kuti munthu

  • adwale matenda a shuga, chitetezo cha thupi lake chichepe zomwe zimachititsa kuti azidwaladwala, asamakhazikike maganizo komanso kuti anenepe kwambiri

M’mimba

Kagayidwe ka chakudya kamasokonekera. Choncho nkhawa kapena kupanikizika kwambiri kungachititse kuti munthu

  • azichita mseru, azisanza, azitsegula m’mimba komanso azilephera kuchita chimbudzi

Ziwalo Zoberekera

Nkhawa ingachititse kuti munthu asamakhale ndi chilakolako chofuna kugonana. Choncho nkhawa kapena kupanikizika kwambiri kungachititse kuti

  • mwamuna azilephera kulowa kuchipinda komanso kuti mkazi azisamba mosakhazikika

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena