Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g20 No. 3 tsamba 6-7
  • Muzimvera Ena Chisoni

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Muzimvera Ena Chisoni
  • Galamukani!—2020
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Vuto Lomwe Limakhalapo
  • Mfundo ya M’Baibulo
  • Kodi Kumvera Ena Chisoni N’kothandiza Bwanji?
  • Zimene Mungachite
  • Chisoni Chimalimbikitsa Munthu Kukhala Wokoma Mtima ndi Wachifundo
    Nsanja ya Olonda—2002
  • Muzisonyeza Kuti Mumawaganizira
    Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2021
  • Kodi Mulungu Amadziwa Mmene Mumamvera?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)——2018
  • Banja Labwino Komanso Mabwenzi Abwino
    Galamukani!—2019
Onani Zambiri
Galamukani!—2020
g20 No. 3 tsamba 6-7
Munthu wamtundu wa Caucasia komanso wa Chisiki akhala moyandikana mundege ndipo akucheza mosangalala.

Muzimvera Ena Chisoni

Vuto Lomwe Limakhalapo

Tikamaganizira kwambiri zimene anthu ena amasiyana ndi ifeyo, tikhoza kuyamba kuona kusiyana kumeneko ngati zolakwa za anthuwo. Zimenezitu zingachititse kuti anthu amene timasiyana nawo tiziwaona kuti ndi otsika. Ndiye tikangoyamba kuona ena moteremu, zimakhala zovuta kuti tiziwamvera chisoni. Kulephera kumvera ena chisoni ndi chizindikiro chakuti ndife atsankho, lomwe ndi vuto lalikulu kwambiri.

Mfundo ya M’Baibulo

“Sangalalani ndi anthu amene akusangalala. Lirani ndi anthu amene akulira.”​—AROMA 12:15.

Kodi lembali likutiphunzitsa chiyani? Mfundo imeneyi tingainene mwachidule kuti muzimvera ena chisoni. Munthu amene amamvera ena chisoni amatha kudziyerekezera ali munthu winayo n’kumamva zimene mnzakeyo akumva.

Kodi Kumvera Ena Chisoni N’kothandiza Bwanji?

Tikamamvera chisoni munthu, timazindikira kuti palibe kusiyana pakati pa ifeyo ndi iyeyo. Timazindikiranso kuti nayenso amakhudzidwa ndi zinthu mofanana ndi mmene ifenso timakhudzidwira ndipo zimene angachite, ndi zimene ifenso tingachite. Kumvera ena chisoni kumatithandiza kudziwa kuti anthu onse, kaya moyo wawo ndi wotani, ndi ofanana. Tikamaganizira kwambiri mmene anthu ena alili ofanana ndi ifeyo, tidzasiya kuwaganizira zolakwika.

Kumvera ena chisoni kudzatithandizanso kuti tiziwalemekeza. Anne-Marie, yemwe amakhala ku Senegal, ankaona kuti anthu osauka ndi otsika. Iye anafotokoza kuti kumvera ena chisoni n’kumene kunamuthandiza. Anati: “Nditaona mmene anthu ochokera m’mabanja osauka amavutikira, ndinadzifunsa kuti ndikanakhala ineyo ndikanamva bwanji? Zimenezi zinandichititsa kuona kuti si ine wapamwamba kuposa anthu amenewo. Ndipotu palibe chilichonse chimene ndinachita kuti ndizikhala moyo wabwino kuposa iwowo.” Mfundo ndi yakuti, tikamayesetsa kumvetsa zimene wina akulimbana nazo, zimatithandiza kuti tizimumvera chisoni osati kumuimba mlandu.

Zimene Mungachite

Ngati mumaganiza zolakwika za anthu a mtundu winawake, tayesani kuona zimene mumafanana ndi anthu amenewo. Mwachitsanzo, taganizirani kuti amamva bwanji

Kumvera ena chisoni kumatithandiza kudziwa kuti anthu onse ndi ofanana

  • akamadya limodzi ndi banja lawo

  • akatopa ndi ntchito ya tsiku limenelo

  • akamacheza ndi anzawo

  • akamamvetsera nyimbo zimene amazikonda

Kenako yerekezerani muli inuyo. Dzifunseni kuti:

  • ‘Kodi ndikanatani munthu wina akanandichititsa kudzimva kuti ndine wachabechabe?’

  • ‘Kodi ndikanamva bwanji anthu ena akanati azindinena asanandidziwe n’komwe?’

  • ‘Ndikanakhala kuti ndine wa mtundu umenewu, kodi ndikanakonda kuti anthu ena azichita nane zinthu motani?’

Munthu wamtundu wa Caucasia komanso wa Chisiki uja akuonetsana zithunzi zosonyeza zinthu zimene amafanana monga banja, masewera omwe amakonda komanso ntchito.

Zimene Zinachitikadi: Robert (Singapore)

“Kale ndinkaganiza kuti anthu amene ali ndi vuto la kumva ndi ovuta kuwamvetsa, opanda nzeru komanso osachedwa kukhumudwa. Choncho ndinkawapewa. Komabe sindinkaona kuti ndili ndi maganizo atsankho chifukwa ndinkaona kuti palibe amene ndikumulakwira.

“Kumvera chisoni anthu amene ali ndi vuto la kumva kunandithandiza kuthana ndi maganizo atsankho amene ndinali nawo. Mwachitsanzo, ndinkaganiza kuti anthu a vutoli alibe nzeru chifukwa chakuti ndinkati ndikawalankhula ankangondiyang’anitsitsa. Ndiyeno ndinayesa kuganizira mmene ndingamvere ngati munthu wina atamandilankhula koma ine osamva. Ndinaona kuti nanenso ndikhoza kumangomuyang’anitsitsa. Ngakhale m’makutu nditaikamo zothandizira kumva, pankhope panga pangamaoneke ngati ndikunena kuti, ‘pepani sindinamvetsetse,’ koma m’chenicheni ndingakhale kuti sindinamve n’komwe.

“Nditayamba kuganizira mmene ndingamamvere nditakhala ndi vuto la kumva, maganizo atsankho omwe ndinali nawo anandichokera.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena