Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • te mutu 19 tsamba 79-82
  • Chikondi kaamba ka Abale ndi Alongo Athu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chikondi kaamba ka Abale ndi Alongo Athu
  • Kumamumvetsera Mphunzitsi Wamkuru’yo
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Abale Athu ndi Alongo Athu Ndani?
    Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso
  • Mwana Wabwino, ndi Woipa
    Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo
  • Kaini Anakwiya Mpaka Anapha M’bale Wake
    Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Anthu Aŵiri a Pachibale Amene Anali ndi Mitima Yosiyana
    Nsanja ya Olonda—2002
Onani Zambiri
Kumamumvetsera Mphunzitsi Wamkuru’yo
te mutu 19 tsamba 79-82

Mutu 19

Chikondi kaamba ka Abale ndi Alongo Athu

KODI inu muli ndi abale ndi alongo angati?—Si munthu ali yense amene ali ndi mbale kapena mlongo m’banja lache pa nyumba. Ngati inuyo muli ngakhale ndi mmodzi yekha, inu mungathe kukhala wothokoza.

Mulungu anatipanga ife kotero kuti ife timaona kukhala achibale kwenikweni kwa anthu ena. Ife tingakhale achibale kwenikweni kwa anthu ena. Ife tingakhale ndi mabwenzi ambiri, koma abale ndi alongo kawirikawiri amasamalirana wina ndi mnzache koposadi mmene mabwenzi amachitira. Pamene mmodzi ali m’bvuto, winayo amathandiza. Ameneyo ndiye mtundu wa mbale amene inuyo mukakonda kukhala naye, ati?—

Koma si munthu ali yense amene ali wabwino kwa mbale wache kapena mlongo wache. Baibulo limatiuza ife za munthu wina amene anammenya mbale wache. Kodi mukulidziwa dzina lache?—Iye anali Kaini, mwana wamwamuna wa munthu woyambilirayo.

Tsiku lina Kaini anatenga zakudya zina zimene iye anazilima monga mlimi. Iye anapanga mphatso kapena nsembe ya chakudya chimenechi kwa Yehova. Mbale wache Abele nayenso anapereka nsembe kwa Yehova. Abele anapereka kwa Mulungu nkhosa yabwino kopambana imene iye anali nayo. Mulungu anakondwera ndi Abele ndipo ndi nsembe yache. Koma iye sanali wokondwera ndi Kaini ndi nsembe yache.

Kodi nchifukwa ninji zinali choncho?—Sichinali chifukwa chakuti Abele anapereka zopambana. Ndipo sikunali kupereka kwache kokha nkhosa kumene kunapanga kusiyanako. Baibulo limatiuza ife kuti Mulungu angathe kuona chimene chiri m’mitima ya anthu. Iye amadziwa mmene ife timalingalirira m’kati mwenimweni m’mitima mwathu.

Kodi nchiani chimene Mulungu anachiona mu mtima mwa Kaina?—Iye anaona kuti Kaini sanamkonde kwenikweni mbale wache. Kaini anatha kuona kuti Yehova anali wokondwera ndi Abele ndi nsembe yache. Koma kodi Kaini anayesayesa kusintha kotero kuti iye akakhale ngati mbale wache?—Ai. Iye anakhala wokwiya.

Yehova anamuuza Kaini kuti iye ayenera kusintha njira zache. Koma Kaini sanamvetsere. Ngati iye akadamkondadi Mulungu, iye akadamvetsera iye. Koma iye sanamkonde Mulungu. Ndipo iye sanamkonde mbale wache.

Chotero, tsiku lina iye anati kwa Abele: “Tiye tipite kumunda.” Kaini anali ndi choipa mu mtima mwache, koma Abele sanachidziwe icho. Abele anapita limodzi ndi Kaini. Pamene iwo anali kumweko m’mundamo okha, Kaini anammenya mbale wache. Iye anammenya zolimba kwambiri chakuti iye anamupha iye. Kodi chimenecho sichinali choopsya?— —Genesis 4:2-8, NW.

Baibulo limatiuza ife kuti pamenepo pali phunziro lapadera lakuti ife tiyenera kuphunzira kuchokera m’chimenecho. Kodi mukulidziwa limenelo?—‘Uwu ndi uthenga umene inu mudaumva kuyambira pa chiyambi: ife tiyenera kukhala ndi chikondi kaamba ka wina ndi mnzache; osati ngati Kaini, amene anachokera mwa woipayo.’ Chotero abale ndi alongo ayenera kukhala ndi chikondi kaamba ka wina ndi mnzache. Iwo sayenera kukhala ngati Kaini.—1 Yohane 3:11, 12, NW.

Kodi nchifukwa ninji kukakhala koipa kwambiri kukhala ngati Kaini?—Chifukwa chakuti Baibulo limanena kuti iye ‘anachokera mwa woipayo.’ Popeza kuti Kaini anachita ngati Mdierekezi, kunali monga ngati kuti Mdierekezi anali atate wache. Taganizirani za chimenecho!

Kodi inu mukuchiona chifukwa chache kuli kofunika kwambiri kuwakonda abale ndi alongo anu?—Ngati inu simuwakonda iwo, kodi inu mudzakhala mwana wa yani?—Inu mukakhala mwana wa Mdierekezi. Inu simukafuna kukhala wotero, eti?—Chotero kodi ndi motani mmene inuyo mungasonyezere kuti inuyo mukufuna kukhala mwana wa Mulungu?—Kulidi mwa njira ya kuwakonda abale ndi alongo anu.

Koma kodi chikondi nchiani?—Chikondi ndicho lingaliro lamphamvu la m’kati limene limatipangitsa ife kufuna kuwachitira anthu ena zinthu zabwino. Ife timasonyeza kuti timawakonda ena pamene ife tiri ndi lingaliro labwino kulinga kwa iwo. Timachisonyeza icho pamene timawachitira iwo zinthu zabwino. Ndipo ngati ife timamkondadi munthu wina, kodi ife tidzaleka kumachita chabwino kwa iye kufikira iye choyamba atatichitira ife kanthu kena?—

Mulungu samachita chimenecho. Ngakhale ife tisanamkonde Mulungu, Mulungu anatikonda ife. Ife tingathe kuphunzira kuchokera m’chimenechi. Ngakhale ena asanasoyeze kutikonda ife, ife tingathe kusonyeza kuti ife timawakonda iwo.

Baibulo limanena kuti Akristu ali ndi abale ndi alongo ambirimbiri koposa chabe awo amene amakhala m’nyumba imodzimodziyo ndi iwo. Kodi inu mukuwadziwa amenewo?—Yesu anati: ‘Ali yense amene amachita chifuniro cha Atate wanga wa kumwamba ali mbale ndi mlongo wanga.’ Chimenecho chimatanthauza kuti onse amene amachita chifuniro cha Mulungu ali abale ndi alongo. Iwo ali banja lapadera la abale ndi alongo. Kodi mukuchidziwa chimenecho?— —Mateyu 12:50, NW.

Kodi inu mukawakonda abale ndi alongo onse m’banja lalikuru Lachikristu limeneli?—Yesu ananena kuti ife tiyenera kutero. Iye anati: ‘Munthu ali yense adzadziwa kuti inu muli ophunzira anga ngati inu mukondana wina ndi mnzache.’ Ife sitingathe kuwakonda owerengeka okha a iwo. Ife tiyenera kuwakonda abale ndi alongo athu onse.—Yohane 13:35, NW.

Kodi ndi motani mmene ife tingasonyezere kuti ife timawakondadi iwo?—Eya, ngati ife tiwakonda iwo, ife sitidzakhala patali ndi iwo chifukwa chakuti ife sitikufuna kulankhula nawo. Ife tidzakhala aubwenzi kwa iwo onse. Ife masiku onse tidzachita chabwino kwa iwo. Ndipo ngati iwo atakhala m’bvuto, ife tidzawathandiza, chifukwa chakuti tiridi banja lalikuru.

Pamene ife tiwakondadi abale ndi alongo athu onse, kodi icho chimasonyezanji?—Icho chimasonyeza kuti ife tiri ophunzira a Yesu, Mphunzitsi Wamkuruyo. Ndipo kodi chimenecho sindicho chimene ife tikufuna kukhala?—

(Kusonyeza chikondi kaamba ka abale ndi alongo athu kwafotokozedwanso pa 1 Yohane 4:8, 20, 21 ndi Agalatiya 6:10. Bwanji osatsegula Baibulo lanu ndi kuwawerenga malemba amenewo?)

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena