Pa nthawi ya mavuto mungateteze ubwenzi wanu pochita zotsatirazi
MUZILIMBITSA BANJA LANU
Muzilimbitsa banja lanu
Baibulo limanena kuti: “Awiri amaposa mmodzi . . . Ngati mmodzi wa iwo atagwa, winayo akhoza kum’dzutsa mnzakeyo.” (Mlaliki 4:9, 10) Anthu okwatirana ayenera kumachita zinthu ngati anthu awiri oyendetsa ndege imodzi omwe amakhala ndi cholinga chimodzi, osati ngati ali mundege ziwiri zosiyana zomwe zikufuna kuphulitsana
Muziyesetsa kuti musamachitire chipongwe mkazi kapena mwamuna wanu, chifukwa cha mavuto amene mukukumana nawo. Ndipo muzikhala oleza mtima komanso ololera.
Mwina kamodzi pa wiki, muzikambirana ndi mkazi kapena mwamuna wanu za mavuto amene mukuyenera kuwakonza. Cholinga chanu chiyenera kukhala cholimbana ndi vutolo, osati kulimbana nokhanokha.
Muzipeza nthawi yochitira zinthu limodzi zimene nonse mumakonda..
Muzikumbukira nthawi yosangalatsa imene munkachitira zinthu limodzi, mwachitsanzo mungaone limodzi zithunzi za pa ukwati wanu.
“Anthu okwatirana sangamagwirizane pa chilichonse, koma zimenezi sizikutanthauza kuti sangamachitire zinthu limodzi. Iwo akhoza kusankha limodzi zochita kenako n’kuthandizana kuti akwaniritse zimene asankhazo.”—David.
MUZILIMBITSA UBWENZI WANU NDI ANZANU
Muzilimbitsa ubwenzi wanu ndi anzanu
Kuwonjezera pa kulandira thandizo kuchokera kwa anzanu, muziganizira mmene inuyo mungawathandizire. Mukamalimbikitsa ena, inunso mumalimbikitsidwa.
Tsiku lililonse muziimbira foni kapena kulembera mameseji anzanu kuti mudziwe mmene zinthu zilili pa moyo wawo.
Muzifunsa anzanu mmene akukwanitsira kupirira mavuto ofanana ndi amene inunso mukukumana nawo.
“Mukakumana ndi mavuto aakulu, anzanu angakuthandizeni. Iwo angakuthandizeni kudziwa zochita ngakhale atangokukumbutsani zimene mukudziwa kale. Anzanu amakuganizirani, ndipo iwonso amadziwa kuti mumawaganizira.”—Nicole.
MUZIKHALA KHOLO LOTHANDIZA
Muzikhala kholo lothandiza
Baibulo limanena kuti: “Munthu aliyense akhale wofulumira kumva, wodekha polankhula.” (Yakobo 1:19) Poyamba, ana anu angamavutike kukufotokozerani zinthu zimene zikuwadetsa nkhawa ndiponso zimene akuganiza, koma mukamawamvetsera mwatcheru, akhoza kumasuka ndi kukufotokozerani.
Muzipeza malo komanso mpata wabwino kuti ana anu amasuke kufotokoza zimene zikuwadetsa nkhawa. Ana ena amaona kuti amamasuka kufotokoza zamumtima mwawo akakhala m’galimoto, akamayenda, kapena akamadya limodzi ndi makolo awo osati akakhala pansi n’kumayang’anizana nawo.
Muzionetsetsa kuti ana anu asamaonere kwambiri nkhani zoopsa.
Muzithandiza ana anu kudziwa zimene banja lanu lakonza kuti mukhale otetezeka.
Muzidziwiratu zimene mungachite ngati patachitika zinthu zadzidzidzi, ndipo muziyeserera kuchita zimenezo ndi ana anu.
“Muzilankhula ndi ana anu ndipo muziwalola kuti afotokoze mmene akumvera. Akhoza kumadzibisa kuti asaoneke kuti ali ndi mantha, nkhawa kapenanso akwiya. Muziwauza ana anu kuti nthawi zina inunso mumamva choncho, ndiponso muziwauza zimene mumachita kuti muyambe kumva bwino.”—Bethany.