Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • tr mutu 12 tsamba 102-113
  • Ulamuliro Wolungama Udzampangitsa Paradaiso

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ulamuliro Wolungama Udzampangitsa Paradaiso
  • Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • ULAMULIRO WOLUNGAMA
  • KUMASUKA KU UCIMO KUDZETSA THANZI LABWINO NDI MOYO
  • KUWACINGAMIRA ANTHU KUCOKERA KWA AKUFA
  • DZIKO LAPANSI LIBWERERA KU MIKHALIDWE YAUPARADAISO
  • CIYESO COTSIRIZIRA CITSIMIKIZIRA ZA KUYENERA KWA KULANDIRA MOYO WAMUYAYA
  • Pambuyo pa Harmagedo, Dziko Lapansi Laparadaiso
    Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi
  • “Tawonani! Ndikupanga Zinthu Zonse Zatsopano”
    “Tawonani! Ndikupanga Zinthu Zonse Zatsopano”
  • Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?
    Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
  • Cholinga cha Mulungu cha Dziko Lapansili Chikwaniritsidwa Posachedwapa
    Nsanja ya Olonda—2006
Onani Zambiri
Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya
tr mutu 12 tsamba 102-113

Mutu 12

Ulamuliro Wolungama Udzampangitsa Paradaiso

1. (a) Kodi ndi mikhalidwe yotani imene imakusonyeza kufunika kwace kwa kulamulira kolungama pa dziko lonse lapansi? (b) Kodi Mulungu adzalipangitsa dziko lapansi kukhala paradaiso?

HA, ndi motani nanga mmene mtundu wa anthu umakufunira kulamulira kolungama pa dziko lonse lapansi! Aliyense ayenera kubvomereza kuti ciunda ici lerolino siciri paradaiso. Umphawi ndi njala ndizo zimene anthu mamiliyoni ambiri akusauka nazo tsiku ndi tsiku. Mizinda yaikuru yoipa imalicotsera dziko lapansi kukongola kwace kwacilengedwe ndi kuuipitsa mpweya ndi madzi okhala cifupi nayo. Mizinda yomaonjezerekaonjezereka ikufikira kukhala ‘nkhalango’ zaupandu, kumene anthu amacita mantha kucoka panyumba pao pa usiku. Kodi ndi motani mmene kwakhalra kosiyana ndi cifuno coyambiriraco ca Mulungu kaamba ka munthu! Koma kodi ndi motani mmene kwakhalira kwabwino kudziwa kuti Mulungu sanacisiye cifuno caceco! Pakuti iye amatitsimikizira ife kuti: “Momwemo adzakhala mau anga amene aturuka m’kamwa mwanga, sadzabwerera kwa Ine cabe.” (Yesaya 55:11; onaninso Genesis 2:8, 15; 1:28.) Iye adzalipangitsabe dziko lapansi ili kukhala paradaiso waulemerero.

2. Kodi ndi motani mmene tingapulumukire kulowa mu dongosolo latsopano la zinthu?

2 Yehova posacedwapa adzalionongeratu dongosolo lonse loipa ili latsopanoli. Ngati mupeza cibvomerezo ca Yehova tsopanoli, inu mungapatsidwe mwai wa kupulumuka kulowa mu dongosolo latsopano la Mulungu. Kodi ici cidzatanthauzanji kwa inu?

ULAMULIRO WOLUNGAMA

3. Kodi njira ya Mulungu ndi yotani ya kubwezeretsera cilungamo?

3 Cosowa cacikurukuru ca mtundu wa anthu, kwa zaka cifupifupi zikwi zisanu ndi cimodzi, cakhala cakuti mtundu wa anthu ubwezeretsedwenso m’cigwirizano cokwanira ndi Yehova Mulungu, Mlengi wace. (2 Akorinto 5:20) Kuti abwezeretse cilungamo pa ciunda ici Yehova mwiniyo wapanga makonzedwe a “ulamuliro pa mlingo wokwanira wa nthawi yoikidwiratu.” Kulamulira uku kapena ulamuliro uli wocitidwa mwa ufumu wa Kristu. Monga momwe taonera, Ufumuwo wayamba kale kulamulira kumwamba ndipo posacedwapa udzayamba kulamulira mwacikwanekwane pa dziko lapansi. Kodi cifuno cace cacikuru ndi cotani pa kucita ici? “Kuti akasonkhanitsenso limodzi zinthu zonse mwa Kristu, zinthu zakumwamba ndi zinthu za pa dziko lapansi.” (Aefeso 1:9, 10, NW) Kulamulira uku kuli njira ya Mulungu ya kuwapangitsira awo onse amene akukhala ndi moyo pa dziko lapansi kukhala ogwirizana kwenikweni ndikulamulira kwace kwakumwambako. Ici ndico cimene timacipempherera pamene timanena kuti: “Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kucitidwe, monga Kumwamba comweco pansi pano.”—Mateyu 6:10.

4. (a) Kodi ndi masinthidwe otani amene Ufumuwo udzwabweretsa ponena za unansi waumunthu? (b) Kodi ncifukwa ninji sipadzakhalanso nkhondo, ndipo kodi ici cidzatanthauzanji kwa mtundu wa anthu?

4 Kodi ici cidzatanthauzanji ponena za umodzi waumunthu? Adzakhala ogwirizana m’kulambira kwangwiro kwa Atate wao wa kumwamba, anthu a mafuko onse ndi mitundu yonse adzakhalira limodzi monga banja limodzi la abale ndi alongo! (Macitidwe 10:34, 35; 17:26) Pokhala ndi ufumu wa Mulungu womalamuliridwa ndi “Kalonga Wamtendere” waceyo pa dziko lonse lapansi, dziko lapansi silidzagawikananso mwa ndale za dziko. Sipadzakhalanso utundu wonyada kuti udzutsenso cidani, kuombana ndi kukhetsa mwazi. (Yesaya 9:6, 7) Zida zonse zankhondo zakupha zimene zidzatsala Armagedo itatha zidzaonongedwa pasanapite nthawi kosatha. (Ezekieli 39:9, 10; Salmo 46:8, 9 [45:9, 10, Dy]) Cotero sipadzakhalanso mipambo m’manyuzipepa yolengeza za anthu amene abvulazidwa kunkhondo, sipadzakhalanso akazi amasiye cifukwa ca nkhondo kapena ana amasiye cifukwa ca nkhondo, sipadzakhalanso nyumba ndi mizinda imene idzaponyedwa mabomba kufikira kukhala bwinja. Ha, ndi dalitso lalikuru cotani nanga mmene limenelilo lidzakhalira kaamba ka mtundu wa anthu!

5. M’kulamulira kwa Kristu, kodi ncifukwa ninji sipadzakhala cisalungamo?

5 Kucokera ku mpando wace wacifumu wakumwambawo Yesu Kristu adzazitsogolera zocitika za pa dziko lapansi mu njira imene idzadzetsa mapindu osatha. Ndi modabwitsa cotani nanga mmene iye waisonyezera mikhalidwe yace yomuyeneretsayo, ngakhale kumaupereka moyo wacewace kaamba ka ubwino wa awo amene adzakhala nzika zace! Kuonjezerapo, colembedwa ca Baibulo cimasonyeza kuti panalibe cinthu ciriconse-ziyeso, zitsenderezo, citonzo, ngakhale Imfa yeniyeniyo—cimene cikanampatutusa Yesu kusacicita coyenera. Pamenepo, ife tingatsimikizire kuti m’kulamulira kwace sipadzakhala citsenderezo, cisalungamo kapena cibvundi.—Yesaya 11:2-5.

6. Kodi Yesu ali munthu wa khalidwe lotani, kotero kuti ife tinayenera kukhala okondwera pokhala naye iyeyo monga Wolamulira?

6 Kodi simungamuyamikirenso wolamulira amene nthawi zonse amalankhula coonadi? Yesu ali munthu wa mtundu umenewo. (Yohane 1:14; 18:37) Ndipo kodi ndani amene sangakondweretsedwe ndi munthu amene amasonyeza cikondi ceniceni ndi kukondweretsedwa koona mtima mwa ena? Pamene Yesu anali kumayendayenda akumalengeza mbiri yabwino, Baibulo limatiuza ife kuti, iye anaigwiritsira nchito mwaufulu mphamvu imene Mulungu anali atampatsa iye kuwaciritsira odwala, ponse pawiri mwakuthupi ndi mu njira yauzimu. (Mateyu 9:35, 36) Pamene kukanakhala kwabwino kwambiri kukhala ndi moyo mu nthawi imene Yesu anali kutumikira pa dziko lapansi, kukakhala kwabwino kopambana kukhala pa dziko lapansi pamene iye akuigwiritsira nchito mphamvu yace kaamba ka ubwino wa mtundu wonse wa anthu.

7. Kodi anthu amene adzalamulira limodzi ndi Yesu mu ufumu wace wakumwambawo ali a khalidwe lotani?

7 Amene adzagwirizana limodzi ndi Yesu mu ufumu wace wakumwambawo adzakhala mafumu ndi ansembe 144,000 otengedwa pakati pa mtundu wa anthu ndi opangidwa kukhala angwiro ndi Mulungu. (Cibvumbulutso 5:10) Awanso, ali anthu amene amacitsimikizira cikondi cao ca cilungamo mpaka imfa.—Cibvumbulutso 14:1, 4, 5; 2:10.

8. (a) Kodi padzakhala oimira ooneka ndi maso a ufumu wakumwambawo wa Kristu? (b) Kodi ndani amene adzawasankha iwo?

8 Koma kodi boma lakumwamba limeneli lidzakhala ndi oimira alionse a pa dziko ooneka ndi maso? Inde, ndithudi! Eya, ngakhale tsopano ulamuliro wakumwambawo umawasankha amuna okhulupirika monga oimira ace mu mpingo Wacikristu, kumatero mwanjira ya mzimu woyera wa Mulungu. (Yesaya 32:1, 2; Macitidwe 20:28) Cotero tingakhale otsimikizira kuti Kristu adzasamala kuona kuti anthu oyenera pa dziko lapansi amasankhidwa kuliimira boma la Ufumuwo, pakuti pa nthawi imeneyo iye adzakhala akumazitsogolera zocitika za pa dziko lapansi. Cifukwa cakuti amuna awa amaiimira Mfumuyo mu njira yapadera, Baibulo limawacha iwo “akalonga.” Awawo onse adzakhala atakutsimikizira kukhulupirika kwao kwa Mulungu ndi cikondi cao pa anthu anzao. Mzimu wokhawokhawo wa Mulungu umene umaitsogolera Mfumu yao yakumwambayo udzawatsogoleranso iwo.—Salmo 45:16 [44:17, Dy].

9. Kodi kaonekedwe ka khungu lace la munthu kapena malo kumene anabadwirako zidzasonyeza kanthu kalikonse ponena za mmene iye adzacitiridwira?

9 Mtundu, ngakhale kaonekedwe ka khungu, kapena malo obadwerako sizidzatanthauza kanthu kalikonse ponena za njira imene oimira aukalonga amenewa amawagwiritsirira nchito malamulo olungama a Mulungu. (Deuteronomo 10:17; Aroma 2:11) Pomacitsatira citsanzo ca Mfumu yaoyo, “akalonga” amenewa adzatumikira modzicepetsa ndi mwacithandizo, akumacipereka citonthozo kwa anthu anzao. Komabe adzakhala otsimikizira pa kumacicirikiza cilungamo ca Mulungu.—Mateyu 11:29; 20:25-28.

10. Mosiyanitsa ndi kupanda cisungiko ndi mantha amene ali ofala kwambiri lerolino, kodi mikhalidwe idzakhala yotani m’kulamulira kolungama kwa Kristu?

10 Dziko lapansi pokhala litacotsedwera ocita zoipa onse, upandu sudzaloledwa kuti uzike mizu kaciwirinso. (Salmo 37:9-11 [36:9-11, Dy]) Sipadzakhalanso kufunikira kwa apolisi, ndende, maunyolo, macenjezo a akuba, mabokosi osungira ndalama azitsulo, maloko ndi makii. M’kulamulira kolungama kwa ufumuwo, inu mudzadziwa kuti aliyense amene akugogoda pa citseko canu ndi bwenzi lanu. Sipadzakhala konse kuopa kubvulazidwa mwa njira iriyonse. Sipadzakhalanso kuopa kubvulazidwa mwa njira iriyonse. Sipadzakhalanso kuopa kwa kumayenda m’munda wa maluwa usiku ndi kumalipenya thambo lodzaza ndi nyenyezi limene liri nchito ya manja a Mlengiyo. Monga momwe kwakhalira koona ndi mpingo wa Mulungu lerolino mu njira yauzimu, kuli cimodzimodzinso mu njira yeniyeni, “adzakhala osatekeseka, opanda wina wakuwaopsa.”—Ezekieli 34:28.

KUMASUKA KU UCIMO KUDZETSA THANZI LABWINO NDI MOYO

11. Kuonjezera pa kumatumikira monga mafumu, kodi ndi m’malo ena ati mamemba a boma lakumwamba la Kristu adzatumikiramo? Cifukwa ninji?

11 Programu yoyambirira ya ufumuwo idzakhala ya nyengo ya zaka cikwi. Mkati mwa nthawi imeneyo Yesu Kristu ndi mamemba a boma lace lakumwamba adzatumikira osati kokha monga mafumu komanso monga ansembe a Mulungu kaamba ka ubwino wa nzika zao zonse zaumunthu. (Cibvumbulutso 20:6) Cifukwa ninji? Cifukwa cakuti anthu onse pa dziko lapansi adzafunikira “kumasulidwa ku ukapolo wa cibvundi” m’malo mwakuti akhale ndi “ulemerero waufulu wa ana a Mulungu.” (Aroma 8:21, NW) Ngakhale oipa ataonongedwa, opulumuka a pa dziko lapansi adzakhalabe opanda ungwiro cifukwa ca ucimo wa colowa kucokera kwa Adamu. Zikhumbo zolakwa za thupi lao lopanda ungwirolo zidzakhalabe zikumamenyana nkhondo ndi zikhumbo zao zoyenera za maganizo ndi mtima. (Aroma 7:21-23) Cotero, kuti alandiridwe mokwanira m’banja la ana a Mulungu, iwo coyambirira afunikira kukhala ndi mautumiki a ansembe akumwambawo a Mulungu. Kodi nciani cimene amenewawo adzacicita?

12. (a ) Kodi ndi mphamvu yaikurukuru yotani imene mamemba a ufumu wakumwamba wa Kristu adzakhala nayo? (b) Kodi anthu adzaufikira mkhalidwe wodalitsika wotani?

12 Iwo adzakhala ndi mphamvu imene yakhala ikusoweka m’maboma aumunthu kufikira pa tsopano lino: mphamvu ya kumacotsera anthu ucimo ndi kupanda ungwiro. Mphamvu imeneyi iri ndi ansembe akumwamba a Mulungu mwa njira ya nsembe ya dipo ya Yesu. Mwana wa Mulungu limodzi ndi ansembe ogwirizana naye pa nthawi imeneyo adzagwiritsira ntchito mapindu a nsembe ya Yesu mwacindunji kwa omvera onse. (Yohane 1:29; 1 Yohane 2:2) Makonzedwe amenewa akuphiphiritsiridwa m’Baibulo ndi “mtsinje wa madzi a moyo” wophiphiritsira umene umayenda tawatawa kucokera “kumpando wacifumu wa Mulungu ndi wa Mwanawankhosa” ndipo “masamba a mtengo ndiwo akuciritsa nawo amitundu.” (Cibvumbulutso 22:1, 2) Mwa kumakupanga kupita patsogolo kosalekeza m’cilungamo limodzi ndi cithandizo ca unsembe wakumwambawo, iwo mosalekeza adzakhalabe acinyamata ndi anyonga, kufikira adzaufikira ungwiro wa thanzi m’maganizo ndi m’thupi. Iwo adzamasulidwa kotheratu ku ukapolo wa ucimo ndi imfa zolowedwa mwa colowa kucokera kwa Adamu.—Yohane 11:26.

13. (a) Kodi ndi motani mmene Cibvumbulutso 21:4 cimawalongosolera madalitso amene Ufumuwo udzawabweretsa? (b) Kodi Yesu anacitanji pamene anali pa dziko lapansi cimene cimasonyeza kuti iye angawabweretse madalitso amenewa?

13 Inde, mwa njira iyi, Mulungu “adzawapukutira misozi yonse kuicotsa pamaso pao; ndipo sipadzakhlanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena cowawitsa; zoyambazo zapita.” (Cibvumbulutso 21:4) Ha, ndi kozizwitsa cotani mmene kudzakhalira kusangalala ndi thanzi langwiro! Monga momwe Mwana wa Mulungu anawaciritsira akhate ndi kuciritsa opunduka ndi akhungu pamene anali pa dziko lapansi cotero kulamulira kwace kolungama kudzadzetsa mapeto a matenda onse ndi kubvutika. (Marko 1:40-42; Yohane 5:9; Mateyu 9:35) Kumene kudzakhala kutatha ndiko kufunika kwa zipatala ndi insuransi ya thanzi! Pokhala kuti matenda ndi imfa zidzakhala zitacotsedwa, codzetsa kulira ca pa dziko lonse cidzacotsedwanso. (1 Akorinto 15:25, 26) Ha, ndi kodabwitsa cotani nanga mmene kudzakhalira kusangalala ndi ufulu wokwanira kumasuka kotheratu ku ucimo, ndi kukhala okhoza kuufikira mlingo wolungama waungwiro wa Mulungu mu kulankhula, kuganizira ndi khalidwe!

KUWACINGAMIRA ANTHU KUCOKERA KWA AKUFA

14. Kodi ndi ciyembekezo cotani ca akufa cimene Yesu anacibvumbula pa Yohane 5:28, 29?

14 Palinso ciyembekezo cacimwemwe cakuti okondedwa anu amene amwalira adzakhala okhoza kusangalala ndi madalitso a kulamulira kolungama kwa Mwana wa Mulungu pa dziko lapansi. Yesu anacibvumbula ciyembekezo ca mamiliyoni osawerengeka a anthu amene ali akufa, akumati: “Musazizwe ndi ici, kuti ikudza nthawi, imene onse ali m’manda adzamva mau ace, nadzaturukira.” (Yohane 5:28, 29) Kodi ndi nthawi ya cisangalalo copatsa nthumanzi yotani nanga mmene iyo idzakhalira pamene coyamba mbiri idzafalitsidwa pa dziko lonse lapansi yakuti: “Akufa akuukitsidwa!”

15.Ncifukwa ninji tingakhale ndi citsimikiziro cakuti Yesu adzawaukitsa akufa?

15 Ife tiri ndi citsimikiziro cokwanira cakuti zimenezi zidzacitikadi. Muzikumbukira kuti, pamene anali pa dziko lapansi, Yesu sanangociritsa kokha odwala ndi opunduka; iyenso anawaukitsanso anthu akufa. (Mateyu 11:2-6) Ici cinaisonyeza mphamvu yodabwitsa ya Mulungu ya kuukitsa akufa, mphamvu imene waipereka kwa Yesu Kristu. Kapena mukucikumbukira cocitika ca pa nthawi imene Yesu anafika pa nyumba ya munthu amene mtsikana wace wa zaka khumi ndi ziwiri anali atamwalira. Polankhula ndi mtsikanayo, Yesu anati: “Buthu, ndinena ndi iwe, Uka.” Kodi cimene cinatsatirapo nciani? Baibulo limatiuza ife kuti: “Pomwepo buthulo linauka, niliyenda.” Kodi ndi motani mmene makolo limodzi ndi apenyereri enawo anacitira pakuona cozizwitsa ici? “Ndipo anadabwa pomwepo ndi kudabwa kwakukuru.” Cimwemwe cao cinali cosefukira.—Marko 5:35, 38-42; onaninso Yohane 11:38-44; Luka 7:11-16.

16. Kodi ndani amene adzaukitsidwa kucokera kwa akufa, ndipo kodi ndi motani mmene icico cidzawayambukirira amoyo?

16 Pamene paradaiso abweretsedwanso ku dziko lapansi, Yesu kaciwirinso adzaigwiritsira nchito mphamvu yace kuwaukitsa akufa. Pakuti Baibulo limatitsimikizira ife kuti “kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama.” (Macitidwe 24:15) Kodi ndi cisangalalo cotani nanga mmene cidzakhalira pa dziko lonse lapansi pamene magulu otsatizanatsatizana adzakhala akumaukitsidwira ku moyo! Tangocilingalirani cimwemwe ca kuwaonanso acibale okondedwa cimene cidzakhalapo! M’malo mwa kumakhalapo mipambo ya cilengezo ca akufa, pangadzakhale zilengezo za oukitsidwa catsopano ndi kumacibweretsa cisangalalo kwa okondedwa ao.

17. Kodi ncifukwa ninji siciri cothetsa nzeru kwa Mulungu kuwakumbukira awo onse amene ayenera kuukitsidwa?

17 Mamiliyoni ambiri a anthu ali akufa, koma cimeneco sicimacipereka cothetsa nzeru kwa Mulungu. Iye angawakumbukire iwo onse. Eya, Baibulo limatiuza ife kuti Mulungu “awerenga nyenyezi momwe ziri; azicha maina zonsezi.” (Salmo 147:4 [146:4, Dy]) Talingalirani za cimene cimeneco cimatanthauza. Kukunenedwa kuti kuli milalang’amba mamiliyoni mazana ambiri, mlalang’amba uliwonse womakhala ndi mamiliyoni mazana ambiri, mlalang’amba uliwonse womakhala ndi mamiliyoni mazana ambiri a nyenyezi, ndipo komabe Mulungu amaidziwa nyenyezi iriyonse mwa dzina lace. Ciwerengero ca anthu onse amene anakhalapo ndi moyo ciri cacing’ono mwa kuyerekezera. Cotero sikudzakhala kobvuta kwa Mulungu kuwakumbukira onse amene anafa ndi amene amapindula ndi dipo la Kristu. (Mateyu 19:26) Iwo adzabwezeretsedwanso ku moyo pompano pa dziko lapansi. Kodi udzakhala mwai wopatsa nthumanzi cotani nanga kukhalapo pa nthawi imeneyo ndi kuwacingamira kucokera kwa akufa!

18. M’ciukiliro, kodi inu mudzakhala wokhoza kuwazindikira awo amene munawadziwa kale? Cifukwa ninji?

18 Pamene iwo adzauka kodi iwo adzakhala anthu amodzimodziwo? Kodi ife tidzawadziwa iwo? Inde! Ngakhale munthu angazisunge zithunzithunzi ndi mau kosatha pa makina otengera mau kuti adzazigwiritsire nchito pambuyo pace pa wailesi ya kanema. Mulungu angacite zoposa pamenepo. Pa nthawi ya ciukiliro iye angampatse aliyense thupi loyenera, monga momwe iye anacitira pa kumlenga munthu woyambayo, ndi kuwaikanso mu ubongo wace maganizo enieniwo a zinthu zonse zimene munthuyo anali ataziphunzira ndi kuzidziwa mkati mwa nthawi ya moyo wace wapapitapo. Motero m’ciukiliro munthu ameneyo adzauka ali ndi umunthu wokhawokhawo umene anali nao pa imfa, monga momwe Yesu woukitsidwayo anausungira umunthu wace. (Ahebri 13:8) Inu mudzawazindikira awo amene munawadziwa poyamba. Ha, ndi ciyembekezo codabwitsa cotani nanga!—Yobu 14:13-15.

19. Kodi bukhu la Cibvumbulutso limasonyezanji ponena za akufa? Cotero nanga ndi ciani cimene cidzacokeratu?

19 Mtumwi Yohane anapatsidwa masomphenya a zinthu zodzutsa mtima izi zimene zidzacitika mkati mwa kulamulira kwa Kristu, ndipo akupezeka m’bukhu la Cibvumbulutso. Masomphenya ace amasonyeza kuti imfa ndi Hade (manda wamba a mtundu wa anthu) ‘adzapereka akufa ao amene ali mwa iwo.’ Palibe aliyense amene adzatsala m’menemo. Pamenepo imfa yocititsidwa cifukwa ca ucimo wa colowa idzakhala itatheratu kosatha. (Cibvumbulutso 20:13, 14; Yesaya 25:8) Amene adzakhala atatha ndiwo malo olinganiza za maliro limodzi ndi miyala yoika pa manda! Sipadzakhalanso manda amene adzatsala kukaononga kaonekedwe ka dziko lapansi lauparadaiso kokongolako.

20. (a) Kodi ndi mwai wotani umene udzatsegulidwira kwa oukitsidwawo, ndipo kodi adzafunikira kucitanji? (b) Kodi iwo adzaweruzidwa pa maziko otani? (c) Kodi ndi motani mmene masinthidwe adzacitikira kwa anthu amene poyambapo anali oopsya?

20 Awo amene adzaukitsidwera ku moyo pa dziko lapansi adzauka kulowa m’mwai wa kuupeza moyo wamuyaya mu paradaiso. Idzakhala nthawi yao yakuphunzira. “Mabuku” okhala ndi cilangizo cocokera kwa Mulungu adzatsegulidwa, ndipo iwo adzafunikira kuwatsatira amenewa m’kuwasanduliza maganizo ao kuti akhale ogwirizana ndi cifuniro ca Mulungu. Iwo adzaweruzidwa “yense monga mwa nchito zace”; ndiko kunena kuti, nchito zimene adzazicita ataukitsidwa ndipo ataphunzira kale za mkati mwa “mabuku” amenewo. (Cibvumbulutso 20:11-13) Mwa kumacita mogwirizana ndi maphunziro amene adzaperekedwawo, ngakhale awo amene pa nthawi yina anali oopsa monga ngati cirombo cakuchire adzasintha macitidwe ao, monga momwe ambiri acitira atagwirizana ndi mpingo Wacikristu. —Yesaya 11:9; 26:9; 35:8, 9.

DZIKO LAPANSI LIBWERERA KU MIKHALIDWE YAUPARADAISO

21. Kodi ndi dalitso lotani la kulamulira kwa Ufumuwo limene likulongosoledwa pa Yesaya 25:6?

21 Kuongokera m’cilungamo kudzadzetsanso mapindu a zinthu zakuthupi. Padzakhala kukwaniritsidwa kwenikweni kwa mau olosera a Yesaya 25:6: “Ndipo m’phiri limeneli Yehova wamakamu adzakonzera anthu ace phwando la zinthu zonona.” Palibe munthu aliyense ku nthawi iriyonse amene adzaudziwa ululu wa kudwala ndi kufooka cifukwa ca kusowa cakudya. Koma kodi ndi motani mmene Mulungu adzaliperekera phwando limeneli?

22. (a) Monga momwe kwasonyezedwera m’Baibulo, kodi ndi motani mmene zocuruka za zinthu zakuthupi zimenezi zidzaperekedwera? (b) Kodi dziko lonse lapansili lidzasinthidwera ku mkhalidwe wotani?

22 Pamene Aisrayeli anali anthu osankhidwa ndi Mulungu, dalitso lace linawapatsa iwo kulemerera kwakukuru. Minda inali kubala mbeu zabwino. Mitengo yao ya zipatso inali kubereka zipatso zabwino kopambana. Yehova anawatsegulira iwo “Cuma cace cokoma, ndico thambo lakumwamba, kupatsa dziko lanu [lao] mvula m’nyengo yace.” (Deuteronomo 28:12; onaninso vesi 8.) Madalitso ofananawo adzapezekanso mwacikwanekwane m’kulamulira kwa ufumu wa Kristu. (Salmo 67:6, 7 [66:7, 8, Dy]) Nzika za pa dziko lapansi za Ufumuwo zidzalikwaniritsa lamulo limene Adamu ndi Hava sanalikwaniritse. Iwo ‘adzaligonjetsa’ dziko lapansi, akumalipangitsa dziko lonse kukhala paradaiso. Kunali ponena za ciyembekezo cimeneco, limodzi ndi kumalingaliranso za ciyembekezo ca ciukiliro, cakuti Yesu anamuuza wocita zoipa womvera cifundo uja amene anapacikidwira naye limodzi kuti: “Zoonadi ndikuuza iwe lero, Udzakhala ndi ine m’Paradaiso.”—Luka 23:39-43, NW.

23. Kodi ndi motani mmene Salmo limalongosolera za mkhalidwe wacimwemwe umene udzakhalapo pa dziko lapansi?

23 Pamenepo dziko lonse lapansi lidzasonyeza cimwemwe. Kudzakhala monga ngati kuti zigwa zace ndi mapiri, mitengo yace ndi maluwa, mitsinje yace ndi nyanja, zonsezo zikumasangalala nako kulamulira kolungama kwa Yehova. (Salmo 96:11-13 [95:11-13, Dy]; 98:7-9 [97:7-9, Dy]) Mpweya wabwino sudzaipitsidwanso konse. Mtsinje ndi khwawa lirilonse mudzayenda madzi abwino, osaipitsidwa. Sipadzakhalanso kuipitsidwa kwa dziko.

24. Kodi nciani cimene kulamulira kwa Kristu kudzaucitira mtundu wa anthu ponena za zinyama?

24 Dziko lonse lapansi—nkhalango zace, minda yace, mapiri ace—zonsezo zidzakhala munda umodzi wokongola, wokometseredwa ndi nyama za mitundu yosiyanasiyana ndi mbalame. Izinso, zidzakumvera kulamulira kwanzeru kwa Mwana wa Yehovayo. Ndipo “m’dziko lonse lapansi lokhalidwa ndi anthu” limene likudzalo iye adzazipangitsa zonsezo kulowa m’kumalamuliridwa ndi mtundu wa anthu mopanda cibvulazo.—Ahebri 2:5-8; Salmo 8:4-8, NW [8:5-9, Dy].

CIYESO COTSIRIZIRA CITSIMIKIZIRA ZA KUYENERA KWA KULANDIRA MOYO WAMUYAYA

25. (a) Pakutha pa zaka cikwi zoyambazo, kodi Ufumuwo udzakhala utacitanji? (b) Pamenepo kodi ndi ciyeso cotani cimene cidzacitika, ndipo ncifukwa ninji?

25 Ufumu wa Mulungu wocitidwa ndi Kristu udzalamulira kwamuyaya. Komabe, cakumapeto kwa zaka cikwi coyambiriraco pa dziko lapansi. Uwo udzakhala utacicotsa cisalungamo ca mtundu uliwonse. Mtundu wonse wa anthu pa dziko lapansi udzakhala monga zolengedwa zangwiro pamaso pa mpando wacifumu wa Woweruza Wamkuruyo, Yehova Mulungu. Mwa njira iriyonse iwo adzakhala ofanana ndi anthu oyambirira angwiro aja mu Edene. (1 Akorinto 15:24) Kodi iwo adzakhala oyenerera kuti nzika za Ufumuwo ziyesedwe ponena za kudzipereka kwao ku kulamulira kolungamako kwa Mulungu. Yehova adzawapatsa iwo mwai wakuti asonyeze kukhulupirika kwao. Motani? Mwa kummasula Satana limodzi ndi ziwanda zace kucokera ku undende wao ‘m’phompho.’ (Cibvumbulutso 20:7) Mwa ciyeso ici aliyense wokhala m’banja la Mulungu la pa dziko lapansi aliyense payekha angakhale ndi mwai wa kulipereka yankho la iye mwini lonena za citokoso cimene cinaperekedwa kwa Atate wao wakumwambayo ndi Satana.

26. Kodi nciani cimene cidzakhala coturukapo ca (a) awo amene adzakhala okhulupirika kwa Mulungu? (b) awo amene adzamtembenukira Mulungu? (c) Satana ndi ziwanda zace?

26 Awo amene adzakhala okhulupirika kwa Mulungu adzaweruzidwa kukhala oyenera kukhala ndi moyo wosatha. Yehova adzakupereka kuyenera kumeneku kwa iwo, akumawalemba maina ao ”m’bukhu la moyo.” Aliyense amene mopanduka adzamtembenukira Mulungu adzaonongedwa mu “imfa yaciwiri.” Pamenepo, Satana Mdierekezi, limodzi ndi ziwanda zace, adzaonongedwa kosatha. (Cibvumbulutso 20:7-10, 15) Ku nthawi yonse, sikudzacitikanso kuti dziko lapansili, kapena mbali iriyonse ya chilengedwe caponseponse cacikurukuruci ca Mulungu, lidzadodometsedwanso ndi ucimo ndi cipanduko. Pokhala lidzakhala litapangidwa kukhala paradaiso kumene cilungamo cidzakhalako, kwa nthawi yonse imene ikudzayo dziko lapansili lidzakhala monga ngati malo a mtengo wapatali otamanda dzina la Yehova.

27. Ngati ife tiufunadi moyo m’dziko lapansi lauparadaisolo, kodi tiyenera kucitanji tsopano?

27 Kodi cifuno ca Mulungu ca kukupereka kulamulira kolungama pa dziko lapansi lauparadaiso cimakupangitsani inu kuciyamikira kwakukuru cilungamo cace? Kodi ico cimaonjezera mwa inu kuzindikira za nzeru yace? Kodi ico cimakusonkhezereni inu kucisonyeza cikondi canu kaamba ka iye? Ngati ndi conco, pamenepo muyenera kucita zonse zimene mungathe kuzicita tsopanolino kuti muzimtumikira iye mwa mtima wonse. Khalani ndi phande m’kumawauza ena za dzina ndi cifuno ca Yehova. (Salmo 89:14-16 [88:15-17, Dy]; 1 Yohane 4:19) Tsopano muzikhala ndi moyo mogwirizana ndi maprinsipulo olungama a Yehova, ndipo muzikonzekera kaamba ka moyo wamuyaya m’dziko lapansi lauparadaiso m’kulamulira kolungama kwa Ufumuwo.

[Chithunzi patsamba 108]

Ngakhale akufa anaukitsidwa ndi Yesu nakhala ndi moyo

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena