Pa nthawi yamavuto mungasamale ndalama zanu pogwiritsa ntchito njira zimenezi
MUZICHEPETSA ZINTHU ZIMENE MUMAGULA
Muzichepetsa zinthu zimene mumagula
Musamapupulume kugula zipangizo kapena zovala zatsopano. Muzidzifunsa kuti: ‘Kodi ndikufunikiradi galimoto? Kodi ndingalime dimba la masamba?’
Musanagule chinthu muzidzifunsa kuti: ‘Kodi ndichofunikiradi? Kodi ndikwanitsa kugula?’
Ngati kwanu zimachitika, mungalembetse kuboma kapena ku mabungwe kuti muzilandira chithandizo.
“Monga banja, tinakhala pansi n’kuonanso mmene timagwiritsira ntchito ndalama. Tinachepetsa ndalama zimene timagwiritsa ntchito pochitira zosangalatsa. Tinayambanso kukonza chakudya chosawononga ndalama zambiri.”—Gift.
MUZIPANGA BAJETI
Muzipanga bajeti
Baibulo limanena kuti: “Zolinga za munthu wakhama zimam’pindulira, koma aliyense wopupuluma, ndithu adzasauka.” (Miyambo 21:5) Kupanga bajeti kumakuthandizani kuti musamawononge ndalama zambiri kuposa zimene mumapeza.
Choyamba, lembani ndalama zimene mupeze mwezi umenewo.
Chachiwiri, onani zinthu zimene mumafunika kulipira mwezi uliwonse.
Kenako yerekezerani zimene mumapeza ndi zimene mumagwiritsa ntchito, ndipo ngati n’zotheka mungachepetse kapena kuchotsa zina kuti zigwirizane ndi zimene mumapeza.
“Mwezi uliwonse timalemba ndalama zimene timapeza komanso zimene tikufunika kugwiritsa ntchito. Timayesetsa kusunga ndalama zogwiritsa ntchito pa zinthu zadzidzidzi komanso za zinthu zimene tikufuna kudzagula m’tsogolo. Tikamachita zimenezi sitikhala ndi nkhawa, chifukwa timadziwiratu mmene tingagwiritsire ntchito ndalama zimene timapeza.”—Carlos.
MUZIPEWA NGONGOLE / MUZISUNGA NDALAMA
Muzipewa ngongole / muzisunga ndalama
Muzikhala ndi pulani yabwino kuti mubweze ngongole zimene muli nazo. Ngati n’kotheka, musamakongole ndalama n’komwe. M’malomwake muziyesetsa kusunga ndalama kuti mugule zimene mukufuna.
Mwezi uliwonse muzisunga kandalama koti mudzagwiritse ntchito pa zinthu zimene mukudziwiratu kapena zadzidzidzi.
MUZILIMBIKIRA NTCHITO
Baibulo limanena kuti: “Kugwira ntchito iliyonse kumapindulitsa.”—Miyambo 14:23.
Muzilimbikira ntchito
Muziona ntchito yanu moyenera. Ngakhale itakhala kuti si imene munkafuna, komabe imakupatsani ndalama.
Muziyesetsa kugwira ntchito mwakhama komanso muzikhala odalirika. Zimenezi zidzakuthandizani kuti mukhalebe pa ntchitoyo, komabe ngati ingathe, simudzavutika kupeza ina m’tsogolo.
“Ndimagwira ntchito iliyonse imene yapezeka, ngakhale ntchito yake si imene ndimafuna kapena ndalama zake ndi zochepa. Ndimayesetsa kukhala wodalirika komanso kugwira bwino ntchito ngati kuti ntchitoyo ndi yanga.”—Dmitriy.
Ngati mukufuna ntchito . . .
Muzichitapo kanthu. Muzifunsira ntchito ku makampani amene kungakhale ntchito zimene mungagwire ngakhale sanalengeze kuti akufuna anthu antchito. Muziuza anzanu komanso achibale kuti mukufunafuna ntchito.
Muzikhala okonzeka kusintha. N’zovuta kuti mungapeze ntchito yomwe ili ndi zonse zimene mumafuna.