Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • te mutu 8 tsamba 35-38
  • Mnansi Wabwino

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mnansi Wabwino
  • Kumamumvetsera Mphunzitsi Wamkuru’yo
  • Nkhani Yofanana
  • Phunziro la Kukhala Wokoma Mtima
    Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso
  • Nkhani ya Msamariya Imatithandiza Kudziwa Mnzathu Weniweni
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • Kaphunzitsidwe ka Yesu
    Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo
  • Kodi Kukhala “Msamariya Wachifundo” Kumatanthauza Chiyani?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
Onani Zambiri
Kumamumvetsera Mphunzitsi Wamkuru’yo
te mutu 8 tsamba 35-38

Mutu 8

Mnansi Wabwino

KODI INU mukumdziwa munthu ali yense amene ali ndi kaonekedwe ka khungu kosiyana ndi kanu?—M’malo ena kaonekedwe ka anthu ochuruka ndiko kakuda kapena kopfiira. M’malo ena pafupifupi munthu ali yense ali ndi khungu loyera. Iwo amabadwa otero.

Kodi iko kamakupangani kukhala abwinopo koposa anthu ena ngati inu muli ndi kaonekedwe kena ka khungu koposa iwo?—Kodi munthu wokhala ndi khungu lakuda ayenera kuganizira kuti iye ali bwinopo koposa munthu wina amene khungu lache liri loyera? Kapena kodi munthu wina wokhala ndi khungu loyera ayenera kuganizira kuti iye ali bwinopo koposa munthu amene khungu lache liri lakuda? Kodi inu mukuganiza bwanji?—

Ngati ife timumvetsera Mphunzitsi Wamkuru, Yesu Kristu, ife tidzakhala okoma mtima kwa munthu ali yense. Sikumapanga kusiyana kuli konse kaya munthu angachokere mu mtundu wotani kapena kaya kaonekedwe ka khungu lache kali kotani. Ife tifunikira kuwakonda anthu a mitundu yonse. Ichi ndicho chimene Yesu anachipunzitsa.

Tsiku lina Myuda wina anafika kudzamufunsa Yesu funso lobvuta. Munthu ameneyu anaganizira kuti Yesu sakalidziwa yankho. Iye anati: ‘Kodi nchiani chimene ine ndiyenera kuchita kuti ndikhale ndi moyo kosatha?’

Limeneli linali funso lapafupi kwambiri kwa Mphunzitsi Wamkuruyo. Koma m’malo mwa kumaliyankha ilo yekha, Yesu anamfunsa munthuyo kuti: ‘Kodi nchiani chimene lamulo la Mulungu limanena kuti ife tiyenera kuchita?’

Munthuyo anayankha kuti: ‘Lamulo la Mulungu limati, “Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndipo uzikonda mnansi wako monga iwe mwini.”’

Yesu anati: ‘Mwayankha bwino. Pitirizanibe kumachita chimenechi ndipo inu mudzaupeza moyo wamuyaya.’

Koma munthuyo sanafune kumkonda munthu ali yense. Chotero iye anayesayesa kupeza chodzikhululukira nacho. Iye anamufunsa Yesu kuti: “Kodi ndani amene kwenikweni ali mnansi wanga?” Kodi inuyo mukanaliyankha motani funso limenelo? Kodi ndani amene kwenikweni ali mnansi wanu?—

Munthu ameneyu angakhale atafuna kuti Yesu anena kuti: ‘Anansi anu ndiwo mabwenzi anu.’ Koma bwanji ponena za anthu ena? Kodi iwo ali anansi athunso?—

Kuti aliyankhe funsolo, Yesu ananena mwambi wina. Uwo unali wonena za Myuda wina ndi Msamariya wina. Umu ndi mmene uwo unanenedwera:

Munthu wina anali kumayenda mu mseu wochokera ku mzinda wa Yerusalemu kunka ku Yeriko. Munthu ameneyu anali Myuda. Pamene iye analinkuyenda, achifwamba anamgwira iye. Iwo anamkantha nagwa pansi, ndi kutenga ndarama zache ndi zobvala zache. Achifwambawo anammenya iye ndi kumsiya iye m’mbali mwa mseuwo atakomoka.

Nthawi yaifupi pambuyo pache wansembe wina anadzeranso mseu womwewo. Iye anamuona munthu amene anali wobvulazidwa kwambiri. Kodi nchiani chimene iye anachichita? Kodi nchiani chimene inuyo mukanachichita?—

Wansembeyo anangolambalala ku mbali ina ya mseuwo. Iye sanaime nkuima komwe. Iye sanachite konse chinthu chiri chonse kumthandiza munthuyo.

Ndiyeno munthu wina wokonda chipembedzo kwambiri anadzera mseuwo. Iye anali Mlevi, amene anatumikira mu kachisi mu Yerusalemu. Kodi iye akaima kuti athandize? Iye anachita chinthu chimodzimodzicho monga anachita wansembeyo. Iye sanapereke chithandizo chiri chonse. Kodi chimenecho chinali chinthu choyenera kuchita?—

Potsirizira pache Msamariya wina anadzera mseuwo. Iye anamuona Myudayo ali gone pamenepo wobvulazidwa kwambiri. Tsopano, Asamariya ndi Ayuda ambiri sanakondane wina ndi mnzache. Chotero kodi Msamariya ameneyu akamsiya munthuyo popanda kumamthandiza iye? Kodi iye akanena mu mtima mwache kuti: ‘Kodi nchifukwa ninji ndiyenera kumthandiza Myuda ameneyu? Iye sakanandithandiza ine ngati ndikanabvulala’?

Eya, Msamariya ameneyu anamyang’ana munthu womagona m’mbali mwa mseuyo, ndipo iye anamumvera iye chisoni kwambiri. Iye sanathe kumsiya iye ndi kumlola iye kufa.

Chotero Msamariyayo anatsika pa nyama yache. Iye anapita kwa munthuyo, ndi kuyamba kumawasamalira mabala ache. Iye anathira pa iwo mafuta ndi vinyo. Zimenezi zikawathandiza mabalawo kupola. Ndiye iye anawamanga mabalawo ndi nsaru.

Msamariyayo mosamala anamnyamulira munthu wobvulazidwayo pa nyama yache. Ndiyeno iye anayenda pang’onopang’ono kufikira iye anafika ku nyumba yodyera, kapena hotela laling’ono. Panopo Msamariyayo anapeza malo kaamba ka munthuyo kuti akhale, ndipo iye anamsamalira iye bwino lomwe.

Tsopano Yesu anamfunsa munthuyo amene iye anali kulankhula naye kuti: ‘Kodi ndi uti wa anthu atatu amenewa amene inuyo mukuganiza kuti anali mnansi wabwino?’ Kodi inuyo mukanayankha motani? Kodi anali wansembeyo, Mleviyo kapena Msamariyayo?—

Munthuyo anayankha kuti: ‘Msamariyayo anali mnansi wabwino. Iye anaima ndi kumsamalira munthu wobvulazidwayo.’

Yesu anati: ‘Inu mwalondola. Chotero pitani ndi kuchita zimodzimodzizo inuyo.’—Luka 10:25-37, NW.

Kodi umenewu sunali mwambi wabwino kwambiri?—Umamveketsa bwino amene ali anansi athu. Anansi athu sali kokha mabwenzi athu a pa mtima. Anansi athu a m’dziko lathu, kapena anthu amene ali ndi kaonekedwe ka khungu kofanana ndi kamene ife tiri nako. Anansi athu ali anthu a mitundu yonse.

Chotero ngati inu mumuona munthu wina atabvulala, kodi nchiani chimene mudzachichita?—Bwanji ngati munthuyo ali wochokera m’dziko lina kapena ali ndi kaonekedwe ka khungu kosiyana ndi kanu?—Iye ali chikhalirebe mnansi wanu. Chotero inu muyenera kumthandiza iye. Ngati muona kuti muli ang’ono kwambiri kuti simungathe kuthandiza, pamenepo mungathe kundifunsa ine kuti ndithandize. Kapena inu mungathe kuitana mpolisi, kapena mphunzitsi wa pa sukulu. Kumeneko ndiko kumakhala ngati Msamariyayo.

Mphunzitsi Wamkuruyo amatifuna ife kukhala okoma mtima. Iye amatifuna ife kuwathandiza ena, mosasamala kanthu za amene iwo angakhale. Chimenecho ndicho chifukwa chache chimene iye anausimbira mwambi wonena za munthu amene anali mnansi wabwino.

(Ponena za nkhani iyi ya mmene ife tiyenera kuwaonera anthu a mafuko ndi mitundu ina, werenganiso Machitidwe 10:34, 35; 17:26; Mateyu 5:44-48.)

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena