Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g21 No. 1 tsamba 8-9
  • Zimene Tingachite Kuti Tikhale Okhutira

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zimene Tingachite Kuti Tikhale Okhutira
  • Galamukani!—2021
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Tizigwira Ntchito Mwakhama
  • Tizikhala Oona Mtima
  • Muziona Ndalama Moyenera
  • Sankhani Maphunziro Abwino Kwambiri
  • Kodi Mungatani Kuti Musakhale Wokonda Ndalama?
    Galamukani!—2015
  • Kodi Ndalama ndi Zimene Zimabweretsa Mavuto Onse?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Ndalama
    Galamukani!—2014
  • Tiziona Ndalama Moyenera
    Galamukani!—2007
Onani Zambiri
Galamukani!—2021
g21 No. 1 tsamba 8-9
Mayi ndi mwana wake akuyenda mosangalala pakati pa anthu amene akugula zinthu zapamwamba m’mashopu ku India.

Zimene Tingachite Kuti Tikhale Okhutira

Tonsefe, kaya tili pabanja kapena ayi, ana kapena achikulire, timafuna kukhala osangalala komanso okhutira. Mlengi wathu amafunanso kuti tizikhala choncho, ndipo amatipatsa malangizo abwino kwambiri.

Tizigwira Ntchito Mwakhama

“Agwire ntchito molimbikira. Agwire ndi manja ake ntchito yabwino, kuti akhale ndi kanthu kena kopatsa munthu wosowa.”—AEFESO 4:28.

Mlengi wathu amatilimbikitsa kuti tizikhala ndi maganizo oyenera pa nkhani ya ntchito. Chifukwa chiyani? Munthu amene amagwira ntchito molimbika amakhala wosangalala chifukwa amapeza zinthu zofunika pa moyo wake komanso wa banja lake. Angathenso kuthandiza ena amene akufunika thandizo, ndipo amakhalanso wodalirika kwa abwana ake. Choncho munthu amene amagwira bwino ntchito, amakhalitsa pantchitopo. Malemba amafotokoza momveka bwino kuti zotsatirapo za kugwira ntchito mwakhama “ndi mphatso yochokera kwa Mulungu.”​—Mlaliki 3:13.

Tizikhala Oona Mtima

“Tikukhulupirira kuti tili ndi chikumbumtima choona, popeza tikufuna kuchita zinthu zonse moona mtima.”​—AHEBERI 13:18.

Tikakhala oona mtima anthu ena amatilemekeza, timakhala ndi mtendere wamumtima, timagona tulo tabwino komanso anthu ena amatidalira. Koma anthu achinyengo amadzilanda okha zinthu zimenezi komanso chikumbumtima chawo chimawavutitsa ndipo amakhala mwamantha kuti tsiku lina akhoza kudzagwidwa chifukwa cha chinyengo chawocho.

Muziona Ndalama Moyenera

“Moyo wanu ukhale wosakonda ndalama, koma mukhale okhutira ndi zimene muli nazo pa nthawiyo.”​—AHEBERI 13:5.

Timafunika ndalama kuti tigule chakudya ndi zinthu zina zofunikira. Komabe, “kukonda ndalama” n’koopsa kwambiri. Kungachititse munthu kuti azigwiritsa ntchito nthawi komanso mphamvu zambiri kuti azifunafuna ndalama zochuluka. Chifukwa chakuti amangosakasaka ndalama kwambiri, banja lake silingamayende bwino, sangamakhale ndi nthawi yocheza ndi ana ake komanso zingakhudze thanzi lake. (1 Timoteyo 6:9, 10) Ndiponso munthu amene amakonda ndalama akhoza kuyesedwa kuti achite zinthu zachinyengo. Munthu wina wanzeru anati: “Munthu wochita zinthu mokhulupirika adzapeza madalitso ambiri, koma woyesetsa kuti apeze chuma mofulumira, sadzapitiriza kukhala wosalakwa.”​—Miyambo 28:20.

Sankhani Maphunziro Abwino Kwambiri

“Usunge nzeru zopindulitsa ndiponso kuganiza bwino.”​—MIYAMBO 3:21.

Maphunziro abwino amatithandiza kukhala anthu odalirika. Koma maphunziro am’dzikoli paokha sangatithandize kukhala otetezeka komanso osangalala. Kuti zinthu zizitiyendera bwino pa moyo wathu, timafunika maphunziro amene Yehova amatipatsa. Malemba amanena kuti munthu amene amamvera Mulungu, “zochita zake zonse zidzamuyendera bwino.”​—Salimo 1:1-3.

Ndine Wosangalala Komanso Wokhutira

“M’dera limene ndimakhala, anthu ambiri amachita khama kuti apeze maphunziro apamwamba, akhale olemera komanso akhale otchuka. Komabe pambuyo poti akwanitsa zolinga zawozo, sakhalabe osangalala. Koma Baibulo linandithandiza kudziwa kuti chinthu chofunika kwambiri pa moyo ndi chiyani. Ndinaphunzira kuti ndalama zikhoza kutithandizadi m’njira zina, koma sizingagule chimwemwe komanso chikondi chenicheni. Panopa ndine wosangalala komanso wokhutira, chifukwa Baibulo linandithandiza kuti ndizisankha zinthu mwanzeru pa nkhani ya ndalama komanso ntchito.”​—Kishore.

Kishore.

Dziwani zambiri:

Kuti mupeze malangizo ochokera kwa Mlengi wathu okuthandizani pa nkhani ya ntchito, ndalama komanso maphunziro, pitani pa jw.org ndipo pitani pamene alemba kuti ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA > MTENDERE KOMANSO MOYO WOSANGALALA.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena