Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • te mutu 17 tsamba 71-74
  • Anthu Awiri Amene Sananene Zoona

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Anthu Awiri Amene Sananene Zoona
  • Kumamumvetsera Mphunzitsi Wamkuru’yo
  • Nkhani Yofanana
  • Chifukwa Chake Tiyenera Kupewa Bodza
    Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso
  • Petulo ndi Hananiya Ananama, Kodi Tikuphunzirapo Chiyani?
    Nsanja ya Olonda—2013
  • Tizilankhula Zoona Zokhazokha
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2018
  • Kunama—Kodi Nthaŵi Zina N’kolungama?
    Galamukani!—2000
Onani Zambiri
Kumamumvetsera Mphunzitsi Wamkuru’yo
te mutu 17 tsamba 71-74

Mutu 17

Anthu Awiri Amene Sananene Zoona

BWANJI ngati mtsikana amlonjeza mai wache kuti, “Inde, ndidzafika pa nyumba nditangoweruka ku sukulu.” Koma kenaka ana ena ampempha iye kukhalabe ndi kusewera nawo. Kodi kukakhala kwabwino kukhala—kwa nthawi yaing’ono chabe?—

Kapena mwinamwache mnyamata awalonjeza atate wache kuti, “Ai, sindiponyanso mpira m’nyumba.” Kodi kukakhala kwabwino kukuchita iko kowerengeka chabe pamene atate wache sali kuona?—

Mphunzitsi Wamkuruyo anasonyeza chinthu choyenera kuchichita. Iye anati: ‘Ingowalolani mau anu akuti Inde atanthauze Inde, ndi Ai wanu, Ai; pakuti kanthu kena kali konse kali kochokera kwa woipayo.’—Mateyu 5:37, NW.

Kodi nchiani chimene Yesu anachitanthauza mwa chimenecho?—Iye anatanthauza kuti ife tiyenera masiku onse kuwasunga mapangano athu; ife tiyenera masiku onse kunena zoona.

Pali nkhani ina imene imasonyeza mmene kuliri kofunika kunena zoona. Iyo iri yonena za anthu awiri amene ananena kuti iwo anali ophunzira a Yesu.

Nthawi yaifupi pambuyo pa imfa ya Yesu, anthu ambiri anakhala ophunzira ache. Ena a anthu amenewa anadza ku Yerusalemu kuchokera ku malo akutali. Munomo kwa nthawi yoyamba iwo anamva za Yesu. Iwo anafuna kudziwa zochuruka. Monga choturukapo chache iwo anakhalabe m’Yerusalemu kotalikirapo koposa mmene iwo anayembekezelera. Ena a iwo ndarama zinawathera ndipo anafuna chithandizo kotero kuti iwo akanatha kugula chakudya.

Ophunzirawo m’Yerusalemu anafuna kuwathandiza iwo. Chotero, ambiri a ophunzira amenewa anagulitsa zinthu zimene iwo anali nazo ndipo iwo anadza nazo ndaramazo kwa atumwi a Yesu. Ndiyeno atumwiwo anapereka ndaramazo kwa anthu amene anazifunikira izo.

Wophunzira wina wochedwa Hananiya ndi mkazi wache Safira anagulitsa munda umene iwo anali nao. Palibe munthu ali yense amene anawauza iwo kuti iwo anafunikira kuugulitsa. Iwo anadzisankhira chimenecho okha. Koma chimene iwo anachichita sichinali chifukwa chakuti iwo anawakonda ophunzira atsopanowo. Kwenikweni, iwo anafuna kuwapangitsa anthu kuganizira kuti iwo anali abwinopo koposa ndi mmene iwo analiri kwenikweni. Chotero iwo anasankha kukupangitsa iko kuonekera ngati kuti iwo anali kumapereka ndarama zonse kuwathandiza ena. Koma kwenikweni anali kupita kukapereka kokha mbali ya izo ndi kusunga zinazo. Kodi nchiani chimene mukuganiza ponena za chimenecho?—

Eya, Hananiya anadza kudzawaona atumwi a Yesu choyamba. Iye anapereka ndaramazo kwa iwo. Koma Hananiya sanali kupereka ndarama zonse. Mulungu anachidziwa chimenechi. Chotero iye anamlola mtumwi Petro kudziwa kuti Hananiya sanali kumakhala woona. Atatero Petro anati:

‘Hananiya, kodi nchifukwa ninji iwe wamlola Satana kukuchititsa iwe kuchita chimenechi? Mundawo unali wako. Iwe sunafunikire kuugulitsa uwo. Ndipo ngakhale iwe utaugulitsa mundawo, zinali kwa iwe kusankha chimene iwe ukachita nazo ndaramazo. Koma kodi nchifukwa ninji iwe unayerekezera kupereka ndarama zonse pamene iwe unali kupereka kokha mbali ya izo? Mwa ichi iwe unali kunana, osati kwa ife tokha, koma kwa Mulungu.’

Zinali zoopsya motero. Hananiya anali kunama! Iye sanachichite chimene iye anachinena kuti iye adzachichita. Iye ndi mkazi wache anangoyerekezera kuchichita icho.

Baibulo limatiuza ife chimene chinachitika kenako. Ilo limati: ‘Pa kuwamva mau a Petro, Hananiya anagwa pansi namwalira.’ Mulungu anamkantha Hananiya! Mtembo wache unaturutsidwa kunja nukaikidwa.

Pafupifupi maora atatu pambuyo pache Safira mkazi wache analowa. Iye sanadziwe chimene chinali chitamchitikira mwamuna wache. Chotero Petro anamufunsa iye: ‘Kodi inu awirinu munagulitsa mundawo kuchuruka kwa ndarama zimene inu munatipatsa?’

Safira anayankha kuti: ‘Inde, ife tinaugulitsa mundawo kwa ndarama zochuruka motero.’

Koma limeneli linali bodza! Iwo anadzisungira okha zina za ndaramazo. Chotero Mulungu anamkanthanso Safira.—Machitidwe 5:1-11, NW.

Kodi inu mukuganizira kuti pali kanthu kena kamene ife tiyenera kukaphunzira kuchokera m’chimene chinamchitikira Hananiya ndi Safira?—Inde. Icho chimatiphunzitsa ife kuti Mulungu sanawakonda onama. Iye amatifuna ife masiku onse kunena zoona.

Anthu ambiri amanena kuti sikuli koipa kunena bodza. Iwo amanena mabodza pafupifupi tsiku liri lonse. Koma kodi inu mukuganiza kuti chimenecho chiri choyenera?—

Kodi munadziwa kuti matenda onse, kupweteka ndi imfa zimene ziri pa dziko lapansi zinadza chifukwa cha bodza?—Mdierekezi anamnamiza mkazi woyambayo Hava ponena za Mulungu. Monga choturukapo chache, iye analiswa lamulo la Mulungu. Kenako iye anamchititsa Adamu kuswanso lamulo la Mulungu. Tsopano iwo anali ochimwa, ndipo ana ao onse akabadwa ochimwa. Ndipo chifukwa cha uchimo iwo akabvutika ndi kufa. Kodi zonsezo zinayambika motani?—Ndi bodza.

Palibe kudabwa Yesu ananena kuti Mdierekezi “ali wabodza ndi atate wa bodza.” Iye anali woyambilira kunena bodza. Pamene munthu ali yense amanena bodza, iye ali kuchita chimene Mdierekezi anachichita. Ife tiyenera kuganizira za chimenechi ngati ife tiyamba kumva dyokodyoko kuti tinene bodza.—Yohane 8:44, NW.

Kawirikawiri kuli pamene munthu amachita kanthu kena kolakwa chakuti iye angamwe dyokodyoko kuti anene bodza za icho. Mwachitsanzo, inu mungaononge kanthu kena. Inu mungakhale musanalinge kuchita icho, koma chinthucho chaonongekabe. Kodi nchiani chimene inu muyenera kuchita?—Kodi inu muyenera kuyesa kuchibisa icho ndi kuyembekezera kuti palibe munthu ali yense amene adzadziwa?—

Ife tiyenera kumkumbukira Hananiya ndi Safira. Iwo anayesayesa kubisa zoona. Ndipo Mulungu anasonyeza mmene iko kunaliri koipa mwa kumawakantha iwo.

Chotero, mosasamala kanthu za chimene ife tingachichite, ife sitiyenera kunena bodza ponena za icho. Baibulo limati: “Lankhulani zoona.” Ilonso limati: “Musamanamizana wina ndi mnzache.” Yehova masiku onse amalankhula zoona, ndipo iye amatiyembekezera ife kuchita chimodzimodzi.—Aefeso 4:25; Akolose 3:9.

(Ife masiku onse tiyenera kunena zoona. Imeneyo ndiyo nsonga imene yanenedwa pa Eksodo 20:16; Miyambo 6:16-19; 14:5; 12:19; 16:6.)

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena