Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g21 No. 2 tsamba 10-12
  • Kodi Zipangizo Zamakono Zimakhudza Bwanji Banja Lanu?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Zipangizo Zamakono Zimakhudza Bwanji Banja Lanu?
  • Galamukani!—2021
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • ZIMENE MUYENERA KUDZIWA
  • ZIMENE MUNGACHITE
  • Kodi Mungatani Kuti Zipangizo Zamakono Zisamakusokonezeni?
    Mfundo Zothandiza Mabanja
  • Zimene Mungachite Kuti Musamagwire Ntchito Pamene Simuli Kuntchito
    Mfundo Zothandiza Mabanja
  • Mungatani Kuti Mupewe Kuthetsa Banja Pambuyo Pokhala Limodzi kwa Zaka Zambiri?
    Mfundo Zothandiza Mabanja
  • Zimene Mungachite Ngati Mumacheza Kwambiri ndi Munthu Amene si Mwamuna Kapena Mkazi Wanu
    Galamukani!—2013
Onani Zambiri
Galamukani!—2021
g21 No. 2 tsamba 10-12
Bambo ali pabwalo la ndege ndipo akulankhula pafoni ndi mkazi wake amene ali kunyumba.

Kodi Zipangizo Zamakono Zimakhudza Bwanji Banja Lanu?

Zipangizo zamakono zikamagwiritsidwa ntchito moyenera zikhoza kulimbitsa ubwenzi umene umakhalapo pakati pa mwamuna ndi mkazi wake. Mwachitsanzo, zingathandize anthu okwatirana kuti azilankhulana nthawi iliyonse.

Komabe anthu ena omwe ali pabanja amagwiritsa ntchito molakwika zipangizo zawo zamakono, ndipo amalola kuti . . .

  • asamakhale ndi nthawi yochezera limodzi.

  • azigwirira ntchito kunyumba popanda zifukwa zomveka.

  • abise zinthu zina ngakhalenso kusiya kukhulupirirana.

ZIMENE MUYENERA KUDZIWA

Mwamuna ndi mkazi wake ali pabedi ndipo aliyense akugwiritsa ntchito foni yake pakati pa usiku.

MUKAMACHITIRA ZINTHU LIMODZI

Mwamuna wina dzina lake Michael ananena kuti: “Nthawi zina ndikamacheza ndi mkazi wanga zimangokhala ngati iyeyo ‘palibepo.’ Amangokhalira pafoni ndipo amanena kuti, ‘Chichereni sindinagwireko foni.’” Mwamuna wina dzina lake Jonathan ananena kuti n’zochitika ngati zimenezi “anthu okwatirana amaoneka ngati ali limodzi koma zisali choncho.”

ZOTI MUGANIZIRE: Kodi ndi kangati pamene foni kapena meseji imakusokonezani mukamacheza ndi mkazi kapena mwamuna wanu?​—AEFESO 5:33.

NTCHITO

Anthu ena amagwira ntchito imene imafunika kuti aziyankha foni kapenanso maimelo pamene ali kunyumba. Pomwe ena amene ntchito yawo sifuna nthawi yambiri, amagwirabe ngakhale pamene ali kunyumba. Mwamuna wina dzina lake Lee ananena kuti: “Zimakhala zovuta kuti ndisamayankhe foni kapena meseji iliyonse imene yabwera yochokera kuntchito pa nthawi imene ndapatula kuti ndicheze ndi mkazi wanga.” Mayi wina dzina lake Joy ananena kuti: “Ndimagwirira ntchito kunyumba choncho nthawi zonse ndimakhala ndikugwira ntchito. Zimafunika khama kuti uzigawa bwino nthawi.”

ZOTI MUGANIZIRE: Mwamuna kapena mkazi wanu akamalankhula nanu, kodi mumamvetsera mwatcheru?​—LUKA 8:18.

KUKHULUPIRIKA

Kafukufuku wina anasonyeza kuti anthu okwatirana amayamba kukayikirana chifukwa cha zimene mmodzi wa iwo waika pamalo ochezera a pa intaneti. Anthu 10 mwa 100 alionse amene anafunsidwawa ananena kuti ankaika zinthu pamalo ochezera a pa intaneti zomwe sankafuna kuti mwamuna kapena mkazi wawo adziwe.

Anthu ambiri amakhulupirira kuti malo ochezera a pa intaneti ali ndi zinthu zambiri “zoopsa zomwe ndi zobisika” komanso amachititsa kuti “kuchita chigololo kukhale kosavuta.” N’zosadabwitsa kuti maloya ena oona nkhani zothetsa ukwati amanena kuti nthawi zambiri malo ochezera a pa intaneti ndi amene amachititsa kuti mabanja ambiri azitha.

ZOTI MUGANIZIRE: Kodi mumabisirana nkhani zimene mumacheza ndi munthu amene si mwamuna kapena mkazi mnzanu?—MIYAMBO 4:23.

ZIMENE MUNGACHITE

MUZIDZIWA ZINTHU ZOFUNIKA KWAMBIRI

Munthu amene amanyalanyaza kudya, sakhala ndi thanzi labwino. Mofanana ndi zimenezi, munthu amene amanyalanyaza kucheza ndi mkazi kapena mwamuna wake amakumana ndi mavuto ambiri m’banja lake.​—Aefeso 5:28, 29.

MFUNDO YA M’BAIBULO: “Muzitsimikizira kuti zinthu zofunika kwambiri ndi ziti.”​—AFILIPI 1:10.

Kambiranani mfundo zimene zili m’munsimu zomwe mungakonde kuti muzigwiritse ntchito, kapena lembani zanu zomwe zingathandize kuti zipangizo zamakono zisamasokoneze banja lanu.

  • Tsiku lililonse tiziyesetsa kuti ngakhale kamodzi tizidyera limodzi chakudya

  • Kukhala ndi nthawi yoti tisamagwiritse ntchito zipangizo zamakono

  • Kupeza nthawi yapadera yochitira limodzi zinthu zosangalatsa kapena kukaona malo enaake

  • Kuzimitsa mafoni usiku komanso kuwaika patali ndi pomwe timagona

  • Kuzimitsa mafoni kwa 15 minitsi tsiku lililonse, n’cholinga choti tizilankhulana popanda chosokoneza chilichonse

  • Tsiku lililonse kukhala ndi nthawi inayake yoti tisamagwiritse ntchito intaneti

ZOTI MABANJA AKAMBIRANE

Yambani ndi kuwerenga komanso kuganizira mafunsowa panokha, ndipo kenako kambiranani mayankho ake ndi mwamuna kapena mkazi wanu.

  • Kodi mungagwiritse ntchito bwanji zipangizo zanu zamakono kuti zilimbitse banja lanu?

  • Kodi inuyo panokha mukuganiza kuti zipangizo zamakono zimasokoneza banja lanu kufikira pati?

  • Kodi mungakonde kusintha zinthu ziti?

  • Kodi mumakwanitsa kuti mukakhala kunyumba musamagwire ntchito pa zipangizo zamakono? Nanga mwamuna kapena mkazi wanu angavomereze zimene mwayankhazo?

  • Kodi mungasonyeze bwanji kuti ndinu oganiza bwino pa nthawi imene mumafuna kuti mwamuna kapena mkazi wanu azicheza nanu?

    MFUNDO YA M’BAIBULO: “Aliyense asamangodzifunira zopindulitsa iye yekha basi, koma zopindulitsanso wina.”​—1 AKORINTO 10:24.

Jason ndi Alexandra.

“Ndimagwirira ntchito kunyumba, choncho ndimayesetsa kuweruka pa nthawi yake. Nthawi inayake ikakwana, ndimazimitsanso mauthenga ondidziwitsa kuti kwabwera imelo kuti ndizigwiritsa ntchito foni yanga pa zinthu zina n’cholinga choti ntchito isandisokoneze.”​—JASON NDI MKAZI WAKE ALEXANDRA

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena