Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g22 No. 1 tsamba 13-15
  • 4 | Muziteteza Chiyembekezo Chanu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • 4 | Muziteteza Chiyembekezo Chanu
  • Galamukani!—2022
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • CHIFUKWA CHAKE ZILI ZOFUNIKA
  • Zimene Muyenera Kudziwa
  • Zimene Mungachite Panopa
  • Baibulo Limapereka Chiyembekezo Chodalirika
  • Kodi Chiyembekezo Ndingachipeze Kuti?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Baibulo Limatithandiza Kuti Tikhale Ndi Chiyembekezo
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
  • Baibulo Limatithandiza Kukhala Ndi Chiyembekezo
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Yambani Kuphunzira Baibulo
  • Mungakhale Ndi Chiyembekezo Chabwino mu 2024—Kodi Baibulo Limanena Zotani?
    Nkhani Zina
Onani Zambiri
Galamukani!—2022
g22 No. 1 tsamba 13-15
Baibulo lotsegula lili pafupi ndi mphika wa maluwa.

MAVUTO A M’DZIKOLI

4 | Muziteteza Chiyembekezo Chanu

CHIFUKWA CHAKE ZILI ZOFUNIKA

Nkhawa zobwera chifukwa cha mavuto a m’dzikoli zingakhudze anthu m’njira zosiyanasiyana. Anthu ambiri amene amakhudzidwa ndi zimenezi amakhala opanda chiyembekezo ndipo amati zinthu sizingasinthe. Kodi ndiye amachita zotani?

  • Ena safuna n’komwe kuganizira zam’tsogolo.

  • Ena amamwa mowa kapena kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo kuti aiwale mavuto.

  • Enanso amaona kuti kuli bwino kungofa ndipo amafunsa kuti, “Moyo uli ndi phindu lanji?”

Zimene Muyenera Kudziwa

  • Mavuto ena amene mumakumana nawo akhoza kukhala a kanthawi ndipo akhoza kutha nthawi iliyonse.

  • Ngakhale zitakhala kuti mavuto amene mukumana nawo sangasinthe, pali zina zimene mungachite kuti mupirire.

  • Baibulo limatipatsa chiyembekezo chodalirika. Limati mavuto onse amene timakumana nawo panopa adzatha.

Zimene Mungachite Panopa

Baibulo limanena kuti: “Musamade nkhawa za tsiku lotsatira, chifukwa tsiku lotsatira lidzakhala ndi zodetsa nkhawa zakenso. Zoipa za tsiku lililonse n’zokwanira pa tsikulo.”​—Mateyu 6:34.

Muzithana ndi nkhawa za tsiku lililonse palokha. Musamadere nkhawa zamawa mpaka kufika polephera kuchita zinthu zofunika zalero.

Kumangodera nkhawa zinthu zoipa zimene mukuona ngati zichitika, kungangokuwonjezerani nkhawa ndipo kungakuchititseni kuti muzikayikira kuti m’tsogolo mavuto adzatha.

KODI MUNGATANI KUTI MUPIRIRE?​—Mfundo Zimene Zingakuthandizeni

MUZIGANIZIRA ZABWINO

Mzimayi akuyang’ana panja kudzera pawindo mosangalala.

Baibulo limanena kuti: “Masiku onse a munthu wosautsika amakhala oipa, koma munthu wamtima wosangalala amachita phwando nthawi zonse.” (Miyambo 15:15) Mukamangokhalira kuganizira zinthu zoipa, simungapeze njira yothetsera mavuto anu. Koma kuganizira zabwino, kungakuthandizeni kuti mupeze njira yothetsera mavuto amene mukukumana nawo.

  • Musamangokhalira kuonera kapena kumvetsera nkhani.

  • Tsiku lililonse likamatha, muzilemba zinthu ziwiri ­kapena zitatu zimene mungathokoze.

  • Muzilemba ndandanda ya zinthu zimene mukufuna kuchita tsiku limenelo. Ngati muli ndi mapulani a zinthu zikuluzikulu, muzizigawa kuti zikhale zing’onozing’ono n’cholinga choti muzitha kuona zomwe mwakwanitsa kuchita tsiku likamatha.

MUZILOLA KUTI ENA AZIKUTHANDIZANI

Bambo wachikulire akulimbikitsa wachinyamata.

Baibulo limanena kuti: “Wodzipatula . . . amachita zosemphana ndi nzeru zonse zopindulitsa.” (Miyambo 18:1) Panokha simungakwanitse kutuluka m’dzenje lakuya, koma ngati munthu wina atakuthandizani, mungakwanitse.

  • Muzipempha anzanu kapena achibale kuti akuthandizeni.

  • Muzipeza njira za mmene inuyo mungathandizire ena. Kuthandiza ena kungakuchititseni kuti muziona mavuto anu moyenera.

  • Ngati mukuona kuti mavuto sadzatha, ndipo mukuonanso kuti moyo ndi wosafunika, mukhoza kukaonana ndi adokotala. Nthawi zina kuda nkhawa kwambiri ndi chizindikiro choti simuli bwino, mwina mukudwala matenda ovutika maganizo. Anthu ambiri amathandizidwa akapita kuchipatala.a

a Magazini ya Galamukani! sisankhira anthu thandizo la mankhwala.

Baibulo Limapereka Chiyembekezo Chodalirika

Wolemba masalimo wina anapemphera kwa Mulungu kuti: “Mawu anu ndi nyale younikira kumapazi anga, ndi kuwala kounikira njira yanga.” (Salimo 119:105) Kodi Baibulo lomwe ndi mawu a Mulungu limachita bwanji zimenezi?

Tikamayenda usiku, nyale imatithandiza kuona pamene tingaponde. Mofananamo, m’Baibulo muli malangizo anzeru omwe angatithandize tikamapanga zosankha zovuta.

Kuwala kumatithandiza kuti tione kumene tikupita. Mofanana ndi zimenezi, Baibulo limatithandiza kudziwa zinthu zimene zichitike m’tsogolo.

Baibulo ndi Buku lopatulika lomwe limafotokoza mmene moyo wamunthu unayambira. Limafotokozanso chiyembekezo chodalirika cha zomwe zichitike m’tsogolo. Limafotokoza:

Baibulo ndi Buku lopatulika lomwe limafotokoza mmene moyo wamunthu unayambira. Limafotokozanso chiyembekezo chodalirika cha zomwe zichitike m’tsogolo. Limafotokoza:

Mmene

Mmene mavuto anayambira: Baibulo limanena kuti, “monga mmene uchimo unalowera m’dziko kudzera mwa munthu mmodzi, ndi imfa kudzera mwa uchimo, imfayo n’kufalikira kwa anthu onse chifukwa onse anachimwa.”​—Aroma 5:12.

Chifukwa

Chifukwa chake ulamuliro wa anthu walephera kuthetsa mavuto athu: Baibulo limanena kuti, “munthu wochokera kufumbi alibe ulamuliro wowongolera njira ya moyo wake.” (Yeremiya 10:23) Umboni wa zimenezi ndi mmene mavuto achulukira m’dzikoli.

Zimene

Zimene Mulungu adzachite kuti akonze dzikoli: Baibulo limanena kuti, “iye adzapukuta misozi yonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka.”​—Chivumbulutso 21:4.

Chithunzi cha muvidiyo yakuti “N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kuphunzira Baibulo?” Mayi akufotokozera mwamuna wake zimene wawerenga m’Baibulo.

DZIWANI ZAMBIRI. Onerani vidiyo yakuti N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kuphunzira Baibulo?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena