Phunziro 15
Kuwafika Pamtima Omvetsera Anu
1-4. N’chifukwa chiyani mtima uli wofunika kwambiri kwa ife monga atumiki a Yehova?
1 Mtumwi Paulo sanaleke kuwapempherera kwa Yehova aja amene anawalalikira uthenga wabwino, kuti ‘maso a mtima wawo aŵalitsike.’ (Aef. 1:16-18) Onani kuti Paulo panopa analankhula za kuŵalitsidwa kwa mtima, osati maganizo. Kodi anatanthauza chiyani? Kuti tikhale olankhula nkhani ndi aphunzitsi ogwira mtima, tifunikira kuzindikira mfundo imeneyi.
2 Kudzera mwa Paulo, mzimu wa Yehova unavumbula zofananazo zimene unanena kudzera mwa atumiki ake okhulupirika a Woyesa mitima wamkuluyo. (Miy. 21:2) Mwachitsanzo, kwa woloŵanyumba wake wokhulupirika, Mfumu yokalamba Davide inapereka uphungu wabwino uwu: “Mwana wanga, um’dziŵe Mulungu wa atate wako, um’tumikire ndi mtima wangwiro ndi moyo waufulu; pakuti Yehova asanthula mitima yonse, nazindikira zolingirira zonse za maganizo; ukam’funafuna Iye udzam’peza, koma ukam’siya Iye adzakusiya kosatha.” (1 Mbiri 28:9) Kulambira koona kochokera mumtima n’kumene kumakondweretsa Mlengiyo.
3 Davide Wamkulu, Yesu Kristu, anapereka uphungu wanzeru wofananawo pamene anaphunzitsa kuti: “Uzikonda Ambuye Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse, ndi mphamvu yako yonse.” (Marko 12:28-30) Ponena za kukondweretsa Mulungu, chimene chili mu mtima wa munthu ndicho chimakhala chofunika kwambiri. Tikazindikira chimenecho, mawu a Miyambo 4:23 adzakhala ndi tanthauzo lamphamvu yokulirapo kwa ife: “Chinjiriza mtima wako koposa zonse uzisunga; pakuti magwero a moyo atulukamo.”
4 Nkhani imeneyi yofika pamtima ndi kukopa mtima wa womvetsera wina aliyense iyenera kukhala yofunika kwambiri kwa onse amene amalalikira ndi kuphunzitsa za uthenga wabwino wa ufumu wa Mulungu. Ndi nkhani yofunika kwa kholo lachikristu pophunzitsa ana ake, ndi kwa mlaliki aliyense amene amachititsa phunziro la Baibulo lapanyumba kwa aja amene adzamvetsera uthenga wabwino. Abale amene amaphunzitsa kupulatifomu ayenera kupenda nkhaniyi mosamalitsa. M’mikhalidwe yonse yoteroyo m’pofunika kuti tiyesetse kuloŵetsa uthenga wamtengo wapatali wa choonadi m’maganizo a ena. Komabe tifunikira kuchita zoposerapo. Tiyenera kuwafika pamtima. Timafuna kukopa ena kuti ‘apatse mtima wawo kwa Atate wamkulu wakumwamba.’—Miy. 23:26.
5, 6. N’chifukwa chiyani tiyenera kuyesetsa zoposerapo m’malo mongoloŵetsa chidziŵitso m’maganizo a anthu ena?
5 Kulekanitsa maganizo ndi mtima. Mphunzitsi waluso wa uthenga wabwino akhoza kuloŵetsa chidziŵitso m’maganizo mwa omvetsera. Posakhalitsa wophunzira kapena womvetserayo amakhala wokhoza kubwereza ndi kufotokoza yekha zimene waphunzitsidwazo. Amakhala atazimvetsetsa ndipo zimakhomerezeka m’maganizo mwake. Koma mafunso amabukapo, Kodi iye adzatani nacho chidziŵitsocho? Kodi amangofuna kupeza chidziŵitso, kapena kodi chidziŵitsocho chidzam’limbikitsa kuchitapo kanthu?
6 Apa tsopano mpamene mtima umaloŵerapo, pakuti Baibulo limanena kuti mtima ndiwo umasonkhezera munthu. Wolambira Mulungu weniweni anganene mawu a wolemba Baibulo wina wouziridwa kuti: “Ndinawabisa mawu anu mumtima mwanga, kuti ndisalakwire Inu.” (Sal. 119:11) Munthu atha kuloŵetsa chidziŵitso chopambana chonena za zolinga za Mulungu m’maganizo mwake, akhoza kumvetsa bwino lomwe mapulinsipulo abwino a Baibulo, komabe n’kutheka kuti mtima wake osam’sonkhezera m’pang’ono pomwe kuti agwiritse ntchito mapulinsipulo amenewo ndi chidziŵitso chonsecho pa moyo wake. Anthu ambiri amva ziphunzitso zotsitsimutsa za choonadi cha Mawu a Mulungu, koma zimakanika kuti agwiritse ntchito ziphunzitsozo pamiyoyo yawo, kapena kuti apereke mwayi wofananawo kwa anthu enanso, chifukwa amakhala alibiretu mtima woti agwire ntchito imeneyo yopulumutsa miyoyo.
7, 8. Sonyezani kulekana kumene kulipo pakati pa maganizo ndi mtima.
7 M’pofunikira kuti maganizo alandire chidziŵitso ndi kuchisanthula. M’maganizo ndimo mumachokera nzeru, ndimo m’likulu mosanthulira chidziŵitso. Maganizo amasonkhanitsa chidziŵitso, ndipo pambuyo pochilingalira ndi kuchipenda bwino amafika pa zosankha zakutizakuti. Ndipo Malemba amasonyeza kuti m’njira inayake, maganizo amagwirizana mwachindunji ndi mtima. Mtima uli ndi ntchito yaikulu, pakuti mumtimamo ndimo mumachokera chikondi ndi chisonkhezero. Mmene mtima wa munthu umatsogolera moyo wake wonse zimaonekera kwa anthu ena. Potsirizira pake iwo amadziŵa chimene munthuyo ali m’kati mwake. Koma Yehova nthaŵi zonse amadziŵa “munthu wobisika wamtima.”—1 Pet. 3:3, 4.
8 Nthaŵi zina mtima unganyalanyaze zosankha za maganizo, ukumapereka chisonkhezero chimene chimalimbikitsa ndi kukulitsa chilakolako kapena chikhumbo chake m’malo mwa kalingaliridwe kanzeru. Munthu sangofunikira kudziŵa ndi maganizo ake chimene chili choyenera pamaso pa Yehova, koma afunikiranso kukhala ndi chilakolako mumtima mwake choti achite choyeneracho. Luso la mtima limeneli losankhapo chimodzi pa zofuna zambiri limasonyeza chifukwa chake Baibulo limanena kuti mtima wa munthu ‘umapanga zolingalira’ ndi kuti ‘umalingalira [kusumika maganizo ake pa] njira zake.’ (Miy. 19:21; 16:9) Kupatulapo ngati mikhalidwe iwaletsa kutero, anthu ambiri amachita zinthu zokonda mitima yawo. Zimenezi zili choncho makamaka pankhani za makhalidwe ndi zauzimu.—Mat. 5:28.
9, 10. Kodi chingatithandize n’chiyani kufika pamtima wa wophunzira?
9 Kufika pamtima. Nangano ndi motani mmene mphunzitsi wachikristu angafikire mitima ya anthu? Njira imodzi ndiyo mwa kusonkhezera ophunzirawo kusinkhasinkha moyamikira zinthu zimene aziphunzira. Kumbukirani mmene akum’simbira Mariya, amayi wa Yesu wom’bereka, kuti iye “anasunga zinthu izi zonse mumtima mwake.” (Luka 2:51) Nkhaniyo sikunena kuti anazisunga “m’maganizo mwake,” ngakhale kuti maganizonso anachitapo mbali. Anasungira zinthuzo mumtima mwake, gwero la chikondi ndi chisonkhezero, n’chifukwa chake pambuyo pake anakhala Mkristu wokhulupirika. Kuti muthandize ophunzira lerolino kuloŵetsa choonadi m’mitima mwawo, pezani nthaŵi yokwanira yoti mufotokoze mfundo zazikulu m’njira yokhutiritsa. Musayese kuphunzitsa mfundo zochuluka kwambiri.
10 Mafunso amathandiza pofuna kudziŵa ngati choonadi cha Baibulo chimene mumakambirana chikuzika mizu m’mitima ya ophunzira. Mutakambirana mfundo zatsopano za choonadi mungafunse kuti, “Kodi tsopano mukuganiza bwanji pa zimenezi? Kodi n’zimene mumakhulupirira?” Yesani kuchita zimenezo pamene mulankhula nkhani za ophunzira. Popanda kudziŵa zimene zili mumtima wa munthu, sitingathe kum’thandiza kupita patsogolo mu utumiki wa Yehova.
11. Kodi tingagogomeze motani kwa wophunzira za kufunika kwa unansi wake ndi Yehova?
11 Kuti mukhomereze Mawu a Mulungu pamtima pawo, mufunikira kuthandiza ophunzira anuwo kuganizira za unansi wawo ndi Yehova. Nanga ndi malo ati abwino kwambiri amene mungaphunzirire kukulitsa luso limeneli koposa m’nkhani zanu za m’Sukulu Yateokalase? Limbikitsani amene mumawaphunzitsawo kudalira Yehova ndi mtima wawo wonse, chifukwa chom’konda iye, ndi chifukwa cha kutikonda kwake. Mwa mafunso olingaliridwa bwino, mutha kuwathandiza kuzindikira kuti zimene akuziphunzira m’Baibulo n’zochokera kwa Mlengi wathu wachikondi, Yehova, amene “ali wodzala chikondi, ndi wachifundo.” (Yak. 5:11) Mlungu ndi mlungu, ngati mukuchititsa phunziro, gogomezani za chikondi ndi nzeru za Yehova monga zikuonekera m’choonadi chodabwitsa chimene mukuphunzira pamodzi. Limbikitsani ophunzirawo kuona mmene miyoyo yawo ikukhudzidwira ndi mmene idzakhudzidwira m’masiku a m’tsogolo. Kambiranani mapulinsipulo a Baibulo kaŵirikaŵiri kotero kuti awazoloŵere. Athandizeni kukulitsa chizoloŵezi chomafuna kutsimikiza za chifuniro cha Atate wakumwamba m’nkhani iliyonse asanapange chosankha. Pang’onopang’ono mudzawathandiza kuzindikira kuti miyoyo yathu ndi chilichonse chimene tili nacho n’za Mulungu, pakuti “Iye mwini apatsa zonse moyo ndi mpweya ndi zinthu zonse”; ndi kuti kum’lambira iye, ndi kum’tumikira, ziyenera kukhala zinthu zofunika kopambana mumtima ndi m’maganizo mwathu.—Mac. 17:25.
12-14. Kodi ophunzira afunikira kudziŵanji za cholinga cha munthu pochita chinthu, ndipo munthu angapende motani zolinga zake?
12 Nthaŵi ndi nthaŵi m’pofunika kukumbutsa mfundo yakuti kwa Mulungu, chimene chili kanthu si chimene tichita chokha, komanso cholinga chathu pochita chinthucho. Iye amafuna kuti tizikondwera pochita chifuniro chake. Mofanana ndi tate wa m’buku la Miyambo, Atate wathu wakumwamba akutilangiza kuti: “Mwananga, tamvera mawu anga; tcherera makutu ku zonena zanga. Asachoke ku maso ako; uwasunge m’kati mwa mtima wako. Pakuti ali moyo kwa omwe awapeza, nalamitsa thupi lawo lonse.”—Miy. 4:20-22.
13 Choncho mukhoza kulimbikitsa aja amene mumaphunzitsa kuti aziganizira zolinga zawo pochita zinthu ndi kumadzifunsa okha kuti: Kodi cholinga changa n’chiyani pofuna kuchita ichi kapena chija? Kodi chikundilimbikitsa n’chiyani posankha njira imeneyi ya kachitidwe? Ndikudziŵa zimene maganizo anga akunena, koma kodi zili mumtima mwanga n’zotani makamaka? Kodi pamenepa ndikufuna kukondweretsa Mulungu kapena kungokhutiritsa zofuna zanga? Kodi maganizo angaŵa alidi oona mtima? Kapena kodi ndikungodzinyenga ndekha ndi malingaliro olakwika?
14 Mukhozanso kuchenjeza ophunzira anu za ngozi kapena mbuna zimene zingagwetse osasamala. Mwachitsanzo, munthu angaike kwambiri mtima wake pa cholinga chinachake, mwina choyenera mwa icho chokha, koma chimene chimadodometsa kulambira kapena kutumikira kwake Yehova pamlingo wakutiwakuti. Mwambi wouziridwa umanena mwatchutchutchu kuti: “Wokhulupirira mtima wakewake ali wopusa; koma woyenda mwanzeru adzapulumuka.”—Miy. 28:26.
15-17. Kodi chitsanzo cha Yesu ndi makambirano onena za pemphero zingaupindulitse motani mtima?
15 Chomalizira, m’pofunika kumafotokozera ophunzira athu chitsanzo chabwino chimene tili nacho mwa Ambuye Yesu. Iye anali wokhulupirika kwa Atate wake wakumwamba. Chifukwa chake n’chakuti ‘anakonda chilungamo, ndipo anadana nacho choipa: ndipo Mulungu anam’dzoza iye ndi mafuta a chikondwerero koposa ena onse.’ (Sal. 45:7) Kodi mtima wabwino woterowo anakhala nawo motani? Iye anaphunzira osati kum’dziŵa Mulungu kokha, komanso kum’kondweretsa. Nthaŵi zonse anakumbukira chifuniro cha Atate wake. Yesu nthaŵi zonse ankafunsira kwa Atate wake m’pemphero. Mwa mapemphero ake, kunali ngati amapempha Mulungu ‘kuti am’pende ndi kumuyesa, kuti ayeretse impso zake ndi kuyesa mtima wake.’ (Sal. 26:2) Iye sanafune kungodalira maganizo ake kapena zolakalaka za mtima wake. “Atate, . . . si chimene ndifuna Ine, koma chimene mufuna Inu,” ndilo linali pemphero la chosankha chake itayandikira imfa yonenedweratuyo yopereka nsembe.—Marko 14:36.
16 Kodi chimenecho si chitsanzo chabwino kwambiri chosonyeza ophunzira? Iwonso tingawathandize kufuna chitsogozo cha Mulungu m’miyoyo yawo mwa pemphero lochokera pansi pa mtima lopempha nzeru yoti atsate nayo njira imene Mulungu amavomereza. Aŵerengereni ena a mapemphero a Yesu. Pamene Yesu anabwera padziko lapansi anapemphera kwa Mulungu monga Mwana Wake. Pophunzitsa otsatira ake mmene angapempherere, Yesu anayamba pemphero lake lachitsanzo ndi mawu akuti: “Atate wathu wa Kumwamba.” (Mat. 6:9) Choncho popemphera munthuyo ayenera kukhala ngati mwana amene akulankhula kwa atate wake. Mapemphero ndi amene amasonyeza bwino mtundu wake wa unansi umene tili nawo ndi Yehova. Kodi unansi umenewo uli waubwenzi, wokhulupirirana, ndi wachikondi monga umene mwana amakhala nawo ndi atate amene amam’konda ndi mtima wonse? Kapena kodi wangokhala monga wa mnansi kapena mnzanu wamba amene mumangokambirana mukakumana? Yesetsani kufikira mitima ya anthu amene mumalankhula nawo ndi amene mumaphunzira nawo mwa kukambirana nawo za pemphero, mmene iwo amalionera ndi zinthu zimene amapempha.—Miy. 15:8, 29.
17 Chifukwa Mulungu amaona mitima kukhala yofunika kwambiri, ifenso tifunikira kuganizira kwambiri za mtima pophunzitsa Mawu ake. Kaya ndi polankhula nkhani yapoyera kapena ya wophunzira kapena pochititsa phunziro la Baibulo lapanyumba, cholinga chanu chisakhale kuphunzitsa zochuluka kwambiri. Dekhani kuti muthandize ena kuyandikira pafupi ndi Yehova kuti Mawu ake akhomerezeke zolimba mumtima mwawo.