Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g21 No. 2 tsamba 4-6
  • Kodi Zipangizo Zamakono Zimakhudza Bwanji Ubwenzi Wanu ndi Anthu Ena?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Zipangizo Zamakono Zimakhudza Bwanji Ubwenzi Wanu ndi Anthu Ena?
  • Galamukani!—2021
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • ZIMENE MUYENERA KUDZIWA
  • ZIMENE MUNGACHITE
  • Kodi Mungatani Kuti Mukhale ndi Anzanu Apamtima?
    Galamukani!—2016
  • Kodi Malo Ochezera a pa Intaneti Akusokoneza Moyo Wanga?
    Zimene Achinyamata Amafunsa
  • Nkhani Yovomereza Ana Kugwiritsa Ntchito Intaneti—Gawo 1: Kodi Mwana Wanga Azigwiritsa Ntchito Intaneti?
    Mfundo Zothandiza Mabanja
  • Ndingatani Ngati Makolo Anga Sakundilola Kugwiritsa Ntchito Malo Ochezera a pa Intaneti?
    Zimene Achinyamata Amafunsa
Onani Zambiri
Galamukani!—2021
g21 No. 2 tsamba 4-6
Anthu a m’mayiko osiyanasiyana akucheza pa vidiyokomfelensi.

Kodi Zipangizo Zamakono Zimakhudza Bwanji Ubwenzi Wanu Ndi Anzanu?

Anthu akhoza kulumikizana mosavuta ngakhale atakhala m’mayiko otalikirana kwambiri chifukwa cha kutumizirana mameseji pa foni, maimelo, kulankhulana pa vidiyokomfelensi komanso kucheza pamalo ochezera a pa intaneti. Zipangizo zamakono zimawathandiza kwambiri.

Komabe, anthu amene amakonda kugwiritsa ntchito zipangizo zamakono pofuna kucheza ndi anzawo, nthawi zina . . .

  • amalephera kumvetsa mmene anzawo akumvera.

  • amadzimva kuti ali okhaokha komanso amasowa ocheza naye.

  • amaganizira zofuna zawo zokha kuposa za ena.

ZIMENE MUYENERA KUDZIWA

Mtsikana akuona zinthu pamalo ochezera a pa intaneti usiku. Positi imene akuonayo yaonedwanso ndi anthu ena 723,000.

CHIFUNDO

Kuti tithe kusonyeza ena chifundo timafunika kuganizira mmene akumvera zomwe zimafuna kudekha komanso kuleza mtima. Zimenezi sizingatheke ngati tatanganidwa kuwerenga komanso kutumiza mameseji, kapena kuona zithunzi pamalo ochezera a pa intaneti.

Ngati zipangizo zamakono zikukulamulirani, kuyankha mameseji a anzanu kukhoza kukhala mtolo wokulemetsani. M’malo mofuna kuthandiza mnzanu amene akufunikiradi thandizo, cholinga chanu chimangokhala kuona komanso kuyankha mofulumira mamesejiwo.

ZOTI MUGANIZIRE: Kodi mungasonyeze bwanji kuti ‘mumamvera ena chisoni’ mukamagwiritsa ntchito zipangizo zamakono pocheza ndi anzanu?​—1 PETULO 3:8.

KUSOWA OCHEZA NAYE

Kafukufuku wina anapeza kuti, pambuyo poti aona zinthu zina ndi zina pamalo ochezera a pa intaneti, anthu ambiri amadzimva kuti ndi osafunika. Ochita kafukufukuyu ananena kuti kuona zithunzi kapena zinthu zina zimene anthu ena aika kungachititse munthu kudziona kuti “palibe chilichonse chanzeru chimene wachita.”

Komanso kuona zithunzi zosangalatsa zimene ena aika, kungachititse munthu kuyamba kudziyerekezera molakwika ndi anthu ena. Ndipotu zimaoneka ngati aliyense akusangalala ndi moyo, pomwe inuyo simukusangalala.

ZOTI MUGANIZIRE: Mukamagwiritsa ntchito malo ochezera a pa intaneti, kodi mungatani kuti musamadziyerekezere molakwika ndi anthu ena?​—AGALATIYA 6:4.

KUDZIGANIZIRA TOKHA

Mphunzitsi wina analemba kuti ana ena a m’kalasi mwake anali odzikonda, ndipo ankangofuna kukhala ndi anzawo omwe “angawachitire zinazake.”a Anthu oterewo amangoganizira zimene angapeze kwa anzawowo. Anthu amenewa amaona anzawo ngati foni imene akhoza kungoigwiritsa ntchito akaifuna kenako n’kuizimitsa.

ZOTI MUGANIZIRE: Kodi zimene mumaika pa intaneti, zimasonyeza kuti muli ndi chizolowezi cha mpikisano kapena chomangoganizira za inu nokha?—AGALATIYA 5:26.

ZIMENE MUNGACHITE

GANIZIRANI MMENE MUMAGWIRITSIRA NTCHITO ZIPANGIZO ZAMAKONO

Ngati zipangizo zamakono sizimakulamulirani koma inuyo ndi amene mumazilamulira, zingakuthandizeni kuti mukhale ndi anzanu abwino komanso kuti mukhale nawo pa ubwenzi wolimba.

MFUNDO YA M’BAIBULO: “Chikondi . . . sichisamala zofuna zake zokha.”​—1 AKORINTO 13:4, 5.

Pa mfundo zotsatirazi sankhani zimene mungakonde kuti mugwiritse ntchito kapena lembani zanu zimene mungaganize.

  • Muzicheza ndi anthu pamasom’pamaso (kusiyana n’kumangolemberana mameseji kapena maimelo)

  • Mukamacheza ndi anthu ena muziika patali foni yanu kapena muziika ku sailenti

  • Chepetsani nthawi imene mumakhala mukuona zinthu zimene anthu aika pamalo ochezera a pa intaneti

  • Muzimvetsera ena akamalankhula

  • Muziimbira foni mnzanu amene akukumana ndi mavuto

a Zili m’buku lakuti Reclaiming Conversation.

DZIFUNSENI KUTI . . .

  • Kodi anzanga omwe ndimagwirizana nawo timakondanadi?

  • Kodi ndikangati pamene foni kapena meseji imandisokoneza ndikamacheza ndi munthu pamasom’pamaso?

  • Kodi zithunzi zimene ndimaika pa intaneti komanso makomenti anga zimasonyeza kuti ndimangoganizira za ine ndekha?

  • Kodi ndimamva bwanji pambuyo poona zinthu pamalo ochezera a pa intaneti?

  • Kodi ndingasinthe zinthu ziti kuti zipangizo zamakono zisamandilepheretse kupeza anzanga enieni?

    MFUNDO YA M’BAIBULO: “Musamaganizire zofuna zanu zokha, koma muziganiziranso zofuna za ena.”​—AFILIPI 2:4.

Emily.

“Kuti upeze anzako enieni zimatenga nthawi komanso pamafunika khama, choncho tinganene kuti munthu umakhala ndi anzako ochepa. Chofunika sikukhala ndi anzako ambirimbiri, koma kukhala ndi anzako a makhalidwe abwino amene mumafunirana zabwino.”​—EMILY

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena