Mutu 13
Carici Coona ndi Maziko Ace
1. Kodi ncifukwa ninji kuli kofunika kucizindikira carici coona ndi maziko ace?
NGATI tifuna kukhala ndi moyo kwamuyaya mu dongosolo latsopano la Mulungu ife tiyenera kucizindikira carici coona ndi maziko ace. Ponena za zinthu ziwiri izi, Yesu anati: “Pa thanthwe ili ndidzamangapo Carici canga.” (Mateyu 16:18, Dy) Kodi carici cimeneci nciti ndipo kodi ndi ciani cimene ciri thanthwe pa limene ico cikumangidwapo? Baibulo limatipatsa ife mayankho oyenera.
2. (a) Kodi Baibulo nthawi iriyonse limagwiritsira nchito liu lakuti “carici” kumatanthauza nyumba? (b) Kodi tanthauzo la liu Lacigrikilo ndi lotani?
2 Pamene kuli kwakuti anthu ambiri amalankhula za nyumba mu zimene anthu amakumaniramo kudzalambira kukhala “macarici,” Kodi munayamba mwadziwa kuti Baibulo silitero konse? M’Baibulo liu lakuti “carici” nthawi zonse limanena za anthu, makamaka msonkhano kapena gulu la anthu. (Filemoni 2) Liu Lacigriki lakuti ek·kle·siʹa, limene latembenuzidwa kukhala “carici” capena “mpingo,” limatanthauza kwenikweni “cija cimene caitanidwa.” Ilo limatanthauza za gulu la anthu oitanidwa pakati pa ena kaamba ka cifuno cakuti-cakuti; koma ilo likugwiritsiridwa nchito monga liu lofanana ndi liu Lacihebri lakuti qahalʹ, kumatanthauza “mpingo” kapena “msonkhano.”
3. Kodi ncifukwa ninji carici coonaco cikuyerekezedwa ndi (a) thupi la munthu? (b) namwali wotomeredwa?
3 Carici coona kapena mpingo cikufaniziridwa ndi thupi la munthu, cifukwa cakuti ciri ndi ziwalo zambiri koma mutu umodzi, monga momwe thupi la munthu lakhalira. Malemba ouziridwa, pa Aefeso 1:22, 23 (Dy), pamatiuza ife kuti Mulungu anampangitsa Kristu kukhala ‘mutu wa carici conse, cimene ciri thupi lace,’ Carici ici cikuyerekezedwanso ndi namwali wosakhudzidwa wotomeredwa ndi Kristu, cifukwa cakuti monga kagulu ziwalo za mu carici coonaco ziri zogwirizana kotheratu ndi Kristu, monga momwe mkazi amagwirizanirana ndi mwamuna wace. Pomazilembera ziwalo zina za caricico, mtumwi Paulo anati: “Ndinakupalitsani namwali woyera mtima kwa Kristu.” (2 Akorinto 11:2; onaninso Cibvumbulutso 21:2, 9, 10.) Cotero uwo uli mpingo woyera, wopanda cibvundi ca dziko ndipo uli wodzipereka kwa Mutu wace, Yesu Kristu.
4. (a) Kodi aliyense ‘angagwirizane’ ndi carici coonaco mwa kumalipangitsa dzina lace kulembedwa pa ndandanda yolemberapo maina ya pa dziko lapansi? Cifukwa ninji? (b) Kodi ndi angati amene amacipanga carici coonaco cimene cidzakhala limodzi ndi Kristu kumwamba?
4 Kodi aliyense wa ife angasankhe za “kugwirizana” ndi carici cimeneci mwa kumangolipangitsa dzina lace kulembedwa pa ndandanda ya mamemba pano pa dziko lapansi? Ai; monga momwe Ahebri 12:23 (Dy) amalongosolera, ici ndico “carici ca oyamba kubadwa amene alembedwa m’mwamba.” Mulungu ndiye amene amazisankha ziwalozo. Iye amazikhazikitsa izo mumpingo monga momwe iye amafunira. (1 Akorinto 12:18) Awa ndiwo amene adzakhala limodzi ndi Kristuyo kumwamba. Ndipo Yesu anabvumbula kuti, m’malo mwakuti aphatikizemo onse amene amadzisonyeza kukhala Akristu, ciwerengero cao ciri colekezera pa 144,000.—Cibvumbulutso 14:1-3; Luka 12:32.
5. Kodi ndi kaamba ka cifuno capadera cotani ziwalo za carici coonaco zimaitanidwa?
5 Ndithudi, iwo ali kagulu ka anthu amene aitanidwa kucoka mu mdima wauzimu kaamba ka cifuno capadera. Pamene akali pano pa dziko lapansi iwo molimbika amalalikira “zoposazo” za Mulungu wam’mwambamwambayo, amene anawaturutsa mumdima kulowa m’kuwala kwace kodabwitsa. (1 Petro 2:9) Ndipo, pambuyo pa ciukiliro cao, iwo adzakhala ndi mwai waukuru wa kulamulira limodzi ndi Kristu mu ufumu wace wakumwamba.—Luka 22:28-30.
6. (a) Kodi ziwalo zoyambirira za carici coonaco zinali yani, ndipo kodi ndi motani mmene umboni unaperekedwa kwa iwo wakuti iwo anali ana a Mulungu auzimu? (b) Kodi ndi liti pamene mwai wa kukhala ziwalowo unawatsegukira awo osakhala Ayuda?
6 Ziwalo zoyambirira za carici coona cimeneci zonse zinali Zaciyuda (monga momwe anakhalira Yesu limodzi ndi atumwi ace) kapena atembenuki odulidwa Aciyuda. Pa Pentekoste wa mu 33 C.E.—patangopita masiku khumi Yesu atakwera kumwamba ndi kuitsegula njira yakuti ena amtsatire iye mu nthawi yace—Yehova anakusonyeza kusankha kwace kwa mamemba amenewa mwa kutsanulidwa kwa mzimu woyera. Kulandira kwao mzimu pa cocitika cimene cija kunapereka umboni kwa iwo wakuti iwo tsopano anali ana auzimu a Mulungu ndi olowa nyumba a ufumuwo limodzi ndi Kristu. (Macitidwe 2:1-4, 16-21, 33; Aroma 8:16, 17) Koma ziwalo za carici coonaco sizinangokhala Zaciyuda zokhazokha. Patapita zaka zitatu ndi theka kucokera pa nthawi imene Yesu anafa njira inatsegulidwa kaamba ka akunja kapena osakhala Ayuda kuti aphatikizidwemo. (Macitidwe 10:30-33, 44; Aroma 9:23, 24) Cotero, m’kupita kwa nthawi, carici coonaco cinafikira pa kukhala ndi ziwalo zocokera m’mitundu yonse.
MAZIKO A CARICI COONACO
7. Kodi ndi motani mmene Yesu limodzi ndi mtumwi Paulo amaudziwikitsira mwala wapangondya wamaziko wa carici coona?
7 Kodi ndani amene ali maziko a carici coonaco? Yesu Kristu analongosola momvekera bwino kuti iye mwiniyo ndiye maziko amenewo. Iye anautanthauzira kukhala ukumanena za iye mwiniyo ulosi wa pa Salmo 118:22 [117:22, Dy] akumati: “Mwala umene anaukana omanga nyumba womwewu unakhala mutu wapangondya.” (Mateyu 21:42-44) Mtumwi Paulo amaonjezerapo umboni wace wakuti Yesu ndiye “mutu wapangondya,” pa kuwalembera Akristu a pa Efeso kuti: “Inu muli nzika zinzao za oyera mtimawo ndi apabanja la Mulungu, omangidwa pa maziko a atumwiwo ndi aneneri, Yesu Kristu mwiniyo akumakhala mwala waukuru wapangondya.” (Aefeso 2:19, 20, Dy) Mtumwiyo anali wotsimikizira kwambiri ponena za ici, akumanenanso kaciwiri kuti: “Palibe munthu wina angaike maziko ena, koma aja amene aikidwa kale: amene ali Kristu Yesu.”—1 Akorinto 3:11, Dy.
8. (a) Kodi ncifukwa ninji sipakadakhalapo maziko ena abwino koposa Kristu Yesu? (b) Kodi ndi funso lotani limene tsopano limabuka?
8 Sipangakhale maziko ena abwino kwambiri ndi otsimikizirika kwambiri a carici coonaco koposa Kristu Yesu, kodi angakhalepo? Uli moyo wace wa iye mwiniyo waumunthu wangwiro umene unaperekedwa monga dipo umene umawapangitsa kukhala othekera makonzedwe aumulungu amenewa. Komabe, kodi ndi motani mmene tingaupangitsire umboni umenewu woperekedwa ndi Yesu ndi mtumwi Paulo kugwirizana ndi zimene Yesu anazinena kwa Petro pa Mateyu 16:18? Ife tingakhale otsimikizira kuti palibe kuombana.
‘PA THANTHWE ILI NDIDZAMANGAPO CARICI CANGA’
9. (a) Kodi ndi motani mmene anthu ena amawamvera mau a Yesu a pa Mateyu 16:18? (b) Kodi ambiri a “azibambo” a carici oyambirira anawamva mau a Yesu onena za “thanthwe” monga kukhala akumanena za Petro?
9 Petro anali atangombvomereza Yesu kukhala Kristuyo (kapena, Mesiya), Mwana wa Mulungu wamoyo. Pamenepo Yesu anati: ‘Ndinena kwa iwe: Iwe ndiwe Petro, pa thanthwe ili ndidzamangapo Carici canga.’ (Dy) Ena amawamva mau amenewa kukhala akumatanthauza kuti carici ca Yesu cikumangidwa pa Petro monga maziko. Aka ndiko kalingaliridwe kaukumu ka Carici Caciroma Katolika. Koma kuli kokondweretsa kuona kuti Archibishipo Kenrick, m’buku lakuti An Inside View of the Vatican Council (1870), limasonyeza kuti mwa “azibambo” a carici oyambirirawo okwanira makumi asanu ndi atatu kudza asanu ndi mmodzi, anali khumi ndi asanu ndi awiri okha amene anawaganizira mau a Yesu onena za “thanthwe” kukhala akumatanthauza Petro. Kodi munacidziwa ici?
10. Kodi ndi motani mmene Augustine anawamvera mau a Yesu onena za “thanthwe”?
10 Mwacitsanzo, talilingalirani lingaliro la Augustine (354-430 C.E.), amene kawirikawiri amachedwa “Augustine Woyera.” Ngakhale kunali kwakuti pa nthawi yina anali kumlingalira Petro kukhala “thanthwe,” mtsogolo mwace Augustine anakasintha kalingaliridwe kaceko, akumanena mu bukhu lace lakuti Retractationes (Kusintha): “Ndakhala ndikunena kawirikawiri kuti mau a Ambuye wathu akuti: ‘Iwe ndiwe Petro ndipo pa thanthwe ili ndidzamangapo Carici canga,’ ayenera kumvedwa kukhala akumanena za uyo amene Petroyo anambvomereza pamene iye anati: ‘Inu ndinu Kristu Mwana wa Mulungu wamoyo,’ . . . Pakuti [Petro] sanauzidwe kuti ‘Iwe ndiwe thanthwelo, koma ‘Iwe ndiwe Petro.’ Koma thanthwelo linali Kristu.”
11. Kodi ndani amene Petro miniyo anamdziwa kukhala “thanthwe”?
11 Koma cofunika kwambiri ndico cakuti—kodi ndi motani mmene Petro mwiniyo anawamvera mau a Yesuwo? Ponena za Ambuye Yesu, Petro anati: “Mwa iye wakudzayo, monga ku mwala wamoyo, wokanidwadi ndi anthu koma wosankhidwa ndi wolekezedwa ndi Mulungu: Nanunso mukhale miyala yamoyo yomangidwa, nyumba yauzimu, unsembe woyera, kupereka nsembe zauzimu, zolandirika kwa Mulungu mwa Yesu Kristu. Cifukwa cacimeneco kwanenedwa m’lemba: Onani, ndiika m’Sioni mwala waukuru wapangondya, wosankhika, wamtengo wapatali. Ndipo iye amene adzakhulupirira mwa iye sadzanyazitsidwa. Cifukwa ca cimeneco kwa inu akukhulupirira, iye ndiye wolemekezeka: koma kwa iwo osakhulupirira, mwala umene omangawo anaukana, womwewo wapangidwa kukhala mutu wapangondya: mwala wokhumudwitsa ndi thanthwe lophunthwitsa, kwa iwo akukhumudwa nawo mauwo.” (1 Petro 2:4-8, Dy) Mau awa a Petro amasonyeza kuti iye, mofanana ndi mtumwi Paulo, anamzindikira Yesu kukhala ‘mwala waukuru wapangondya,’ “thanthwe” pa limene caricico cikumangidwapo. Petro wangokhala kokha mmodzi wa “miyala yamoyo” 144,000 imene ikucipanga carici coonaco.
12. (a) Kodi ndi motani mmene tikudziwira ngati Petro anali mtsogoleri “wosacimwa” wa carici coyambiriraco? (b) Kodi ndani nthawi zonse amene amakhala mutu wa carici coonaco?
12 Petro anasangalala ndi mwai wabwino kwambiri monga mtumwi wa Yesu Kristu, ndi zoonadi. Koma palibe kulikonse kumene iye amasonyezako kuti iye analingalira kuti iye anali mkuru wa atumwi. Ndiponso sitimawerenga pena paliponse kuti atumwi ndi ophunzira enawo anamzindkira Petro kukhala “papa” nampatsa iye ulemu woterowo. Pa nthawi imodzi mtumwi Paulo anakuona kukhala koyenerera kumdzudzula Petro (Kefa) mwapoyera pakukhala akumakatsatira kacitidwe kamene sikanali kogwirizana ndi cikhulupiriro Cacikristu. Ceniceni cakuti Petro anali atalakwa pa nkhani iyi yonena za cikhulupiriro ndi kakhalidwe ndi kutinso Paulo anaona kukhala waufulu kumuongolera iye poyera cimasonyeza kuti Petro sanali kuonedwa monga mutu “wosalakwa” wa atumwiwo kapena wa carici coyambirira. (Agalatiya 2:11-14) Mu carici coona muli Mutu umodzi wokha, Yesu Kristu, ameneyo, kuyambira pa nthawi imene anaukitsidwa, ali ‘wamoyo kwamuyaya,’ ndipo cifukwa ca cimeneco safunikira kukhala ndi omlowa m’malo.—Ahebri 7:23-25.
CARICI COGWIRIZANA
13. (a) Kodi ndi mau ati a Yesu amene amasonyeza kuti sipanayenera kukhala magawano a mpingowo kukhala akulu a mpingo ndi Akristu wamba? (b) Kodi ndi motani mmene awo amene anali kutsogolera mu mpingowo anayenera kukhalira?
13 Yesu, Mutuwo, samaligawa thupi la mpingo wacewo kukhala kagulu ka akulu a mpingo ndi gulu la Akristu wamba mwa “anthu wamba.” Iye amawauza atsatiri ace kuti: “Musachedwa Rabi; pakuti Mphunzitsi wanu ali mmodzi, ndipo inu nonse muli abale. Ndipo inu musachule wina atate wanu pansi pano, pakuti alipo mmodzi ndiye Atate wanu wa Kumwamba. Ndipo musachedwa atsogoleri, pakuti alipo mmodzi Mtsogoleri wanu, ndiye Kristu.” (Mateyu 23:8-10) Cotero Yesu amasonyeza kuti palibe magawano pakati pa awo amene amacipanga carici coonaco. Komabe, iye analinganiza kuti anthu azitsogolera mu mpingo Wachikristu, kuti azitumikire zosowa zauzimu za abale ao ndi kuilinganiza nchito ya kulalikira mbiri yabwino. Yesu ananena kuti amenewo sanayenera “kucita ufumu” pa iwo abale ao koma anayenera kukhala monga akapolo kapena atumiki ao. (Mateyu 20:25-28) Kodi akulu a mpingo amene muwadziwa amacita zimenezo?
14. Kodi ncifukwa ninji awo amene akucipanga carici coonaco ayenera kusonkhanitsidwira m’gulu limodzi lokha kaamba ka kulambira?
14 Kuti agwirizane ndi kalongosoledwe ka Baibulo ka carici coona, awo amene amacipangawo ayenera kukhala ogwirizana mu kulambira kwao. Mu nsonga iyi mtumwi Paulo analemba kuti: “Koma ndikudandaulirani inu, abale, mwa dzina la Ambuye wathu Yesu Kristu, kuti munene cimodzimodzi inu nonse, ndi kuti pasakhale malekano pakati pa inu; koma mumangike mu mtima womwewo ndi m’ciweruziro comweco.” (1 Akorinto 1:10) Cotero ife sitingayembekezere Mwamalemba kuwapeza iwo atafalikira pakati pa zipembezo zonse zomaombanazo za mu Cikristu ca Dziko. Iwo ayenera kusonkhanitsidwira limodzi mu gulu limodzi lokha. Monga momwe Aefeso 4:4, 5 amanenera ponena za iwo: “Thupi limodzi . . . Ambuye mmodzi, cikhulupiriro cimodzi.” Kuli kofunika kwa ife kudziwa cimene “cikhulupiriro cimodzi” cimeneco ciri.
KUCIZINDIKIRA CARICI COONACO NDI MAZIKO ACE
15. (a) Kodi ndi motani mmene Krstu limodzi ndi mpingo wacewo amawapindulitsira anthu ena onse omvera? (b) Kodi ndi thayo lotani limene Yesu amanena kuti iye adzalipereka ku carici cace coonaco pa nthawi ya kudza mu mphamvu yace ya Ufumu?
15 Ziwalo za carici coonaco zotsogozedwa ndi Kristu mutu wao zikunenedwa kukhala “mbeu ya Abrahamu, olowa nyumba monga mwa lonjezano.” (Agalatiya 3:29) Lonjezo ili ndilo lakuti ena onse a mtundu wa anthu womvera adzadzidalitsa okha kupyolera mwa Kristu ndi mpingo wace. (Genesis 22:18) Baibulo linaneneratu kuti, pa nthawi ya kukhazikitsa ufumu wa Kristu, padzakhala kokha otsalira a ana amenewa a “Yerusalemu wakumwamba,” gulu lakumwamba la Mulungu, amene adzatsalira pa dziko lapansi. (Agalatiya 4:26; Cibvumbulutso 12:10, 17) Yesu anazilongosola ziwalo izi za carici cake [a dziko lapansi kukhala “kapolo wokhulupirika ndi wocenjera.” Ndipo ananena kuti oterowo amene anapezeka kukhala akumatumikira mokhulupirika pa nthawi ya kudza kwace ku nchito ya kupereka ciweruzo adzasankhidwa kukhala “oyang’anira zace zonse,” ndiko kunena kuti, pa zabwino zonse za pa dziko lapansi za ufumu wa Kristu. Iwo zkakhala akumatsogolera mu nchito ya kulalikira mbiri yabwino ya ufumu wokhazikitsidwawo ku mitundu yonse mu “nthawi ya mapeto.”—Mateyu 24:14, 45-47; 25:19-23.
16. Kodi ndi madalitso otani amene amadza kwa awo amene amasonyeza kuwazindikira moyenera makonzedwe amenewa?
16 Awo onse lerolino amene amayembekezera kupindula moyo wamuyaya mu dongosolo latsopano la Mulungu ayenera kuwazindikira makonzedwe amenewa. Pakuti Yesu ananena kuti, mu “nthawi yamapeto” iyi, iye amawasankhira malo a ciyanjo awo amene amawacitira zabwino otsalira a “abale” ace, olowa nyumba ogwirizana naye amene amupanga mpingo Wacikristuwo. (Mateyu 25:31-40) Amenewa ndiwo otsalira a “miyala yamoyo” imene ikumangidwa nyumba yauzimu kapena kacisi, “cokhalamo Mulungu mwa mizimu.” (1 Petro 2:5; Aefeso 2:20-22) Awo ‘ozicitira zabwino’ ziwalo za kagulu ka kacisi kameneka akulongosoledwa m’bukhu la Cibvumbulutso kukhala “khamu lalikuru” la anthu amene amalowa m’cinjirizo la Mulungu. Taonaninso kuti, iwo amatumikira Mulungu mwacisangalalo “usana ndi usiku m’Kacisi mwace,” ndiko kunena kuti, mogwirizana ndi otsalira a kagulu kauzimu ka pa kacisiko, mpingo Wacikristu.—Cibvumbulutso 7:9, 10, 15.
17. Mwa cimeneco, kodi nciani cimene anthu onga nkhosa amanena kwa otsalira a carici coonaco?
17 Mwa cimeneco, anthu onga nkhosa amenewo amanena kwa olowa nyumba a lonjezo limene linaperekedwa kwa Abrahamuwo kuti: “Tidzamuka nanu, pakuti tamva kuti Mulungu ali ndi inu.” (Zekariya 8:23) Monga momwe awo a carici coona kapena mpingo woonawo amayenda mokhulupirika m’mapazi a Kristu ndi kumaulengeza uthenga Waufumuwo, kuli cimodzimodzinso ndi onga nkhosa awa ‘amapita nawo limodzi,’ kumatumikira Mulungu limodzi nawo. Kodi inu mukucita cimeneco? Ngati ndi conco, muli ndi ciyembekezo ca kulandira moyo wamuyaya pano pa dziko lapansi, limodzi ndi madalitso ena onse amene adzatsatirapo kucokera kwa Kristu limodzi ndi mpingo wace wolemekezedwawo m’mwamba.