Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • sg phunziro 18 tsamba 9-96
  • Kuwongolera Mayankho Anu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuwongolera Mayankho Anu
  • Buku Lolangiza la Sukulu ya Utumiki Wateokalase
  • Nkhani Yofanana
  • Dziŵani Mayankhidwe Oyenera
    Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
  • Kodi Mungayankhe Bwanji?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2009
  • Phunziro Limapindulitsa
    Buku Lolangiza la Sukulu ya Utumiki Wateokalase
  • Tamandani Yehova “Pakati pa Msonkhano”
    Nsanja ya Olonda—2003
Onani Zambiri
Buku Lolangiza la Sukulu ya Utumiki Wateokalase
sg phunziro 18 tsamba 9-96

Phunziro 18

Kuwongolera Mayankho Anu

1, 2. N’chifukwa chiyani tonsefe tiyenera kuyesetsa kumapereka mayankho abwino?

1 Akristu onse ayenera kukulitsa luso la kupereka mayankho abwino. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Mawu anu akhale m’chisomo, okoleretsa, kuti mukadziŵe inu mayankhidwe anu a kwa yense akatani.” (Akol. 4:6) Ndipo n’kwachibadwa kuyesetsa kupereka mayankho abwino. Pamene tiyankha bwino, timasangalala kwambiri. “Munthu akondwera ndi mayankhidwe a m’kamwa mwake; ndi mawu a panthaŵi yake kodi sali abwino?”—Miy. 15:23.

2 Kodi inuyo mumakhala nacho chidwi chofunika kuwongolera mayankho anu? Kodi muli wokhutira ndi kayankhidwe kanu pamisonkhano ya mpingo? Kapena kodi mukuona kuti mutapanga kuwongolera kwinakwake, mutha kupeza chimwemwe choŵirikiza? Mukakhala mu utumiki wakumunda, kodi zimakhalapo nthaŵi pamene muona kuti mkhalidwe winawake mukanachita nawo bwino kuposa mmene munachitiramo? Zimenezo zimatichitikira tonsefe, choncho n’kopindulitsa kuti tione mmene tingawongolere mayankho athu.

3, 4. Kodi mayankho osiyanasiyana angaperekedwe motani pafunso limodzi pamsonkhano?

3 Misonkhano ya mpingo. M’mipingo yambiri ya Mboni za Yehova, alipo anthu ena amene nthaŵi zonse amakhala okonzeka ndi mayankho pamafunso ofunsidwa paphunziro la Nsanja ya Olonda, paphunziro la buku la mpingo kapena pakubwereramo kwapakamwa m’Sukulu ya Utumiki Wateokalase. Zimenezi sikuti zimangochitika mwangozi. Iwo amatapa pa chidziŵitso chimene asonkhanitsa pazaka zambiri za kuphunzira ndi kusonkhana ndi anthu a Yehova; koma, nthaŵi zambiri, zimakhala choncho chifukwa cha kukonzekera kumene angokuchita posachedwa. Ngakhale ongoyamba kumene kusonkhana akhoza kupereka mayankho abwino ngati amaonetsetsa kuti akonzekera pasadakhale.—Miy. 15:28.

4 Ngati mwakhala woyamba kuyankha funso, m’pofunika nthaŵi zonse kuliyankha molunjika. Koma ngati wina wayankhapo kale pafunsolo, musaganize kuti nkhaniyo yathera pomwepo. Pakuti mwa kuwonjezera ndemanga pafunso limodzimodzilo, mutha kuchitapo chimodzi mwa zinthu izi: Kufutukula yankholo, kusonyeza mmene malemba m’ndimeyo akugwirizanira ndi yankholo, kapena kusonyeza mmene nkhaniyo imakhudzira miyoyo yathu. Ngati nkhaniyo ikunena za mikhalidwe yapadziko kapena machitidwe a zipembedzo zonyenga, mungafotokoze chokumana nacho china kapena mkhalidwe wakumaloko woikira umboni pazimene ndimeyo ikunena. Zimenezo zimaonetsa phindu lake la nkhaniyo.

5. N’chifukwa chiyani kuli kofunika kuyankha mwachidule komanso m’mawu anu?

5 Mayankho kaŵirikaŵiri amakhala atanthauzo kwambiri komanso ogwira mtima kwa omvetserawo pamene ali achidule ndi olunjika. Nthaŵi zambiri mayankho oterowo ndiwo amakhala oyenera. Pamene wina alankhula zambiri pofuna kukhudza mfundo zonse za m’ndimeyo, palibe chimene chimaonekera ndipo omvetserawo samaonapo yankho lenileni pafunsolo. Ndiponso, mayankho oikidwa m’mawu ake a woyankhayo, kaŵirikaŵiri amakhala othandiza kwambiri. Kuyankha m’njira imeneyi kumathandiza woyankhayo kupangitsa yankholo kumveka lakelake, ndipo mafotokozedwe akewo nthaŵi zambiri amathandiza ena kumvetsa mfundo zimene mwina m’mbuyomu samazimvetsa. Nkhani zanu mu Sukulu Yateokalase zimakuthandizani kukulitsa luso limeneli.

6. Kodi tingakulitse motani luso lokhala okonzekera ndi mayankho pamene funso lifunsidwa?

6 Kodi inunso mungalikulitse luso lomakhala wokonzekera ndi mayankho? Zimenezo zimafuna kukonzekera pasadakhale. Koma musakonzekere pamene ndime ikuŵerengedwa kapena pamene ena akuyankha, chifukwa mukatero simupeza phindu lenileni la msonkhanowo. Khalani ndi chizoloŵezi chomachongeratu mayankho anu. Ngati mwalemba mzera pansi pa mawu aakulu ochepa okha m’malo mwa masentensi ataliatali, pamenepo kungoyanga’ana mofulumira mawu aakulu amenewo kudzakukumbutsani lingalirolo ndipo mudzakhala wokonzekera kuyankha. Ngati funso pandime lagaŵidwa “a” ndi “b,” kuika chizindikiro m’mbalimo chosonyeza yankho la “a” ndi “b” kudzakuthandizani kusatsogolera wochititsa poyankha. Ngakhale ngati nkhaniyo ilibe mafunso okonzedweratu, ngati padzakhala kutengamo mbali kwa omvetsera kumakhalabe kothandiza kuchonga zimene muona kukhala mfundo zofunika. Mukatero mudzayankha mosavutika, ndipo mudzathandizira kukambiranako kukhala kwaumoyo. Mutayankha kamodzi pamsonkhano, musalekere pamenepo, ndi kuganiza kuti mutha kusiyira ena kuti ayankhe mafunso otsalawo. Khalani wofunitsitsa kuyankha mwaufulu.

7. N’chifukwa chiyani tonsefe tiyenera kuzindikira udindo wathu woyankhapo pamisonkhano?

7 Ena angakhale ndi mantha kuti ayankhe, akumaganiza kuti ena amayankha bwino kwambiri. Koma Baibulo limathandiza kuzindikira udindo wa aliyense wa kutengamo mbali. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Tigwiritse chivomerezo chosagwedera cha chiyembekezo chathu, . . . Ndipo tiganizirane wina ndi mnzake kuti tifulumizane ku chikondano ndi ntchito zabwino, osaleka kusonkhana kwathu pamodzi, monga amachita ena, komatu tidandaulirane.” (Aheb. 10:23-25) Mwa kuyankha timakhala tikumafulumiza ena ku chikondano ndi ntchito zabwino, timawatonthoza mitima ndi kuwalimbikitsa. Tikatero, ifenso timapindula, pakuti timapeza chimwemwe chochokera m’kupatsa komanso timalimbikitsidwa ife eni.

8-12. Perekani maganizo a mmene tingayankhire otsutsa mu utumiki wakumunda.

8 Kuyankha otsutsa mu utumiki wakumunda. Mudzapeza kuti n’kosavuta kuyankha mafunso mu utumiki wakunyumba ndi nyumba ngati mumachita phunziro laumwini nthaŵi zonse ndi kufika pamisonkhano mokhazikika. Koma ngati simudziŵa yankho pafunso limene lafunsidwa, musazengereze kuuza mwininyumbayo kuti simukudziŵa. Ndiyeno lonjezani kukafufuza yankholo kuti mukabwere nalo. Ngati munthuyo ali woona mtima, adzakondwa kuti muchite zimenezo.

9 Kuwonjezera pamafunso oterowo, nthaŵi zina mungakumane ndi otsutsa. Kodi mungawayankhe motani? Musanayankhe n’kothandiza choyamba kudziŵapo kanthu kena za maganizo a munthuyo. Mungafunse chimene chikum’pangitsa kuti atsutse. Mwachitsanzo, munthu wina angakane ndi kunena kuti anamva kuti inuyo simukhulupirira Kristu, pamene kwenikweni sakumvetsa chifukwa chimene amakhulupirira Utatu. Ambiri amatsutsa chifukwa cha kusamvetsa bwino koteroko. Zikatero, m’pofunika kuti nonse aŵiri mumvetse tanthauzo la mawu ofunika kwambiri musanayambe kukambirana. Ndipo nthaŵi zina, zimenezi zingapereke yankho moti sipangafunikirenso kufotokoza zambiri pamfundoyo.

10 Ndiponso pamene wina anena mawu otsutsa, ndi bwino kutenga nkhaniyo monga yofunika kwa nonse aŵirinu, m’malo moti muyambe kupikisana. Choncho, m’malo moipidwa ndi kutsutsa kwakeko, kuoneni kukhala nkhani imene ikum’khudzadi mwininyumbayo. Pokumbukira chimenecho, mungamuuze kuti mwakondwera kuti iye wabweretsa nkhani imeneyo. Ioneni ngati kiyi yopitirizira kukambirana kwanu, imene ingatsegule maganizo a munthuyo kuti alandire choonadi cha Baibulo. Bwanji osayesa zimenezo m’sukulu yateokalase, mwa kumaphatikiza m’nkhani zanu mikhalidwe yoonetsa mmene mungayankhire otsutsa?

11 Nthaŵi zina pamene mulankhula ndi munthu woonetsa chidwi, munthu wina anganene mawu otsutsa ndi cholinga chofuna kusokoneza kukambirana kwanu. Zikakhala choncho, mungakankhire kwa wotsutsayo udindo wopereka umboni. Yesu Kristu anagwiritsa ntchito mafunso potseka pakamwa otsutsa amene anayesa kusokoneza ulaliki wake. (Mat. 22:41-46) Choncho ndi bwino kukumbukira kuti ndi udindo wa munthu wotsutsa nkhani kuikira umboni pazimene akunena. Mwachitsanzo, ngati mwininyumba akuuzani kuti: “Anthu inu simukhulupirira Utatu,” akumasonyeza kuti chikhulupiriro chimenecho n’chofunika kwa Akristu, munganene kuti: “Ndimakhulupirira zonse zimene Baibulo limaphunzitsa. Kodi mungandisonyeze m’Baibulo chifukwa chake ndiyenera kukhulupirira chiphunzitso chimenecho?” Pamenepo udindo wopereka umboni umakhala kwa munthuyo kuti achirikize zimene akunena kuti ndicho choonadi.

12 Yankho lamphamvu kwambiri lofunika kwa munthu aliyense wodzinenera kuti amakhulupirira Malemba ndilo lotengedwa mwachindunji m’Mawu a Mulungu. Limakhala lokhutiritsa kuposa lina lililonse limene ife enife tinganene. Komabe, nthaŵi zonse poyankha munthu khalani odekha komanso aulemu, mosasamala kanthu za khalidwe limene wofunsayo angaonetse. Izi ndizo zoyenera mtumiki wa Mulungu.

13, 14. Pamaphunziro a Baibulo apanyumba, kodi mafunso a wophunzira tiyenera kuchita nawo motani?

13 Pamaphunziro a Baibulo. Kaŵirikaŵiri pamaphunziro a Baibulo pamakhala mkhalidwe waubwenzi, womasuka ndi wolimbikitsa kukambirana kwabwino. Choncho, mutayankha funso la wophunzira, ndi chizoloŵezi chabwino kum’funsa ngati iye wakhutira. N’kutheka kuti mwina mfundo zina sanazimvetse kwenikweni. Ngati muli wosatsimikiza za yankho lina, m’pempheni kuti mukam’fufuzire. Ngati mukufuna kuti wina akuthandizeni, funsani kwa wofalitsa wina wachidziŵitso chochulukirapo. Kumbukirani kuti, pamene muthandiza wina kupeza chidziŵitso chozamirapo cha uthenga wa Baibulo mungakhale mukuyambitsa munthuyo kuyenda pamsewu wa ku moyo, monga mmene Filipo mlalikiyo anathandizira mdindo wa ku Aitiopiya mwa kuyankha mafunso ake.—Mac. 8:26-39.

14 M’kupita kwa nthaŵi kungakhale bwino kusayankha mafunso onse odzutsidwa paphunziro la Baibulo, koma kusunga ena kuti mudzawayankhe m’nkhani zina m’tsogolo. Ndiponso, pofuna kuthandiza wophunzirayo kupita patsogolo, ndi bwino kum’sonyeza mmene angapezere mayankho mwa kudzifufuzira yekha. Mungam’sonyeze zida zina zothandiza kuphunzira Baibulo monga maindekisi osonyezera mabuku a Sosaite kapena chaputala choyenera m’buku la Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. Ndiyeno dzam’funseni pambuyo pake kuti anapezanji, ndi zimene anamvapo. Udindo wanu si wakungoyankha mafunso ake ayi, onetsetsani kukula kwake kwauzimu.

15-18. Kodi tiyenera kuonetsa khalidwe lotani pamene atiitana kukayankha mafunso pamaso pa akuluakulu a boma?

15 Atakuitanani kukaonekera pamaso pa akuluakulu a boma. Pofotokoza nkhani ya kuzunzidwa, mtumwi Petro anati: “Mum’patulikitse Ambuye Kristu m’mitima yanu; okonzeka nthaŵi zonse kuchita chodzikanira pa yense wakukufunsani chifukwa cha chiyembekezo chili mwa inu, komatu ndi chifatso ndi mantha.” (1 Pet. 3:14, 15) Nthaŵi zina tingaitanidwe kuti tikadziyankhire pamaso pa makhothi a milandu kapena akuluakulu a zamalamulo amene ali ndi mphamvu zotifunsa zimene timakhulupirira ndi chifukwa chake timakhulupirira zimenezo. Mtumwiyo akulangiza kuti, “Mum’patulikitse Ambuye Kristu m’mitima yanu.” Tsimikizani kuti pansi pa mtima wanu mukupatsa Ambuye Yesu Kristu ulemu wopambana, malo opatulika, amene simuyenera kuwanyoza. Pamenepo nkhaŵa yonse idzakuchokerani. Ngati tikondweretsa Wodzozedwa wa Mulungu monga Mfumu ya dziko lonse lapansi, palibe chifukwa choti tivutike maganizo ndi mmene anthu a maudindo apamwambawo angachitire.

16 Komabe, molingana ndi langizo loperekedwa pa Aroma 13:1-7, khalani aulemu kwa awo okhala ndi ulamuliro. Ngakhale pamene wofunsayo akupereka chithunzi choonetsa kuti muli ndi zolinga zoipa kapena ngati alankhula moonetsa kuti amadana ndi Mboni za Yehova, musayankhe mwaukali. (Aroma 12:17, 21; 1 Pet. 2:21-23) Kumbukirani kuti muli pamenepo kuti mupereke umboni. Kodi n’kutheka kuti mwina mmodzi wa akuluakuluwo angalabadire? Kapena mwina angakhale ndi maganizo ofeŵerapo kulinga ku ntchito yolalikira? Lolani kuti khalidwe lanu ndi kalankhulidwe kanu zipereke chithunzi chabwino cha njira ya choonadi.—Mat. 10:18-20.

17 Nthaŵi zinanso kumakhala kwanzeru kungonena zochepa kwambiri. Mungafunikire kukankhira udindo wopereka umboni kwa otsutsawo, monga momwe anachitira mtumwi Paulo pom’zenga mlandu. (Mac. 24:10-13) Kapena mungangokhala chete. Imeneyi ingakhale njira yabwino koposa ngati anthu oipa angofuna kukukolani m’mawu kapena kukutonzani pamene alibe cholinga chenicheni chakuti mafunso awo ayankhidwe. (Luka 23:8, 9) Kapena, mungaone kukhala kwanzeru kungokhala chete ngati cholinga chawo ndi kuvulaza Mboni zinzanu kudzera mwa inu. Wamasalmo Davide anati: “Ndidzasunga pakamwa panga ndi cham’kamwa, pokhala woipa ali pamaso panga.” (Sal 39:1, 2) Makamaka m’mayiko kumene kuli chitsutso choopsa kwa Akristu oona n’kofunika kukhala okhoza kulekanitsa pakati pa “mphindi yakutonthola” ndi “mphindi yakulankhula.”—Mlal. 3:7.

18 Pothirira ndemanga pa luso la atumiki a Yehova loyankhira mafunso, nyuzipepala ina ya ku Britain inati: “Chilichonse chimene Mboni ichita chimakhala ndi chifukwa cha Malemba. Ndithudi, chiphunzitso chawo chachikulu ndicho kuzindikira Baibulo lonse kukhala loona kwathunthu. Ndipo m’mfundo imeneyi ndimo mwagona nyonga yawo yachiŵiri; yakuti iwo akhoza kuyankha mafunso onse.” Mawu a Mulungu ndi kuwadalira kwathu ndizo zimatipatsa luso limenelo la kuyankha mafunso amene athetsa nzeru anthu ambiri. Thamo ndi ulemu wonse zimapita kwa Iye. Koma mwa kuyesetsa kuwongolera mayankho athu timapereka ulemu waukulu kwambiri kwa Yehova, timawonjezanso chisangalalo chathu komanso timatsogolera ena m’njira yopezera mtendere ndi Mulungu.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena