Phunziro 6
‘Chitani Khama Kuŵerenga Poyera’
1, 2. Kodi ndi liti pamene timakhala ndi mipata yoŵerenga poyera?
1 Mtumwi Paulo analimbikitsa Timoteo kuti, “Pitiriza kuchita khama pa kuŵerenga poyera.” Ndipo iye analangiza Timoteo kuti aphunzitse Akristu anzake zimenezo limodzinso ndi ziyeneretso zina za utumiki. (1 Tim. 4:13, NW) Uphungu wouziridwa umenewo ulinso woyenerera kwa aliyense wa atumiki a Mulungu lerolino, ndipo tichita bwino kuulabadira.
2 Kuŵerenga poyera kaŵirikaŵiri kumafunika kwa mtumiki wateokalase. Pa phunziro la Nsanja ya Olonda ndi pa phunziro la buku la mpingo malemba ndi ndime zimafunikira kuŵerengedwa. Pamsonkhano wa utumiki ndi Sukulu ya Utumiki Wateokalase, kudzanso mu utumiki wakumunda, malemba a m’Baibulo amaŵerengedwa. Choncho, kukhala m’ŵerengi wabwino poyera kumapindulitsa mtumiki aliyense wa Mulungu ndi amvetseriwo.
3. Kodi kukonzekera n’kofunika chifukwa chiyani?
3 Kuŵerenga kwapoyera ndiko kuŵerenga mofuula kuti ena apindule. Koma kodi omvetsera adzapinduladi ngati woŵerengayo amadodoma potchula mawu ndi kutchula mawu mosayenera kapena kugogomeza mawu osafuna chigogomezocho kumene kumaphimba lingaliro? Kodi angakhale nacho chidwi ngati m’ŵerengiyo saŵerenga mwaumoyo, akumangoŵerenga ndi liwu limodzi losasintha? Kuti muŵerenge bwino pagulu, m’pofunika kuti mukonzekere. Sibwino kupita kukachita gawo lanu logaŵiridwa kwa inu, ngakhale la kuŵerenga paphunziro la buku la mpingo, popanda kuŵerenga pasadakhale nkhaniyo. Apo phuluzi, amvetseri sadzapeza phindu limene akanayenera kupeza, ndipo mwina angaphunzire matchulidwe olakwika a mawu ena kwa woŵerengayo.—Hab. 2:2.
4, 5. Kodi ndi mikhalidwe yotani imene ikufunika kuti kuŵerenga kwapoyera kusonkhezere omvetsera, ndi kuti kumveke mosavuta?
4 Mikhalidwe yofunika. Poŵerenga, khalani waumoyo. Ikani umoyo m’kuŵerenga kwanu, mukumaonetsa mzimu wake wa mawuwo. Mwakutero, mudzapeŵa kuŵerenga kozizira ndi kopanda umoyo. Samalani kuti musatsitse kwambiri mawu anu moti omvetsera anu n’kuphonya mbali zina zofunika. Mawu anu akhale omvekera bwino mbali zonse za nyumbayo kapena holo imene mwasonkhanamo. Palibe aliyense afunikira kuchinjikira khutu lake ngakhale pa liwu limodzi lokha kuti amve.
5 N’kofunika kumveketsa bwino mawu anu, popanda kudulira mbali zake zina, kusawatchula bwinobwino. Ndipo sibwinonso kukhala wosamalitsa monyanyira moti chidwi chonse cha omvetsera n’kupita ku kaŵerengedwe kokhakokhako ndi kusasamalanso za uthengawo. Kuŵerenga komveketsa bwino mawu kumatanthauza kuti womvetsera satsala m’malere pa mawu amene mukuŵerenga. Kusamvekera bwino kaŵirikaŵiri kumachitika chifukwa chosatulutsa mawu onse mokwanira kwa omvetsera. Choncho, zoloŵerani kuweramutsa mutu wanu poŵerenga. Tsegulani pakamwa panu kuti mawu azituluka mosatsinira.
6. Kodi nchiyani chingatithandize kudziŵa moika chigogomezo choyenera, ndipo ndi motani mmene kupuma kumaperekera chigogomezo?
6 Kugogomeza koyenera n’kofunika. Ndithudi, ndiyo mfungulo ya kuzindikira chimene mukuŵerenga. N’kodziŵika bwino kuti kusintha chigogomezo kungapereke tanthauzo losiyana kotheratu kwa omvetsera. Nthaŵi zina liwu limodzi limafuna chigogomezo chapadera, koma kaŵirikaŵiri timafunikira kugogomeza kagulu ka mawu kapena chiganizo. Chimene chingatidziŵitse poika chigogomezo ndicho lingaliro limene tikufuna kupereka, ndipo chotsogolera zimenezo ndicho mfundo yaikulu ya nkhaniyo, osati chabe ndi mbali ina ya sentensiyo. Kupuma m’malo oyenera kumathandiza kwambiri kugogomeza. Kuima pang’ono kumathandiza kuphatikiza mawu m’njira yatanthauzo ndi kusonyeza malingaliro aakulu; kupuma kotalikirapo kumasonyeza mapeto a mbali yaikulu m’sentensiyo.
7. Kodi n’chiyani chimathandiza kuti kuŵerenga kumveke ngati kulankhula kwachibadwa?
7 Poyesetsa kuŵerenga bwino muyenera kusamalanso za mphamvu ya mawu komanso liŵiro lake. Popanda zimenezo, kaŵerengedweko kadzakhala kozizira ndi kosakoma. Koma ngati kuchitidwa bwino, kusinthasintha liwu koteroko kumathandiza kwambiri kuchititsa kuŵerenga kwanu kumveka monga kulankhula kwachibadwa.
8. Kodi ndi liti pamene nkhani yoŵerenga ingakambidwe?
8 Nkhani yoŵerenga. Mbali ina yofunika kwambiri ya kuŵerenga kwapoyera ndiyo kukamba nkhani yoŵerenga. Nkhani imeneyi ili ndi malo ake. Mwachitsanzo, Sosaite nthaŵi ndi nthaŵi ingalinganizire mipingo yonse ya anthu a Mulungu m’dziko lina kuti amve nkhani imodzimodzi panthaŵi imodzi. Malo ena a nkhani zoŵerenga ndi pamisonkhano yaikulu, pamene kumakhala kotheka kuti mbali zina za nkhaniyo n’kugwidwa mawu ndi atola nkhani kapena pamene nkhaniyo ikufunikira kukambidwa m’njira yakutiyakuti yolondola kwambiri.
9, 10. Kodi chovuta chofuna kuchigonjetsa pokamba nkhani yoŵerenga n’chiyani, ndipo tingachite motani zimenezo?
9 Chovuta kwambiri chofunika kuchigonjetsa popereka nkhani yoŵerenga ndicho kuŵerenga mwanjira yakuti mawuwo amveke ngati kulankhula kwachibadwa. Komabe, liwu liyenera kukhala lalikulu bwino. Kaŵirikaŵiri mawu a m’nkhani yolembedwa amaima mosiyana ndi mmene mumalankhulira mwa masiku onse, mwina masentensi kukhala otalikirapo ndi ocholoŵana. Mawu ake angakhale amene simunazoloŵere komanso kakambidwe kake kangakhale kosiyana ndi malankhulidwe anu achibadwa. Mungaone kuti mukanakamba bwino kwambiri ngati mukanaika nkhaniyo m’mawu anuanu. Koma kuyesetsa ndi kuzoloŵera kudzakuthandizani kupita patsogolo kwambiri pa kukamba nkhani zoŵerenga.
10 Kukonzekera pasadakhale, ndiko kiyi yachipambano. Muyenera kutenga nthaŵi kuti muizoloŵere nkhaniyo. Iŵerengeni kangapo kuti mumvetse mfundo zazikulu. Ngati mupezamo mawu achilendo, ayang’aneni m’dikishonale kapena funsani za matanthauzo ndi matchulidwe ake kwa odziŵa bwino chinenero. Ndiyeno yesezani kukamba nkhaniyo mofuula kuti muzoloŵere kakambidwe ka wolemba nkhaniyo. Oŵerenga ena amapeza kuti kuyeseza mofuula akudziyang’ana m’galasi kumawathandiza pambali ya kuyang’ana omvetsera, kumene kuli kofunika kwambiri ngati nkhaniyo ikukambidwa m’holo yaing’ono.
11. Kodi ndi zizindikiro zotani zolemba pankhani yoŵerenga zimene zili zothandiza?
11 Kuli kothandiza kulemba mzera kapena kuchonga mawu ofunika amene mukufuna kuwagogomeza. Oŵerenga ena aona kuti nkothandiza kulemba timizera tonga kotere | togaŵira mawu. Ndiponso, magulu a mawu ovuta kapena achilendo amene muyenera kuwatchula nthaŵi imodzi mosapumira, mungawamange pamodzi ndi mzera wodutsa pamwamba pa mawuwo wokukumbutsani kusaima kufikira mutafika kumapeto kwa mawuwo. Zimenezi zimachititsa kuŵerenga kumveka kwachibadwa komanso kwatanthauzo. Tingaganizirenso za kulemba zizindikiro m’nkhaniyo zosonyeza malo ofuna kupuma kotalikirapo. Kupuma kungadzutse chidwi, kungapereke chigogomezero ndi kulola nthaŵi yakuti mfundozo zikhomerezeke. N’kofunikanso kudziŵa pachimake pankhaniyo kapena mfundo zake zazikulu. Mmenemu mungaikemo zizindikiro, zokutsogolerani kufika pachimake chabwino, komanso kusintha liŵiro.
12-15. N’chifukwa chiyani kukonzekera pasadakhale kuli kofunika kwenikweni poŵerenga Baibulo?
12 Kuŵerenga Baibulo. Kuŵerenga Baibulo n’kofunika kwa achichepere ndi achikulire omwe. Kaŵirikaŵiri pamakhala mikhalidwe yofuna kuŵerenga Baibulo mofuula. Pangakhale nkhani zoterozo nthaŵi ndi nthaŵi mu Sukulu ya Utumiki Wateokalase. Ndipo tonsefe timaŵerenga malemba polankhula ndi anthu mu utumiki wathu. Koma kodi timawaŵerenga bwino? Kodi timayeseza kuti tisamadodome, kuti tigogomeze mbali zochirikiza mfundo yathu ndi kuti kuŵerenga kwathu kumveke ngati kukambirana kwachibadwa?
13 Ndithudi kukonzekera kumafunika kuti tiŵerenge Baibulo. Kumbukirani kuti Baibulo ndi Mawu a Mulungu, kuti ladzaza ndime zokongola ndi zosonkhezera maganizo kwambiri, kudzanso malingaliro olongosoka ndi atsatanetsatane. Tiyenera kuliŵerenga moyenera kuti omvetsera apindule. Titadziŵiratu kuti tidzaŵerenga Baibulo, tiyenera kukonzekera mosamalitsa, kuti tipeŵe kudodoma pamawu achilendo, kapena ziganizo zina.
14 Talingalirani nthaŵi yokondweretsa ija pamene andende obwerera kwawo a Israyeli anasonkhana pabwalo patsogolo pa Chipata cha ku Madzi cha Yerusalemu kuti amvetsere mwachidwi mawu a Mulungu wawo. Kodi Aleviwo opatsidwa nkhani zoŵerengazo anali osakonzekera ndi osasamala poŵerenga? Nkhaniyo imati: “Naŵerenga iwo m’buku m’chilamulo cha Mulungu momveka, natanthauzira, nawazindikiritsa choŵerengedwacho.” (Neh. 8:8) Oŵerengawo anali ndi ulemu waukulu kwa Wamkulukuluyo, amene mawu ake iwo anali kuwanena kwa alambiri anzawo.
15 Kaya tikudziŵerengera tokha mofuula kuti tipindule ife eni, kaya ndi pabanja, m’Nyumba ya Ufumu, kapena kwa munthu wina pakhomo pake, tikhale ndi cholinga cha kulankhula nkhani mokhulupirika monga momwe inalembedwera, ndi mzimu wake wonse ndi mphamvu yolimbikitsa chikhulupiriro. Mphamvu yosonkhezera imeneyi ya kuŵerenga kwapoyera yagogomezedwa m’mawu aŵa olembedwa ndi mtumwi Yohane: “Wodala iye amene aŵerenga, ndi iwo amene akumva mawu a chinenerocho [“ulosiwo,” NW], nasunga zolembedwa momwemo; pakuti nthaŵi yayandikira.”—Chiv. 1:3.