Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g22 No. 1 tsamba 4-6
  • 1 | Muziteteza Thanzi Lanu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • 1 | Muziteteza Thanzi Lanu
  • Galamukani!—2022
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • CHIFUKWA CHAKE ZILI ZOFUNIKA
  • Zimene Muyenera Kudziwa
  • Zimene Mungachite Panopa
  • Zimene Mungachite Kuti Mukhale Ndi Moyo Wathanzi
    Galamukani!—2015
  • Zimene Zingakuthandizeni Ngati Mwayamba Kudwala Mwadzidzidzi
    Nkhani Zina
  • Mmene Mungatetezere Thanzi Lanu
    Galamukani!—1999
  • Sungirirani Chikhulupiriro Chanu ndi Umoyo Wauzimu
    Nsanja ya Olonda—1989
Onani Zambiri
Galamukani!—2022
g22 No. 1 tsamba 4-6
Zakudya zopatsa thanzi zosiyanasiyana zili patebulo.

MAVUTO A M’DZIKOLI

1 | Muziteteza Thanzi Lanu

CHIFUKWA CHAKE ZILI ZOFUNIKA

Mavuto kapena ngozi zam’chilengedwe zikhoza kukhudza thanzi lathu m’njira zosiyanasiyana.

  • Zinthu zoipa zikachitika, anthu amakhala ndi nkhawa, ndipo amene amakhala ndi nkhawa kwa nthawi yaitali akhoza kudwala.

  • Kukabuka miliri, zipatala zimalephera kusamalira bwinobwino odwala, chifukwa amafunika kusamalira anthu ambirimbiri pa nthawi imodzi ndipo mankhwala amasowa.

  • Masoka amabweretsa mavuto azachuma ndipo zimenezi zimachititsa kuti anthu alephere kupeza zinthu zofunika monga chakudya chopatsa thanzi komanso amalephera kulipira thandizo la zachipatala.

Zimene Muyenera Kudziwa

  • Kudwala kwambiri komanso kuvutika maganizo kungasokoneze mmene mumaganizira ndipo zimenezi zingachititse kuti musamachite zinthu zosamalira thanzi lanu. Pamapeto pake matenda anu akhoza kuwonjezereka.

  • Ngati simungasamalire mavuto a thanzi omwe muli nawo, mavutowo akhoza kukula kwambiri ndipo akhoza kuwononga moyo wanu.

  • Mukakhala ndi thanzi labwino, sizingakuvuteni kusankha zinthu mwanzeru panthawi imene mwakumana ndi mavuto.

  • Kaya ndinu wolemera kapena wosauka, mukhoza kuchita zinthu zimene zingateteze thanzi lanu.

Zimene Mungachite Panopa

Munthu wanzeru amadziwiratu zoipa zimene zingachitike ngati angathe ndipo amachita zinthu mosamala kuti azipewe. Zimenezi zingagwirenso ntchito pa nkhani ya thanzi lanu. Nthawi zambiri mungapewe kutenga matenda kapena kuthandiza kuti asafalikire kwambiri pokhala aukhondo. Pajatu kupewa kumaposa kuchiza.

“Tikamayesetsa kukhala aukhondo komanso kusamalira pakhomo pathu, timakhala tikupulumutsa ndalama zimene tikanagwiritsa ntchito popitira kuchipatala komanso kugula mankhwala.”​—Andreas.a

a Mayina ena asinthidwa m’magaziniyi.

KODI MUNGATANI KUTI MUPIRIRE?​—Mfundo Zimene Zingakuthandizeni

Pa nthawi ya mavuto, muziteteza thanzi lanu pochita zinthu izi

MUZIKHALA AUKHONDO

Bambo ali panja ndipo akusamba m’manja ndi sopo.

Muzikhala aukhondo

Baibulo limanena kuti: “Wochenjera ndi amene amati akaona tsoka amabisala.” (Miyambo 22:3) Muzidziwiratu komanso kupewa zinthu zomwe zingaike moyo wanu pangozi.

  • Muzisamba m’manja ndi sopo pafupipafupi, makamaka musanagwire chakudya komanso mukachoka kuchimbudzi.

  • Nthawi zonse muzikonza m’nyumba mwanu ndi kupopera mankhwala ophera tizilombo komanso kupukuta malo komanso zinthu zimene zimagwiridwa pafupipafupi.

  • Ngati n’zotheka, musamayandikane kwambiri ndi anthu amene akudwala matenda opatsirana.

MUZIDYA ZAKUDYA ZOPATSA THANZI

Zakudya zopatsa thanzi zosiyanasiyana zili patebulo.

Muzidya zakudya zopatsa thanzi

Baibulo limanena kuti: “Palibe munthu anadapo thupi lake, koma amalidyetsa ndi kulikonda.” (Aefeso 5:29) Timasonyeza kuti timakonda thupi lathu tikamakhala osamala ndi zinthu zimene timadya.

  • Muzimwa madzi ambiri.

  • Muzidya zipatso komanso masamba osiyanasiyana.

  • Musamadye za mafuta ambiri, mchere wambiri komanso shuga wambiri.

  • Musamasute fodya, kumwa mowa kwambiri kapena kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo.

“Kuti tisamadwaledwale, timayesetsa kudya zakudya zopatsa thanzi. Kupanda kutero ndiye kuti tingamawononge tindalama tochepa timene timapezati, kulipirira thandizo la chipatala. Timaona kuti ndi bwino kugwiritsa ntchito ndalamazi kugulira chakudya chopatsa thanzi.”—Carlos.

MUZICHITA MASEWERA OLIMBITSA THUPI KOMANSO MUZIGONA MOKWANIRA

Bambo akuthamanga mumsewu wa fumbi.

Muzichita masewera olimbitsa thupi

Baibulo limanena kuti: “Kupuma pang’ono kuli bwino kuposa kugwira ntchito mwakhama ndi kuthamangitsa mphepo.” (Mlaliki 4:6) N’zoona kuti timafunika kugwira ntchito koma tiyeneranso kumapuma mokwanira.

  • Muzichita masewera olimbitsa thupi. Mukhoza kuyamba pang’onopang’ono koma mobwerezabwereza. Kuchita masewera olimbitsa thupi kungakuthandizeni kwambiri, kaya ndinu achikulire, olumala kapena mukudwala matenda okhalitsa.

  • Mtsikana akugona.

    Muzipuma mokwanira

    Muzipuma mokwanira. Ngati mungamalephere kugona mokwanira, mungamakhale ndi nkhawa komanso mungamalephere kuika maganizo anu onse pa zimene mukuchita. Zimenezi zikachitika kwa nthawi yaitali, zikhoza kuwononga kwambiri thanzi lanu.

  • Muzidziikira nthawi yoti muzigona, ndipo muzigonadi nthawiyo ikakwana. Muziyesetsa kugona komanso kudzuka nthawi yofananayo tsiku lililonse.

  • Muzipewa kuonera TV kapena kugwiritsa ntchito zipangizo zamakono mukapita kogona.

  • Musamadye kwambiri, musamamwe zakumwa zokhala ndi caffeine, ngati khofi komanso musamamwe mowa mukatsala pang’ono kugona.

“Ndimaona kuti kugona kumakhudza kwambiri thanzi langa. Ngati sindinagone mokwanira, nthawi zina mutu umandipweteka komanso thupi limaphwanya. Koma ndikagona mokwanira, ndimaona kuti ndine wokonzeka kuchita chilichonse chomwe ndimafuna kuchita. Ndimakhala ndi mphamvu zambiri komanso sindimadwaladwala.”​—Justin.

Chithunzi cha muvidiyo yakuti “Zimene Mungachite Kukagwa Mliri Woyambitsidwa Ndi Mavailasi.” Mayi akutsegula chitseko cha nyumba yake kuti mulowe vairasi.

DZIWANI ZAMBIRI. Onerani vidiyo yakuti Zimene Mungachite Kukagwa Mliri Woyambitsidwa Ndi Mavailasi. Komanso werengani nkhani yakuti “Zimene Mungachite Kuti Mukhale Ndi Moyo Wathanzi.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena