Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • sg phunziro 10 tsamba 49-54
  • Kukulitsa Luso Lophunzitsa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kukulitsa Luso Lophunzitsa
  • Buku Lolangiza la Sukulu ya Utumiki Wateokalase
  • Nkhani Yofanana
  • Yang’anirani ‘Luso Lanu la Kuphunzitsa’
    Nsanja ya Olonda—2008
  • Mmene Tingapangire ophunzira ndi Buku la Chidziŵitso
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
  • Muzithandiza Ophunzira Baibulo Anu Kuti Afike Pobatizidwa​—Gawo 2
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2020
  • Tsanzirani Mphunzitsi Wamkulu
    Nsanja ya Olonda—2002
Onani Zambiri
Buku Lolangiza la Sukulu ya Utumiki Wateokalase
sg phunziro 10 tsamba 49-54

Phunziro 10

Kukulitsa Luso Lophunzitsa

1-3. Kodi kuphunzitsa kumaphatikizapo chiyani, ndipo ndi mipata yotani yophunzitsira imene tili nayo?

1 Ife monga Akristu oona timayang’ana kwa Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu monga Aphunzitsi athu Aakulu. Timagwirizana ndi wamasalmo amene anapempha Yehova kuti: “Mundiphunzitse chokonda Inu.” (Sal. 143:10) Tilinso ndi maganizo ofanana ndi ophunzira a Yesu a m’zaka za zana loyamba amene anatcha Yesu “Mphunzitsi.” Ndipo n’zoona kuti Yesu analidi mphunzitsi wopambana! Atapereka Ulaliki wake wa pa Phiri, “makamu a anthu anazizwa ndi chiphunzitso chake: pakuti anawaphunzitsa monga mwini mphamvu.” (Mat. 7:28, 29) Ameneŵa ndiwo Aphunzitsi Aakulu Kopambana, ndipo timafuna kuwatsanzira iwo.

2 Kuphunzitsa ndi luso lofuna kulikulitsa. Kumaphatikizapo kuyankha mafunso akuti chiyani, motani, chifukwa chiyani, kuti ndi liti, pankhani iliyonse. Mkristu aliyense afunikira kumakulitsa luso lake la kuphunzitsa, makamaka poganizira malangizo a Yesu kwa otsatira ake: “Phunzitsani anthu a mitundu yonse.” (Mat. 28:19, 20) Mfundo yoti imeneyi ndi ntchito yofunadi luso titha kuiona m’langizo la mtumwi Paulo kwa Timoteo pamene anati: “Chenjeza, ndi kuleza mtima konse ndi [luso la, NW] chiphunzitso.”—2 Tim. 4:2.

3 Ndithudi mipata ilipo yambiri yophunzitsira ena. Makolo afunikira kuphunzitsa ana awo. Alaliki a uthenga wabwino afunikira kuphunzitsa okondwerera achatsopano mwa maphunziro a Baibulo apanyumba. Kaŵirikaŵiri pamakhalanso mipata yolangizira ofalitsa atsopano. Ndipo abale ambiri amapatsidwa mwayi wolankhula nkhani zolimbikitsa, kaya ndi pamsonkhano wautumiki kapena nkhani zapoyera. Ophunzira onse m’Sukulu ya Utumiki Wateokalase ayenera kukhala ndi chidwi choonetsa kuti ali aphunzitsi amene akupita patsogolo. Pamene mukuyesetsa kukulitsa luso lanu la kuphunzitsa mu utumiki, mudzaona kuti luso limeneli n’lokhutiritsadi komanso lopindulitsa kwambiri. Palibe chinthu chosangalatsa ngati kuphunzitsa munthu wina Mawu a Mulungu, kenako n’kumuona iye akupita patsogolo bwinobwino mwauzimu.

4, 5. Kodi tiyenera kudalira ndani komanso chiyani pophunzitsa?

4 Kudalira Yehova. Chofunika chachikulu kuti tikhale mphunzitsi wogwira mtima wa uthenga wabwino ndicho kudalira Yehova, kum’zindikira iye, kutsatira chitsogozo chake ndi kupempha chithandizo chake. (Miy. 3:5, 6) Ngakhale Yesu anati, “Chiphunzitso changa sichili changa, koma cha Iye amene anandituma Ine.” (Yoh. 7:16) Iye nthaŵi zonse anatchula Mawu a Mulungu. M’makambirano ake olembedwawo, iye anagwira mawu mabuku pafupifupi theka la mabuku onse a Malemba Achihebri, nthaŵi zina akumangotchula za mabukuwo. Choncho pophunzitsa ena, dalirani Mawu a Mulungu a choonadi monga mmene anachitira Yesu. Pezani mayankho anu mmenemo, pakuti ndilo buku lokha lalikulu lophunzitsira anthu kukhala ophunzira a Yesu, inde bukulo ndilo Baibulo Loyera.—2 Tim. 3:16.

5 Ngati mudalira Yehova kwathunthu, simufunikira kudzimva wosakhoza. Mulungu amatiuza zolinga zake m’Mawu ake a choonadi. Ngati muuzako ena chidziŵitso chanu cha choonadi chimenechi, Yehova adzakuchirikizani. Musanene kuti, “Uphunzitsi si wa anthu ngati ife.” Mutha kukhala mphunzitsi waluso ngati mudalira Yehova mwa mapemphero.—2 Akor. 3:5.

6-8. Kodi kukonzekera kumatheketsa motani kuphunzitsa kogwira mtima?

6 Kukonzekera. Ndithudi, kuti muphunzitse zomveka, simungachitire mwina koma choyamba muidziŵe bwino nkhani yanu. Mufunikira kumvetsa bwino mfundo zake musanaziphunzitse munthu wina. (Aroma 2:21) Mmene chidziŵitso chanu chikuŵirikiza, muzinka namukhala mphunzitsi wabwinopo nthaŵi zonse. Koma ngakhale mutangodziŵa zoyambirira zingapo zokha za choonadi, mukhoza kukhalabe mphunzitsi. Ingolankhulani zimene mukuzidziŵa. Ngakhale ana aang’ono akhoza kuphunzitsa ana anzawo kusukulu choonadi chimene amaphunzira kwa makolo awo. Sukulu ya Utumiki Wateokalase ikuthandizani kukulitsa luso lanu la kuphunzitsa.

7 Ngati mukachititsa phunziro la Baibulo kapena kulankhula nkhani, choyamba mvetsani pa inu nokha mfundo zochirikiza nkhani yanu. Yesani kupeza chifukwa chake zinthu zakhalira mmene ziliri. Onani ngati mungathe kufotokoza maganizowo m’mawu anuanu. Mvetsani bwino umboni wa m’Malemba. Konzekerani kukatanthauzira malembawo mogwira mtima.

8 Mbali ina ya kukonzekera ndiyo kuganizira pasadakhale mafunso omwe angadzuke m’maganizo mwa wophunzira malinga ndi chipembedzo chake. Kuteroko kudzakuthandizani kukhala wokonzekera ndi chidziŵitso choyenerana ndi wophunzirayo. Kuzindikira zimene iye akuzidziŵa kale kudzakuthandizani kuyala maziko a mfundo zatsopano om’thandizirapo kupita patsogolo. Wophunzira wina angafunikire mfundo zosiyana malinga ndi zimene amakhulupirira. Choncho kudziŵa wophunzira wanu kumakuthandizani kukonzekera bwino.

9. Kodi mungawalimbikitse motani ophunzira kumayankha m’mawu awo?

9 Mafunso. Mafunso ndi othandiza kwambiri kuti muphunzitse mogwira mtima, monga momwe Yesu Kristu anasonyezera kaŵirikaŵiri. (Luka 10:36) Choncho pochititsa phunziro la Baibulo mukhoza kutsata njira yake, mwa kumagwiritsa ntchito mafunso olembedwa m’zofalitsa. Koma ngati muli mphunzitsi weniweni, simudzakhutira ngati wophunzirayo angoŵerenga yankho m’bukulo. Zikatero mudzafunikira kuperekapo mafunso ena owonjezera amene adzasonkhezera wophunzirayo kufotokoza mfundozo m’mawu akeake. Nthaŵi zina, mungofunikira kunena kuti: “Zimenezo n’zoona, koma mutati munene m’mawu anu mungati chiyani?”

10. Fotokozani ntchito ya mafunso otsogolera.

10 Mudzapezanso kuti mafunso otsogolera amathandiza kwambiri pophunzitsa. Ameneŵa ndi mafunso okuthandizani kutsogolera maganizo a munthuyo ku ganizo limene mwina sanakhalepo nalo. Mumatero mwa kugwiritsa ntchito zimene amazidziŵa kale. (Mat. 17:25, 26; 22:41-46) Zimene mumachita ndizo kunena mumtima mwanu kuti: ‘Wophunzirayu ndikudziŵa kuti amadziŵa zakutizakuti, choncho ngati ndim’funsa mafunso olondolozana, akhoza kufika paganizo loyenera. Koma ngati ndisiya mafunso otsogolera kuti ndingofunsa funso lenilenilo, angafike paganizo lolakwika.’ Kunena kwina, wophunzirayo amakhala ali nacho chidziŵitso choti afike payankho. Kungoti akufunikira chithandizo. N’zoona kuti njira yapafupi ndiyo kungomuuza yankholo. Koma ngati mugwiritsa ntchito mafunso otsogolera, yankholo lidzakhala lolandirika bwino kwa iye chifukwa amalipereka mwini yekha, komanso amathandizika kukhala ndi luso la kulingalira. Mafunso anu adzatsogolera maganizo ake m’masitepe a kulingalira kwatsatanetsatane mpaka atafika paganizo loyenera. Zimenezi zidzakhala zopindulitsa kwambiri kwa iye pambuyo pake.

11. Kodi mafunso ofufuza maganizo angagwiritsidwire ntchito motani?

11 Nthaŵi zina mudzapeza kuti m’pofunika kufunsa mafunso ofufuza maganizo. Mwa mafunso ameneŵa mumafuna kudziŵa zimene wophunzirayo amakhulupirira pankhaniyo. Mwachitsanzo, mungam’funse chimene lamulo la Mulungu limanena pa chiŵereŵere. Iye angatchule lemba limene limasonyeza kuti kutero n’kulakwa. Koma kodi wophunzirayo akuvomerezadi yankho limene waperekalo? Kodi ndiwo maganizo akenso? Mungafunse funso lofuna kudziŵa chimene iye kwenikweni amaganiza pa zachiwerewere. Mungafunse kuti, “Kodi zili n’kanthu ngati tikhala ndi moyo wotero kapena ngati tipeŵa zimenezo?” Pamenepo mutha kudziŵa mbali zofunikira chithandizo chokulirapo ndipo mungapitirize kumam’thandiza. Mafunso ofufuza maganizo amakuthandizani kum’fika pamtima wophunzirayo.

12, 13. N’chifukwa chiyani mafunso ali opindulitsa kuwagwiritsa ntchito ponse paŵiri mu utumiki wa kunyumba ndi nyumba ndi pokamba nkhani papulatifomu?

12 Mafunso alinso othandiza mu utumiki wa kunyumba ndi nyumba. Mwachitsanzo, mungafune kudziŵa zimene mwininyumba akuganiza kotero kuti mum’thandize bwino kuzindikira choonadi cha Baibulo. Muthanso kufunsa mafunso ndi kum’pempha kuti ayankhe chifukwa mukudziŵa kuti mutam’patsa mwayi woti alongosole maganizo ake, iye adzakhala ndi chidwi choti amvetsere zimene mukufuna kunena.

13 Ngakhale polankhula nkhani papulatifomu, pamakhala nthaŵi pamene mumafunsa mafunso ofuna yankho. Chotero mumapempha omvetsera kuti ayankhe. Komanso nthaŵi zina mumafunsa mafunso osafuna yankho—mafunso ofunsa kungoti musonkhezere omvetsera kuganiza, musakuyembekezera yankho kwa iwo. (Luka 12:49-51) Mayankhowo mumapereka ndinu mwini. Nthaŵi zina mungafunse mafunso angapo, musakupereka yankho kufikira mutafika palomalizira. Mtundu wa mafunso amene mungafunse umadalira omvetsera anu ndi zimene mukuwaphunzitsa.

14, 15. Kodi mafanizo ndi kubwereza, cholinga chake n’chiyani?

14 Mafanizo. Mafanizo anali ndi mbali yofunika kwambiri m’chiphunzitso cha Yesu. Mofananamo, aphunzitsi achikristu lerolino angagwiritse ntchito mafanizo a zochitika za moyo wa tsiku ndi tsiku kuti athandize kukhomereza ziphunzitso zabwino kwambiri m’maganizo mwa omvetsera awo. (Mat. 13:34, 35) Yesani kupereka mafanizo osavuta, chifukwa mafanizo ocholoŵana ndi ozama kwambiri angakhale ovuta kuwamvetsa ndipo angafooketse mfundo zanu. Kalata ya Yakobo ili ndi mafanizo ambiri—funde la m’nyanja, tsigiro la chombo, chogwirira m’kamwa mwa kavalo, kalirole, ndi ena otero. Onsewo anatengedwa pa zinthu zozoloŵereka pamoyo. Mphunzitsi watcheru adzayesetsa kupangitsa fanizolo kuyenerana ndi mikhalidwe ya wophunzira wake, msinkhu wake, chipembedzo chake, chikhalidwe cha kwawo, ndi zina zotero. Inde, mafanizo tingawagwiritsenso ntchito m’nkhani, komanso pophunzitsa munthu wina.

15 Kubwereza. Luso limeneli n’lofunika kwambiri pakuphunzitsa kwachipambano, kaya muli papulatifomu kapena mukuphunzitsa munthu panyumba. Yesani kukhomereza m’maganizo mwa womvetserayo mawu ofunika kwambiri, makamaka malemba. Ngati muli ndi nkhani ya wophunzira yokhala ndi mwininyumba, mungafunse mafunso obwereramo, kuti mumveketse mfundo mwa kubwereza. Mwa njira imeneyi mutha kukhala wotsimikiza kuti wophunzirayo wamvetsa lingalirolo. Mukatero, mudzakhala mukufunsa mofanana ndi Yesu pofunsa kuti: “Mwamvetsa zonsezi kodi?”—Mat. 13:51.

16. Ngati mlankhuli ali mphunzitsi wabwino, kodi mudzakhoza kukumbukira chiyani mutamvetsera nkhani yake?

16 Nkhani zimene zimaphunzitsa. Nkhani zimene mumakumbukira moyamikira ndi zija zimene munaphunziramo zochuluka. Chotero yesani kuzindikira chimene chimapangitsa alankhuli ena kukhala aphunzitsi abwino. Pezani chimene chimapangitsa nkhani zawo kukhala zosavuta kukumbukira. Mudzapeza kuti salankhula mofulumira. Amagwiritsa ntchito mafunso. Ponse paŵiri mafunso ofuna yankho kwa omvetsera kapena osafuna yankho ongowasonkhezera kuganiza. Amakupemphani kutsegula malemba ofunika ndi kuti muwatsatire pamene akuŵerenga, kuwafotokoza, kuwamasulira ndi pamene akugogomeza mfundo zazikulu. Ena amagwiritsa ntchito zinthu zoona ndi maso monga chitsanzo. Koma mulimonse, mudzaona kuti n’kwapafupi kwambiri kukumbukira mfundo zoŵerengeka zimene zamveketsedwa bwino koposa zambiri zongofotokozedwa patalipatali. Pamene mugwiritsa ntchito luso la kuphunzitsa, omvetserawo ayenera mosavuta kukhala okhoza kutchula mutu wa nkhani, mfundo zazikulu ndipo mwinanso lemba limodzi kapena aŵiri amene aoneka kukhala apadera.

17, 18. Kodi ndi motani ndipo n’chifukwa chiyani tiyenera kuwadziŵikitsa Aphunzitsi Aakuluwo?

17 Kudziŵikitsa Aphunzitsi Aakulu. Monga mphunzitsi wachikristu nthaŵi zonse muyenera kukumbukira kuti m’pofunika kudziŵikitsa Yehova Mulungu monga Gwero la moyo komanso Yesu Kristu monga njira ya Mulungu yodzeramo moyo ndi madalitso. (Yoh. 17:3) Yesetsani kuthandiza ena kuzindikira ndi kuyamikira Aphunzitsi Aakulu kwambiri ameneŵa.

18 Pamene mukulitsa luso la kuphunzitsa mudzazindikiranso mbali imene chikondi chimachita. Ngati wophunzira afika pom’kondadi Yehova Mulungu, pamenepo adzam’tumikira mokhulupirika. Chotero, pamene phunziro lili m’kati, komanso panthaŵi zoyenera, tchulani thandizo lalikulu limene Mulungu wachitira anthu ochimwafe ndi zimene akutichitirabe. Gogomezani nzeru, chilungamo, chikondi ndi mphamvu za Mulungu, inde mikhalidwe yake ija imene nthaŵi zonse imagwirizana modabwitsa kwambiri kuti anthu omvera apindule. Ngati mtima wa wophunzirayo uli wowongoka, popita nthaŵi iyenso adzakhala wokhulupirika mozama kwa Yehova ndi wofunitsitsa kukhala ndi mbali m’kulemekeza dzina lake.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena