Phunziro 14
Khalani Osamala Komanso Olimba
1. N’chifukwa chiyani tiyenera kukulitsa mkhalidwe wakukhala wosamala pochita ndi ena?
1 Potumiza ophunzira ake kukalalikira, Yesu anawauziratu momvekera bwino kuti akasamale ndi zimene azikanena ndi kuchita. Ngakhale analonjeza kuti akakhala nawo, iwo sanayenera kuchita zinthu zimene zikanabutsa mavuto palibelibe. (Mat. 10:16) Ngakhale pakati pa iwo okha, Akristu ayenera kusamala m’kalankhulidwe ndi kachitidwe kawo kuti asakhumudwitsane wina ndi mnzake. (Miy. 12:8, 18) Choncho m’pofunikira kukulitsa luso lokhala wosamala kwambiri.
2. Kodi kukhala wosamala ndiko chiyani?
2 Kukhala wosamala ndiko “kuzindikira chimene chili choyenera kunena kapena kuchita, pamene muli ndi ena,” ndi “luso lodziŵa kuchita ndi ena popanda kuwakhumudwitsa.” Kukhala wosamala kumatanthauza kukhala wachisomo m’kalankhulidwe ndi kachitidwe kotero kuti ena asakhale ndi maganizo okhumudwa. Sitikufuna kuti wina aliyense akhumudwe ndi njira imene talankhula naye, kapena imene tachitiramo chinthu. Komabe, zimenezi sizikutanthauza kuti sitidzakhumudwitsa wina aliyense ndi zimene tinena kapena kuchita, chifukwa uthenga wa Baibulo weniweniwo uli chokhumudwitsa kwa ena. (Aroma 9:33; 2 Akor. 2:15, 16) Choncho, pamene tikukhala osamala m’kachitidwe, tikhalenso olimba pa choonadi cha Mulungu.
3. Fotokozani mmene zipatso za mzimu zakhalira maziko a mkhalidwe wosamala.
3 Pamoyo wathu wa tsiku ndi tsiku n’kosavuta kukhala wosamala ngati tionetsa zipatso za mzimu wa Mulungu. Zipatso zimenezo ndizo gwero, kapena maziko, okhalira wosamala. (Agal. 5:22, 23) Mwachitsanzo, munthu wokonda anzake sangafune kuwakwiyitsa, koma amakhala wofunitsitsa kuwathandiza. Munthu amene amaonetsa kukoma mtima amakhala wodekha m’kachitidwe kake ka zinthu. Ndipo munthu amene wakulitsa mkhalidwe wodziletsa nakhalabe wodekha zinthu zikavuta, kaŵirikaŵiri akhoza kukopa munthu winayo kuti agwirizane ndi lingaliro lake. Komabe, munthu wopsa mtima msanga kapena waukali sachedwa kunena zinthu mosaganiza zimene zimakwiyitsa ena amene akulankhula nawo. (Miy. 15:18) Kalankhulidwe kathu ndi kachitidwe kathu ka zinthu kayenera kukhala kaja kokopa anthu oganiza bwino, osati kowaingitsa.
4-8. (a) Kodi tingaonetse motani kukhala wosamala mu utumiki wathu wa kunyumba ndi nyumba? (b) Kodi kukhala wosamala kumafuna kuti tigonje? Nanga kumaphatikizapo chiyani?
4 Kusamala pamene tili mu utumiki wakumunda. Mu utumiki wa kunyumba ndi nyumba, mungakhale wosamala mwa kuyamba makambirano anu ndi zinthu zimene zimadandaulitsa mwininyumbayo ndi kusonyeza mmene ufumu wa Mulungu udzathetsera zovutazo. M’thokozeni pa maganizo ake okonda chilungamo, kalingaliridwe kake ndi mtima wake wofuna zinthu zabwino. Kuseka kapena kusuliza chipembedzo chake kudzangotseka maganizo ake. Choncho, m’malo molankhula zinthu zobutsa mikangano, kambiranani zinthu zimene anthu ambiri amazivomereza kukhala zoyenera. Ngati kuli kofunika kukambirana nkhani ina imene ingabutse mkangano, choyamba pezani mfundo imene mungagwirizane ndi mwininyumba, ndipo gogomezani mgwirizano umenewo. Ngati mungakhutiritse mwininyumbayo ndi mfundo za choonadi zopatsa chiyembekezo cha Ufumu ndi madalitso ake, nkhani zinazo mudzaziwongolera m’kupita kwa nthaŵi pamene munthuyo ayamba kukhala ndi chidziŵitso chozamirapo ponena za chisomo cha Mulungu.
5 Munthu wosamala amayesetsa kukopa amene akulankhula nayeyo kuti aloŵe m’makambiranowo ndi kuti apende malingaliro akewo. Paulo anayesetsa kugwiritsa ntchito maganizo awo aja amene anawalalikira, moti anakhoza kupereka mfundo zogometsa mochirikiza uthenga wabwino. (1 Akor. 9:20-22) Ife tifunikira kuchita chimodzimodzi. Kuganizira mwachifundo za mikhalidwe ya anthu ena, chifukwa chimene iwo alili motero, chifukwa chimene amakhulupirira ndi kulankhula mmene akuchitiramo, kudzakuthandizani kuchita nawo mosamala komanso mwachifundo. Mwinamwake chimene chikuwachititsa kulingalira mwa njira imeneyo ndi mikhalidwe yosiyanasiyana pamoyo, mwinanso zimene akumana nazo, kapenanso chifukwa cha chikhulupiriro chinachake chimene ali nacho. Mutapeza chimene chikuchititsa kalingaliridwe kakeko, mukhoza tsopano kupeza njira yabwino yoloŵetsera makambirano anuwo mu ulaliki wa uthenga wabwino, m’malo moti munene zokhumudwitsa winayo chifukwa chosadziŵa zifukwa zimene akukhalira ndi maganizo amenewo.
6 Kuganizira malingaliro a munthu winayo sikutanthauza kuti muchoke pa chimene chili cholondola. Kukhala wosamala sikupotoza choonadi. Nthaŵi zonse muyenera kukhala wolimba pa cholondola. Kupanda kutero, wina angapeze kuti pofuna kukhala wosamala akupotozanso choonadi. Chimene chingakulepo ndicho kuopa munthu m’malo mokonda chilungamo. Komabe, ngakhale kuti kusamala sindiko kupotoza choonadi, iko kumafunanso nthaŵi yake, ndiko kuti, kusankha bwino nthaŵi yoti mupereke chidziŵitso chakutichakuti. Nthaŵi zina kukhala wosamala kumafuna kungonyalanyaza zimene wina wanena. Kungakhale bwino kwambiri zinthu zina kuzisiyira nthaŵi ina m’tsogolo, pamene munthuyo adzakhala wozikonzekera. Ndi mmenenso Yesu anachitira pamene anati: “Ndili nazo zambirinso zakunena kwa inu, koma simungathe kuzisenza tsopano lino.” (Yoh. 16:12) Choncho ngakhale pamene tisakugwirizana ndi amene tikulankhulana nayeyo, tiyenera kupeŵa kuyesa kuwongolera nthaŵi yomweyo lingaliro lina lililonse lolakwika. Tikamatero, tizingotseka maganizo ake ndi kuletsa makambirano kuti asapitirire.
7 Pamene mwininyumba m’kati mokambirana, atchula zinthu zambiri za m’Baibulo zimene iye akunena kuti n’zolakwa, m’povuta kuti m’nthaŵi yaifupiyo mutsutse mosamala chilichonse cha zimene wanenazo. Kaŵirikaŵiri ndi bwino kungonyalanyaza zochuluka za izo ndi kukambirana zokhazo zokhudzana ndi nkhani imene mukukambiranayo. Kapena mwininyumba angayese kukuloŵetsani m’mikangano ya nkhani za dziko. Mwaluso peŵani kuloŵetsedwamo, mukumapereka yankho la m’Baibulo pa mavuto apadziko oterowo. Mwa kutero mudzatengera chitsanzo cha Yesu.—Mat. 22:15-22.
8 Pamene mukumana ndi mwininyumba waukali, khalani wosamala komanso wolimba. Musalole kuti choonadi chisukuluke pofuna kuziziritsa mtima wa munthuyo. M’malo mwake, yesani kumvetsa chifukwa chake akulingalira motero, mwina ngakhale kum’funsa chimene akuganizira zimenezo. Ngati ayankha, inunso munganene kuti mukufuna kumuuza chifukwa chake mukuganizira m’njira ina. Koma ngakhale kuti makambiranowo akufikitsani potani, kukhala wosamala n’kumene kudzaphulapo zabwino koposa. Kumbukirani uphungu wa pa Miyambo 15:1: “Mayankhidwe ofatsa abweza mkwiyo; koma mawu oŵaŵitsa aputa msunamo.” Komabe, ngati anthu ena aonetsa kukhala osaganiza, chanzeru pamenepo ndi kungochokapo.—Mat. 7:6.
9, 10. Kodi kukhala wosamala n’kofunikanso pochita ndi abale athu achikristu?
9 Kuchita mosamala ndi abale achikristu. Kuchita kwathu mosamala tiyenera kukukulitsa osati kulinga kwa anthu osadziŵa Yehova okha, koma n’kofunikanso pochita ndi abale athu auzimu. Nthaŵi zina abale ndi alongo amene amakhala osamala kwambiri mu utumiki wakumunda angaiŵale kukhalanso osamala pochita ndi abale awo. Kukhala wodekha m’kalankhulidwe ndi m’kachitidwe n’kofunika kwambiri m’gulu la Yehova polimbikitsa mzimu wa chikondi ndi umodzi komanso kumvana kwa tsiku ndi tsiku. Paulo anati: “Tichitire onse chokoma, koma makamaka iwo a pa banja la chikhulupiriro.”—Agal. 6:10.
10 Timasamala za abale athu, makamaka ponena za thanzi lawo lauzimu, chifukwa tonse tili m’gulu la Yehova. (Afil. 2:2, 4) Komabe, munthu wosamala amazindikira kuti pamene akusamala za abale ake, safunikira kuloŵerera m’nkhani zaumwini, mwina kumafunsa mafunso ochititsa manyazi pankhani zimene sizim’khudza. Kukhala wosamala kudzatithandiza kusakhala ‘wodudukira nkhani za eni.’—1 Pet. 4:15.
11. Kodi Malemba amasonyeza motani kuti akulu afunikira kukhala osamala mumpingo?
11 Kukhala wosamala n’kofunikanso makamaka kwa akulu chifukwa amasamalira mavuto mumpingo. Pamene mtumwi Paulo anapatsa Timoteo malangizo onena za mmene angachitire ndi anthu osalamulirika mumpingo wachikristu, iye anagogomeza kufunika kokhala wodekha ndi wokoma mtima, akumati: ‘Kapolo wa Ambuye sayenera kuchita ndewu, komatu akhale woyenera, waulere pa onse, . . . woleza, wolangiza iwo akutsutsana mofatsa; ngati kapena . . . akazindikire choonadi, ndipo akadzipulumutse ku msampha wa Mdyerekezi.’ (2 Tim. 2:24-26) Mofanafanamo mtumwiyo analangiza kugwiritsa ntchito “mzimu wa chifatso” pofikira mbale wina amene watenga sitepe lolakwika asanazindikire. (Agal. 6:1) Popatsa uphungu anthu oterowo akulu afunikira kukhala osamala, komanso akhalenso olimba pa chilungamo.
12, 13. Nanga n’chifukwa chiyani kusamala kuli kofunika m’mabanja mwathu?
12 Kukhala kwathu osamala pochita ndi ena kuyenera kuphatikizapo apabanja pathu. Palibe chifukwa chokhadzulira mawu wina wa m’banja kapena kum’chitira mosakoma mtima chabe chifukwa chakuti tam’zoloŵera. Iwonso amafunikira kuchita nawo mosamala. Koma ngati muwakhadzulira mawu kapena kunena nawo mwaukali, adzatifutuka. Ndipo ngati ena m’banjalo si atumiki a Yehova, kodi ndiye kuti tiyenera kukhala wosasamala polankhula nawo? Kutalitali. Chifukwa kukhala wosamala pochita ndi osakhulupirira kungawasonkhezere kuyamba kulambira koona tsiku lina.—1 Pet. 3:1, 2.
13 Kukhala wosamala mwateokalase kumabala zipatso zabwino zochuluka, kaya tikuchita ndi anthu wamba, abale ndi alongo athu auzimu, kapena a m’banja lathu lenilenilo. Kumamveka kokoma kwa womvetserayo, monga mmene ikunenera Miyambo 16:24 kuti: “Mawu okoma ndiwo chisa cha uchi, otsekemera m’moyo ndi olamitsa mafupa.” Choncho, yesetsani kukhala wosamala, posonkhezeredwa ndi chilakolako champhamvu chofuna kupindulitsa munthu aliyense amene mukumana naye.