Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • te mutu 12 tsamba 51-54
  • Anayesedwa ndi Mdierekezi

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Anayesedwa ndi Mdierekezi
  • Kumamumvetsera Mphunzitsi Wamkuru’yo
  • Nkhani Yofanana
  • Tifunika Kukana Ziyeso
    Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso
  • Zimene Yesu Anachita Atayesedwa
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • “Tsutsani Mdyerekezi” Monga Anachitira Yesu
    Nsanja ya Olonda—2008
  • Kuphunzira Kuchokera Kuziyeso za Yesu
    Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
Onani Zambiri
Kumamumvetsera Mphunzitsi Wamkuru’yo
te mutu 12 tsamba 51-54

Mutu 12

Anayesedwa ndi Mdierekezi

KODI munthu wina ali yense anayamba wakufunsani inu kuchita kanthu kena kamene kanali kolakwa?—Kodi iye anakulimbikitsani inu kukachita iko? Kapena kodi iye ananena kuti kukakhala kokondweretsa ndi kuti sikukakhala kwenikweni kulakwa kukachita iko?—Pamene munthu amachita chimenechi kwa ife, iye ali kumayesayesa kutiyesa ife.—

Kodi nchiani chimene ife tiyenera kuchita pamene ife tiri kumasyesedwa? Kodi tiyenera kugonjera ndi kuchita chimene chiri cholakwa?—Chimenecho sichikamkondweretsa Yehova Mulungu. Koma kodi mukumdziwa amene chikamkondweretsa?—Satana Mdierekezi.

Satana ali Mdani wa Mulungu ndipo iye ali mdani wathu. Ife sitingamuone iye, chifukwa chakuti iye ndi mzimu. Koma iye angathe kutiona ife. Tsiku lina Mdierekezi analankhula ndi Yesu, Mphunzitsi Wamkuruyo, ndipo anayesayesa kumuyesa iye. Tiyeni tichione chimene Yesu anachichita. Pamenepo ife tidzachidziwa chinthu choyenera kuchichita pamene ife tikuyesedwa.

Yesu anali atapita ku mapiri kukapemphera kwa Mulungu. Iye anafuna kuganizira za nchito imene Mulungu anampatsa iye kuichita.

Pamene Yesu anali kumeneko m’mapirimo, masiku ndi mausiku makumi anai anatha! Nthawi yonseyi Yesu sanadye kanthu kali konse. Yesu tsopano anali ndi njala kwambiri.

Imeneyi ndiyo nthawi pamene Satana anayesayesa kumyesa Yesu. Mdierekeziyo anati: “Ngati inu muli mwana wa Mulungu, uzani mwala uwu usanduke mtanda wa mkate.” Ha, ndi motani nanga mmene mkate ukanakomera!

Koma kodi Yesu akadatha kuusandutsa mwala kukhala mtanda wa mkate?—Inde, iye akadatha. Pakuti Yesu ali Mwana wa Mulungu. Iye ali ndi mphamvu zapadera.

Kodi inuyo mukanaupanga mwalawo kukhala mtanda wa mkate ngati Mdierekeziyo akadakufunsani inu kuchichita icho?—Yesu anali ndi njala. Chotero kodi kukanakhala koyenera kukuchita iko kamodzi kokha?—Yesu anadziwa kuti kukakhala kolakwa kuzigwiritsira nchito mphamvu zache m’njira imeneyi. Yehova anampatsa iye mphamvu zimenezi kuwaitanira nazo anthu kwa Mulungu, osati kuzigwiritsira nchito izo pa iye mwini.

Chotero, m’malo mwache, Yesu anamuuza Satana kuti kwalembedwa m’Baibulo kuti: ‘Munthu ayenera kukhala ndi moyo, osati ndi mkate wokha, koma ndi mau ali onse amene amaturuka pa kamwa pa Yehova.’ Yesu anadziwa kuti kumachita chimene chimamkondweretsa Yehova kuli kofunikadi kwambiri koposa kumakhala ndi chakudya kuti adye.

Koma Mdierekeziyo anayesa kachiwiri. Iye anamtengera Yesu mu Yerusalemu ndipo anamuimika iye pa mbali yaitali ya kachisiyo. Pamenepo Mdierekeziyo anati kwa Yesu: ‘Ngati inu muli mwana wa Mulungu, dziponyeni nokha pansi kuchokera pano. Pakuti kwalembedwa kuti angelo a Mulungu adzakuwakhani kuti musadzipweteke.’ Kodi nchiani chimene Yesu anachichita?—

Kachiriwirinso, Yesu sanamumvere Satana. Iye anamuuza Satanayo kuti kunali kolakwa kumuyesa Yehova mwa kumauseweretsa moyo wache.

Komabe Satana sanaleke. Iye anamtengera Yesu ku phiri lalitari kwambiri. Iye anamsonyeza iye maufumu onse a dziko lapansi ndi ulemelero wao. Ndiyeno Satana anati kwa Yesu: ‘Zinthu zonsezi ndidzakupatsani ngati mugwada ndi kuchita kachitidwe ka kulambira kwa ine.’ Kodi inuyo mukanachitanji?—

Yesu sanakuchite uko. Iye anadziwa kuti kukakhala kulakwa kumlambira Mdierekezi mosasamala kanthu za zimene iye akazilandira. Chotero Yesu anati kwa Mdierekeziyo: ‘Choka, Satana! Pakuti Baibulo limati, Ndiye Yehova Mulungu wako yekha amene uyenera kumlambira ndipo uyenera kumtumikira iye yekha.’—Luka 4:1-13; Mateyu 4:1-10, NW.

Ife timayang’anizananso ndi ziyeso. Kodi mukudziwa motani?—Nachi chitsanzo.

Mai wanu angapange pae yokoma kwambiri kapena keke kaamba ka chakudya cha usana. Koma iwo angakuuzeni kuti musadye chiri chonse cha izo kufikira pa nthawi ya chakudya. Inu mungakhale muli ndi njala kwambiri. Chotero inu mungaone kuti mtima uli dyokodyoko kuti mudye. Kodi mudzawamvera amai wanu?—Satana amafuna kuti inu musamvere.

Koma kumbukirani Yesu. Iye analinso ndi njala kwambiri. Koma iye anadziwa kuti kumkondweretsa Mulungu kunali kofunika kopambana.

Pamene inuyo mukusinkhuka pang’ono, kungakhale kwakuti ana ena adzakufunsani inu kumeza timibulu tina. Kapena iwo angakupatseni fodya kuti musute. Iwo angakuuzeni inu kuti zimenezi zidzakupangitsani inu kupezadi bwino. Koma zinthu zimenezi zingakhale mankhwala. Iwo angathe kukudwalitsani kwambiri, ndipo angathedi kukuphani. Kodi nchiani chimene mudzachichita?—

Kumbukirani Yesu. Satana anayesayesa kumchititsa Yesu kusewera ndi moyo wache mwa kumamuuza iye kulumpha pa kachisiyo. Koma Yesu sanachichite icho. Iye sanamumvere Satana. Ngakhalenso inu simuyenera kumumvera munthu ali yense amene amayesayesa kukuchititsani inu kumeza mankhwala.

Kuli kwapafupi kuchita chimene chiri choyenera pamene munthu ali yense ali kumachichita icho. Koma kungathe kukhala kobvuta kwambiri pamene ena ali kumayesayesa kutichititsa ife kuchita cholakwa. Iwo anganene kuti chimene iwo ali kumachichita sichiri choipa kwambiri. Koma funso lalikuru ndilo lakuti, Kodi nchiani chimene Mulungu amachinena ponena za icho? Iye amadziwa bwino kwambiri.

Chotero mosasamala kanthu za zimene ena amazinena, ife sitidzazichita zinthu zimene Mulungu amati siziri zoyenera. M’njira imeneyo ife masiku onse tidzampangitsa Mulungu kukhala wachimwemwe, ndipo sitidzamtumikira konse Mdierekezi.

(Chilangizo chabwino choonjezereka ponena za kuchikaniza chiyeso cha kuchita cholakwa chikupezeka pa Mateyu 26:41, Miyambo 22:24, 25 ndi Salmo 1:1, 2.)

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena