Mutu 9
Cifukwa Cace Cimene “Kagulu Kankhosa” Kamapita Kumwamba
1. (a) Pamene Yesu anali pa dziko lapansi, kodi nciani cimene anawauza atsatiri ace ponena za moyo wakumwamba? (b) Ncifukwa ninji anthu ambiri amafuna kupita kumwamba?
PAMENE Yesu Kristu anali cikhalirebe limodzi ndi atsatiri ace pano pa dziko lapansi, iye analankhula nawo za moyo wakumwamba. Iye anawauza iwo kuti iye anali kupita kukawakonzera iwo malo ndi kuti, mu nthawi yace, iwo adzakhala kumeneko limodzi naye. (Yohane 14:1-3) Mamiliyoni ambiri a anthu acipanga kukhala colinga cao kuti akhale ndi moyo wakuwamba umenewo. Kwa iwowo kumapereka ciyembekezo ca cimasuko ku mabvuto a moyo uno. Koma kodi mumacidziwa cifukwa cace Mulungu walinganizira kuti anthu ena apite kumwamba? Kodi mumacidziwa cimene adzacicita kumeneko?
2. (a) Kodi ufumu wa Mulungu nciani, ndipo kodi uwo wakhazikitsidwa kuti? (b) Cotero, pamene Yesu ananena kuti “kagulu ka nkhosa” kadzalowa “ufumuwo,” kodi zinatanthauzanji?
2 Mkati mwa utumiki wace wa pa dziko lapansi Yesu ananena zambiri ponena za “ufumu wa Mulungu.” Iye anawaphunzitsa atsatiri ace kupemphera kuti, mwanjira ya Ufumuwo, cifuniro ca Mulungu cidzacitidwa pano pa dziko lapansi. Motero, dziko lapansi lidzafikira kukhala kwao kokongola kwa mtundu wa anthu. Koma ufumuwo, kapena bomalo, lidzakhala la Mulungu la kumwamba, ndipo pa cifukwa ca ici Yesu kawirikawiri analichula ilo kukhala “Ufumu wa Kumwamba.” (Mateyu 5:20; 6:9, 10) Ici cimatithandiza ife kucizindikira cimene iye anacitanthauza pamene iye anati: “Musaopa, kagulu ka nkhosa inu; cifukwa Atate wanu akonda kukupatsani Ufumu.” (Luka 12:32) Inde, Mulungu adzakapatsa “kagulu ka nkhosa” aka mbali m’boma lakumwambalo limene lidzalamulira mtundu wonse wa anthu.
3. Kodi nciani cimene Cibvumbulutso 20:6 cimanena kuti awo amene adzaukitsidwira ku moyo wakumwamba adzacicita kumeneko?
3 Pa Cibvumbulutso 20:6 timawerenga ponena za awo amene adzaukitsidwira ku moyo wakumwamba: “Adzakhala ansembe a Mulungu ndi a Kristu, nadzacita ufumu pamodzi ndi Iye zaka cikwizo.” Yesu Kristu ndiye mfumu yaikuru ndiponso mkuru wansembe, ndipo anthu okhulupirika awa amene atengedwa kucokera ku dziko lapansi akutumikira limodzi naye.—Chivumbulutso 5:9, 10.
4. Kodi ncifukwa ninji kuli koyenerera kuti awo amene Mulungu wawalinganiza kuti adzakhale mu ufumu wa kumwamba atengedwe kucokera ku dziko lapansili?
4 Kodi ncifukwa ninji akusankhidwa kucokera ku dziko lapansi kaamba ka nchito yoteroyo? Cifukwa cakuti panali pano pa dziko lapansi pamene ulamuliro wa Yehova unajededwapo. Panali panopo pamene kukhulupirika kwa anthu kulinga kwa Mulungu kunaikidwa pa ciyeso mwa citsutso cocokera kwa Mdierekezi. Panali panopo pamene Yesu anakutsimikizira kukhulupirika kwace kotheratu kwa Mulungu kucipyola ciyeso ndipo anaupereka moyo wace monga dipo kaamba ka mtundu wa anthu. Cotero kunali kucokera pa dziko lapansi ili pamene Yehova analinganiza za kukatenga “kagulu ka nkhosa” ka anthu kuti akagwirizane ndi Mwana wace mu ufumu wakumwambawo. Ali anthu amene amasonyeza cikhulupiriro cokwanira m’makonzedwe a Mulungu a cipulumutso kupyolera mwa Kristu. Ali awo amene miyoyo yao imamtsimikizira Mdierekezi kukhala wabodza pamene iye ananena kuti anthu amamtumikira Mulungu kokha cifukwa ca zifukwa zadyera. Yehova moziziwitsa walinganiza kuti awagwiritsire iwo nchito kaamba ka ulemerero wace.—Aefeso 1:9-12.
5. (a) Kodi ncifukwa ninji ali makonzedwe acikondi a Mulungu kuwaika pa malo olamulira awo amene azidziwa zothetsa nzeru zimene mtundu wa anthu umakumana nazo mofala? (b) Kodi ndi madalitso otani amene okhala pa dziko lapansi adzasangalala nawo pamene ansembe akumwamba amenewa agwiritsira nchito mapindu a nsembe ya dipo ya Kristu?
5 Monga mafumu ndi ansembe omatsogozedwa ndi Yesu Kristu, iwo adzatumikira ali kumwambako m’kumacikwaniritsa cifuniro ca Yehova kulinga ku mtundu wa anthu. Kodi ndi kodabwitsa cotani nanga mmene kudzakhalira kukhala nao monga olamulira awo amene atsimikizira kukhala okhulupirika kwa Mulungu! (Cibvumbulutso 20:4) Ndipo ha, ndi cokondi cotani nanga ca Mulungu kwawagwiritsira nchito awo amene anakumana nazo zothetsa nzeru zimene ziri zofala pakati pa mtundu wa anthu! Ndithudi, iwowo, mofanana ndi Kristu, adzacita nawo awo amene adzakhala akuwalamulirawo mozindikira za mkhalidwe wao. (Ahebri 2:17, 18) Kodi ndi dalitso lotani nanga mmene ililo lidzakhalira kwa anthu okhala pa dziko lapansi pamene ansembe akumwamba amenewa adzawapereka kwa iwo mapindu a nsembe ya dipo ya Kristu, kumawaciritsa iwo mwauzimu, mwamaganizo ndi mwakuthupi kufikira iwo adzaufikira ungwiro!—Cibvumbulutso 21:2-4.
KODI NDI ANGATI AMENE AMAPITA KUMWAMBA?
6. Kodi ndi angati amene amakapanga “kagulu ka nkhosa” kameneko?
6 Awo amene amaitanidwa ndi Mulungu kuti akakhale ndi phande mu utumiki wakumwamba woterowo ali owerengeka m’ciwerengero. Monga momwe Yesu ananenera kuti, iwo ali “kagulu ka nkhosa.” Patapita zaka zambiri kucokera pamene Yesu anabwerera kupita kumwamba, Yesu anacibvumbula ciwerengero cenicenico m’masomphenya a kwa mtumwi Yohane, amene analemba kuti: “Ndinapenya, taonani, Mwanawankhosayo ali kuimirira pa phiri la Ziyoni, ndipo pamodzi ndi Iye zikwi zana mphambu makumi anai kudza anai, . . . ogulidwa kucokera kudziko.” (Cibvumbulutso 14:1, 3) Ndithudi, “Mwanawankhosa” amene wachulidwa panoyo ndiye Yesu Kristu; ndipo “phiri la Ziyoni” ili siliri pa dziko lapansi, koma liri kumwamba kumene kuli Yesu. (Yohane 1:29; Ahebri 12:22) Cotero a 144,000 amenewo ali anthu amene amafa pano pa dziko lapansi monga anthu ndipo amaukitsidwira ku moyo wakumwamba monga zolengedwa za mzimu, monga momwe anacitira Yesu. (Aroma 6:5) Pomawayerekeza ndi mamiliyoni zikwi-zikwi a anthu amene amakhala pa dziko lapansi, iwo ndithudi ali “kagulu ka nkhosa.”
7. (a) Kodi a 144,000 ndiwo okha amene adzalandira cipulumutso? (b) Kodi Yesu anawadziwikitsa awo amene adzakhala pa dziko lapansi mwa liu lotani?
7 Komabe, “kagulu ka nkhosa” ka awo amene amapita kumwambawo sindiko awo okha amene adzalandira cipulumutso. Monga momwe taonera, iwo adzakhala akuwalamulira anthu acimwemwe okhala pa dziko lapansi. Yesu anawachula awa kukhala ‘nkhosa zace zina,’ mwa zimene “khamu lalikuru” likutumikira Mulungu mokhulupirika ngakhale tsopanolino.—Yohane 10:16; Cibvumbulutso 7:9, 15.
MMENE MUNTHU AMADZIWIRA NGATI IYE ALI MMODZI WA ‘KAGULU KA NKHOSAKO’
8. Kodi ndi motani mmene munthu amene waitanidwira kumwamba amadziwira?
8 Mamemba a ‘kagulu ka nkhosako’ amadziwa kuti Mulungu wawaitanira iwo kukakhala ndi moyo kumwamba. Motani? Mwanjira ya kagwiridwe ka nchito ka mzimu wa Mulungu, umene umacidzala ndi kucikulitsa mwa iwo ciyembekezo ca kukakhala ndi moyo kumwamba. Mtumwi Paulo, monga mmodzi wa ‘kagulu ka nkhosako’ analemba kuti: “Mzimu yekha acita umboni pamodzi ndi mzimu wathu, kuti tiri ana a Mulungu; ndipo ngati ana, pomweponso olowa nyumba; inde olowa nyumba ace a Mulungu, ndi olowa anzace a Kristu; ngatitu ife timva zowawa pamodzi naye, kuti tikalandirenso ulemerero pamodzi ndi Iye.” (Aroma 8:16, 17) Kagwiridwe ka nchito ka mzimu wa Mulungu kamakasintha kacitidwe konse ka munthu ameneyo, kotero kuti malingaliro ace ndi mapemphero ace amazikidwa pa kumtumikira Mulungu limodzi ndi colinga ca ciyembekezo ca kumwamba. Kukhala limodzi ndi Kristu kumwamba kumakhala kofunika kwambiri kwa iye koposa zinthu zonse za pa dziko lapansi.
9. Munthu asanaupende mkhalidwe wace ponena za moyo wakumwamba, kodi nciani cimene ciri cofunika?
9 Mosakaikira inu munayamba mwailingalira nkhani imeneyi, ndipo mwina mwace inu munadabwa ngati muli mmodzi wa awo amene adzalandira moyo wa kumwamba. Munthu asanaulingalire bwino lomwe mkhalidwe wace wa iye miniyo, iye amafunikira kuti acizindikire cimene Baibulo limaphunzitsa pa nkhani iyi. Cifukwa ninji? Cifukwa cakuti mzimu woyera wa Mulungu umene umapereka umboni wakuti munthuyo waitanidwira ku ulemerero wakumwamba ndiwo mzimu wokhawojkhawo umene unkatsogolera kalembedwe ka Baibulo. Pomakumbukira ici, tiyeni tiupende mkhalidwewo.
10. (a) Kodi ndi cikhulupiriro cotani cimene cingakhale citampangitsa munthu kuyembekezera kupita kumwamba? (b) Kodi ndi coonadi ca Baibulo cotani cimene siciri codziwidwa ndi awo amene amalingalira kuti anthu onse abwino amapita kumwamba?
10 Kalelo kodi munali kukhulupirira kuti anthu onse abwino amapita kumwamba? Ngati kuli conco, ndipo ngati munali kuyesayesa kuti mukhale ndi moyo wabwino, inunso mungakhale mutayembekezera kuti mudzaphatikizidwe pakati pao. Mwa njira iyi inunso mungakhale mutayembekezera za kudzagwirizanitsidwanso ndi okondedwa anu amene anamwalira. Koma pamene munali ndi ciyembekezo cimeneco, kodi munadziwa kuti Baibulo limanena kuti atumiki a Mulungu okhulupirika moterowo monga ngati Mfumu Davide ndiponso Yohane Mbatizi sanakwere kumwamba? (Macitidwe 2:29, 34; Mateyu 11:11) Pa nthawi imeneyo kodi munadziwa kuti 144,000 okha osankhidwa kucokera pakati pa mtundu wa anthu mkati mwa zaka mazana khumi ndi asanu ndi anai zapitazo ndiwo amene adzakhala ndi moyo wakumwamba? Ndipo pamenepo kodi munadziwa kuti Baibulo limakhala ndi ciyembekezo ca moyo wamuyaya m’mikhalidwe yolungama pano pa dziko lapansi kwa ena onse amene amafikira kukhala atumiki okhulupirika a Mulungu?—Salmo 37:10, 11, 29 [36:10, 11, 29, Dy].
11. Kodi ndi cifukwa ca ciphunzitso conyenga cotani ponena za moyo anthu ambiri amalingalira kuti adzapita kumwamba?
11 Pa nthawi imeneyo pamene munali kulingalira za moyo wakumwamba kaamba ka inu mwini, kodi munali kukhulupirira m’kusafa kwa moyo waumunthu? Pamenepo, modziwika bwino, inu mungakhale mutayembekezera kuti moyo wanu udzapita kumwamba. Koma ngati munali ndi ciyembekezo cimeneco sikunali cifukwa cakuti mzimu wa Mulungu unali kupereka umboni kwa inu. Mosiyana ndi cimeneco, monga momwe mukudziwira tsopano, Mau a Mulungu ouziridwa amanena kuti moyo waumunthu umafa ndipo sumakhalaponso. Cotero awo amene amafa ayenera kudalira pa Mulungu kuti awaukitse iwo ndi kuwaika ku malo alionse amene iye amafuna iwo kuti akhalemo.—Ezekieli 18:4; 1 Akorinto 15:35-38.
12. (a) Kodi ndani amene amasankha anthu amene adzalandira moyo wakumwamba? (b) Kodi ndi ku ciyembekezo cotani kumene Mulungu amawasonyezako kwakukurukuru anthu lerolino?
12 Pamenepo, mu nkhani iyi tiyenera kuyang’ana m’Malemba kaamba ka citsogozo ndipo osakulola kutekeseka kwa maganizo, kapena zikhulupiriro zosacirikizidwa m’malemba, kukusokoneza kulingalira kwathu. Awo amene alandira moyo wakumwamba sindiwo anthu amene amadzisankhira okha; Mulungu ndiye amene amasankha. (2 Atesalonika 2:13, 14) Iwo amafunsidwa kuwasiya mamemba okondedwawo a pa banja lao ndi mabwenzi ao ndi zinthu zonse za pa dziko lapansi kaamba ka mwai wa kukhala ndi phande monga mafumu othandizira ndi ansembe ang’ono limodzi ndi Kristu ndiponso monga mbali ya “mkwatibwi” wace. (Cibvumbulutso 21:2) Cimeneco ndico cimene Mulungu waciika patsogolo pao, ndipo iwo amasonyeza ciyamikiro cacikuru kaamba ka ico. Koma sikumafunikira kuti munthu akhale wa kagulu kakumwamba kameneko m’malo mwakuti apeze cimasuko ku mabvuto a moyo uno. Mulungu amazikondanso ‘nkhosa zace zina’ zapadziko lapansi. Iye walonjeza kuti iye adzalipangitsa dziko lapansili kukhala paradaiso, kumene sikudzakhalanso kumva ululu kapena kumva cisoni. Zenizeni zikusonyeza kuti kuli kwakukurukuru ku ciyembekezo ca pa dziko lapansi cimeneco ca moyo kumene Mulungu wakhala akuwatsogozako anthu mu zaka zaposacedwapazi.
13. (a) Kodi ndani amene moyenerera amanyema mkate ndi vinyo pa Cikumbutso ca caka ndi caka ca imfa ya Kristu? (b) Kodi ndaninso amene amakhalapo?
13 Komabe, caka ndi caka, pa cikumbukiro ca imfa ya Kristu, mamemba owerengeka otsalirawo a “kagulu ka nkhosa” amene akali cikhalirebe pa dziko lapansi amacipanga Cikumbukiro ca imfa ya Kristu. Monga momwe Yesu analangizira, iwo amadya mkate wopanda cotupitsa ndi vinyo wofiira, zimene ziri zizindikiro zoimira thupi ndi mwazi zimene Yesu anazipereka amene iye anawalangiza za kudya za zizindikiro izi kuti iye anali kupangana nawo ‘pangano la ufumu’; cotero awo amene sali olowa nyumba a ufumu wakumwambawo samadyako zizindikirozo. (Luka 22:19, 20, 29) Komabe, awo amene amayembekezera ku moyo wapadziko lapansi amasonkhana mu ziwerengero zazikuru caka ndi caka monga apenyereri pa m’gonero wa Ambuye. Monga munthu amene ali wokondweretsedwa kwenikweni ndi moyo m’kulamulira kwa ufumu wa kumwambawo, inunso munayenera kusonkhana nawo.
KUBWERANSO KWA KRISTU
14. Kodi ndi lonjezo lotani limene Yesu analipanga ponena za kubweranso?
14 Pa madzulo a tsiku lotsatizana ndi la kuphedwa kwace Yesu Kristu anawalonjeza mamemba okhulupirika khumi ndi mmodzi a “kagulu ka nkhosa” kuti iye adzabweranso, akumati: “Ndipita kukakukonzerani inu malo. . . . Ndidzabweranso, ndipo ndidzalandira inu kwa ine ndekha; kuti kumene kuli Ineko; mukakhale inunso.”—Yohane 14:2, 3.
15. (a) Kodi nciani cimene Cibvumbulutso 1:7 cimanena ponena za kubweranso kwa Kristu, ndipo kodi ici ciyenera kumvedwa kukhala njira yooneka ndi maso? (b) Kodi ndi motani mmene timadziwira kuti mtundu wonse wa anthu mwacisawawa sudzamuona Kristu pa kubweranso kwace?
15 Kodi uku kukdzakhala kubweranso kooneka ndi maso kwakuthupi? Ena anganene kuti Cibvumbulutso 1:7 cimati: “Taonani, adza ndi mitambo; ndipo diso lirilonse lidzampenya Iye.” Kodi cimeneci cimatanthauza kuti adzamuona iye kwenikweni ndi maso ao akuthupi? Baibulo limalankhula osati kokha za kuona ndi maso anthu akuthupiwa, koma za kuona mu lingaliro lakuti ife timaona kapena kuzindikira ndi maganizo. Yesu anasonyeza kuti Afarisi acipembedzo a m’tsiku lace anali akhungu ngakhale kunali kwakuti iwo anati, “Tipenya.” Iwo anali akhungu mwauzimu. (Yohane 9:39-41; Yesaya 43:8) Kuli kuona mu lingaliro lauzimu limeneli kumene tiyenera kucizindikira Cibvumbulutso 1:7 kukhala cikumanena za iko. “Diso lirilonse” likucititsidwa ‘kumuona’ iye cifukwa cakuti, ngakhale kukhale kwakuti akane kusonyeza cikhulupiriro tsopano, pamene Kristu adzawapha oipa, iwo adzadziwa zimene zikucitikazo cifukwa cakuti auzidwiratu pasadakhale. Komabe, kunena kuti Yesu sadzabwera moonekera ku maso aumunthu iye mwiniyo analongosola momvekera bwino, pakumati: “katsala kanthawi, ndipo dziko lapansi silindionanso Ine; koma inu mundiona; popeza Ine ndiri ndi moyo inunso mudzakhala ndi moyo.” (Yohane 14:19) Mtundu wonse wa anthu sudzamuonanso iye mwacisawawa cifukwa cakuti iye anali kubwerera kumwamba. Koma “kagulu ka nkhosa” kadzamuona iye cifukwa cakuti iye anali kuyembekezera kudzawatenga iwo kuti akakhale naye kumeneko.
16. Pamenepo, kodi nciani cimene kubweranso kwa Kristu kumatanthauza?
16 Cotero kubweranso kwa Kristu sikumatanthauza kuti adzabweranso monga munthu kudzakhala pa dziko lapansi. Koma m’malo mwace, kumatanthauza kuti iye adzaunyamula ulamuliro wace waufumu ndi kumalilamulira dziko lapansi ndi kuti adzawaukitsa a “kagulu ka nkhosa” acewo kucokera kwa akufa kupita kukalandira mfupo yao kumwamba. Kumeneko iwo amakhala ndi phande m’kumacikwaniritsa cifuno cacikondi ca Mulungu mwa njira ya ufumu wace. Inu mukukhala ndi moyo mu nthawi imene nanunso, mungakhale nao madalitso ocokera mu kulamulira kwa Ufumu umenewo.—Cibvumbulutso 11:15-18.