Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • te mutu 15 tsamba 63-66
  • Kapolo Wosakhululukira

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kapolo Wosakhululukira
  • Kumamumvetsera Mphunzitsi Wamkuru’yo
  • Nkhani Yofanana
  • Chifukwa Chake Tiyenera Kukhululukira Ena
    Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso
  • Phunziro la Kukhululukira
    Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
  • Phunziro m’Kukhululukira
    Nsanja ya Olonda—1988
  • Anawaphunzitsa Kufunika Kokhululukira Ena
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
Onani Zambiri
Kumamumvetsera Mphunzitsi Wamkuru’yo
te mutu 15 tsamba 63-66

Mutu 15

Kapolo Wosakhululukira

KODI munthu wina ali yense anayamba wakuchitirani kanthu kena kolakwa?—Kodi iye anakubvulazani kapena kukunenerani kanthu kena kosakhala bwino?—Chinakupangitsani inu kukhumudwa,—eti?

Pamene kanthu kena konga kameneko kachitika, kodi inu muyenera kumchitira munthu winayo m’njira yosakhala bwino imodzimodziyo imene iye amakuchitirani inu?—Anthu ambiri akatero.

Koma Mphunzitsi Wamkuruyo ananena kuti ife tiyenera kuwakhululukira awo amene amatilakwira ife. Kuti asonyeze mmene kuliri kofunika kwambiri kukhala wokhululukira, Yesu anawakambira iwo mwambi. Kodi mungafune kuumva uwo?—

Nthawi ina kunali mfumu. Iyo inali mfumu yabwino. Iyo inali yokoma mtima kwambiri. Iyo inkawakongoletsadi ndarama akapolo ache pamene iwo anafuna chithandizo.

Koma tsiku linafika pamene mfumuyo inafuna kuti ndarama zache zibwezedwe. Chotero iyo inawaitana akapolo ache amene anaikongola ndarama, niwafunsa iwo kuti aibwezere. Eya, munthu wina anaikongola mfumuyo ndarama zokwanira mamiliyoini makumi asanu ndi limodzi! Zimenezo ndi ndarama zochuruka kwambiri. Ndarama zochuruka koposa zimene ine ndakhala nazo m’moyo wanga wonse.

Kapolo ameneyu anali ataononga ndarama za mfumuyo ndipo analibe chiri chonse cha kubwezera nacho. Chotero mfumuyo inalamula kuti kapoloyo agulitsidwe. Mfumuyo inanenanso kuti agulitse mkazi wa kapoloyo ndi ana ache ndi chinthu chiri chonse chimene kapoloyo anali nacho. Ndiyeno mfumuyo inayenera kulipidwa ndarama zolandiridwa kuchokera ku malondawo. Kodi inuyo mukuganizira kuti chimenechi chinampangitsa kapoloyo kumva bwanji?—

Kapoloyo anaipempha mfumuyo kuti: ‘Chonde, musandichitire zimenezo. Ndiyembekezereni pang’ono, ndipo ndidzabweza chinthu chiri chonse chimene ndiri nanu ngongole.’ Ngati inuyo mukanakhala mfumuyo kodi mukanachitanji ndi kapoloyo?—

Mfumu yabwino inamumvera chisoni kwambiri kapolo wache. Chotero iyo inamuuza kapoloyo kuti iye sanafunikire kubweza ndaramazo. Iye sanafunikire kubweza iri yonse ya ndarama mamiliyoni makumi asanu ndi limodziwo! Ha, ndi motani nanga mmene chimenecho chinayenera kumpangitsira kukondwa kapoloyo!

Koma kodi nchiani chimene kenaka kapoloyo anachichita? Iye anapita nampeza kapolo wina amene anakongola kwa iye ndarama zana limodzi lokha. Zimenezo siziri ndalama zochuruka poyerekezeredwa ndi ndarama mamiliyoni makumi asanu ndi limodziwo. Munthuyo anamgwira kapolo mnzacheyo pa khosi nayamba kumkanyanga iye. Ndipo kapoloyo anati kwa iye: ‘Bweza ndarama zana limodzi zija zimene iwe unandikongola.’

Kodi inu mungamganizire munthu wina akumachita kanthu kena konga kameneko?—Kapoloyo anali atakhulululukidwa zochuruka ndi mfumu yabwinoyo. Ndipo tsopano iye anatembenukanso ndi kufuna kuti kapolo mnzacheyo abweze ndarama zana limodzi. Ichi sichinali chinthu chokoma mtima kuchichita.

Eya, kapolo amene anakongola ndarama zana limodzi zokhayo anali wosauka. Iye sakanatha kubweza ndaramazo nthawi yomweyo. Chotero iye anagwa pansi pa mapazi a kapolo mnzacheyo ndi kupempha kuti: ‘Chonde ndiyembekezereni pang’ono, ndipo ndidzabweza zimene ndiri nanu ngongole.’ Kodi munthuyo anayenera kumyembekezera pang’ono kapolo mnzacheyo?— Kodi inuyo mukanachita chimenecho?—

Eya, munthu ameneyu sanali wokoma mtima, monga umo inaliri mfumuyo. Chifukwa chakuti kapolo mnzacheyo sanathe kumlipira iye pomwepo, iye anamchititsa mnzacheyo kuponyedwa m’ndende. Iye ndithudi anali wosakhululukira.

Akapolo enawo anaziona zonsezi zikuchitika. Iwo anaiuza mfumuyo zonsezo. Mfumuyo inakhala yokwiya kwambiri ndi kapolo wosakhululukirayo. Chotero iyo inamuitana iye, niti: ‘Kapolo woipa iwe, kodi ine sindinakukhululukire zimene iwe unandikongola? Nanga, kodi sukanayenera kukhala wokhululukira kwa kapolo mnzako?’

Iye anayenera kukhala ataphunzira phunziro kuchokera kwa mfumu yabwinoyo. Koma iye sanaphunzire. Chotero tsopano mfumuyo inalamulira kuti kapolo wosakhululukirayo aponyedwe m’ndende kufikira iye atabweza ndarama mamiliyoni makumi asanu ndi limodzizo. Ndipo, ndithudi, m’ndende iye sakanatha konse kupeza ndarama zoti abweze. Chotero iye akakhalabe kumeneko kufikira iye atamwalira.

Pamene Yesu anamaliza kukamba mwambi umenewu, iye anati kwa otsatira ache: ‘M’njira imodzimodziyo Atate wanga wakumwamba adzachitanso ndi inu ngati inuyo ali yense payekha samkhululukira mbale wache kuchokera m’mitima yanu.’—Mat. 18:21-35, NW.

Mukuonatu, tonsefe tiri ndi ngongole kwambiri kwa Mulungu. Moyo wathu umachokera kwa Mulungu, koma chifukwa chakuti ife timachita zinthu zolakwa iye akanatha kuuchotsa uwo mwa ife. Ngati ife tikanayesa kumlipira Mulungu ndarama, m’nthawi yonse ya moyo wathu sitikadatha konse kupeza ndarama zokwanira kumlipira iye zimene ife tiri naye ngongole.

Anthu ena ali nafe ngongole yaing’ono kwambiri, poyerekezera ndi zimene ife tiri nazo ngongole kwa Mulungu. Zimene iwo ali nazo mangawa kwa ife ziri ngati ndarama zana limodzi zimene kapolo winayo anazikongola kwa winayo. Koma zimene ife tiri nazo mangawa kwa Mulungu ziri ngati ndarama mamiliyoni makumi asanu ndi limodzi zimene kapoloyo anazikongola kwa mfumuyo.

Mulungu ali wokoma mtima kwambiri. Ngakhale kuli kwakuti ife tachita zinthu zolakwa, iye adzatikhululukira ife. Iye sadzatichititsa ife kulipira mwa kumaichotsa miyoyo yathu mwa ife kosatha. Koma iye amatikhulululukira ife kokha ngati ife timkhulupilira Mwana wache Yesu, ndipo ngati ife tiwakhululukira anthu ena amene amatilakwira ife. Chimenecho ndicho kanthu kena kakukaganizira, ati?—

Chotero, pamene munthu wina achita kanthu kena kosakhala bwino kwa inu, koma kenaka iye anena kuti pepani, kodi nchiani chimene inu mudzachichita? Kodi inu mudzamkhululukira iye?—Bwanji ngati icho chichitika nthawi zambiri? Kodi inu mudzamkhululukirabe iye?—

Ngati ife tikanakhala munthu amene anali kumapempha kuti akhululukidwe, ife tikanafuna kuti munthu winayo atikhululukire ife, kodi sitikatero?—Ife tiyenera kumchitira iye chimodzimodzi. Ife sitiyenera kungonena kuti ife timkhululukira iye, koma ife tiyeneradi kumkhululukira iye kuchokera mu mtima mwathu. Pamene ife tichita chimenecho, ife timasonyeza kuti ife tikufunadi kukhala atsatiri a Yesu.

(Kukugogomezera kufunika kwa kumakhala wokhululukira, werenganinso Mateyu 6:14, 15, Luka 17:3, 4 ndi Miyambo 19:11.)

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena