Mutu 26
Ana Amene Amatamanda Mulungu
KODI inu munayamba mwaima kuganizira chifukwa chache chimene inu muli ndi pakamwa? Kodi ndi motani mmene inu mumapagwilitsilira ipo nchito?—
Ndithudi kuli koona kuti ife tifunikira pakamwa podyera. Koma pakamwa sipali podyera pokha. Ochuruka a ife timadya nthawi zowerengeka chabe pa tsiku. Koma kodi sikuli koona kuti inu mumapagwiritsira nchito pakamwa panu kwambirimbiri kaamba ka kulankhula?—Milomo yanu, lilime lanu, mano anu, chidakadaka chanu, ndi zina zambiri, zonse zimachita mbali nthawi iri yonse imene inu mulankhula.
Tangoganizirani mmene zikanakhalira ngati inu simunali kutha kulankhula. Ha, ndi motani nanga mmene kukanakhalira kwachisoni ngati inuyo simukadatha konse kumuuza munthu wina ali yense chimene inu munali kumachiganizira! Kodi inu simuli okondwa kuti Yehova anatipatsa ife pakamwa?—Ndipo popeza kuti iye anatipatsa ife pakamwa pathu, kodi inu simukubvomereza kuti ipo panayenera kugwiritsiridwa nchito m’njira imene idzamlemekeza iye?—
Imeneyo ndiyo njira imene Mfumu Davide analingalilira. Iye anali mtumiki wa Mulungu. Ndipo iye anati: “Pakamwa panga padzanena chilemekezo cha Yehova.” Kodi inu mukubvomereza kuti chimenechi chiri chinthu chabwino kuchichita ndi pakamwa pathu?—Pamenepo, tiyeni tichibwereze limodzi chimene iye ananena: “Pakamwa panga padzanena chilemekezo cha Yehova.”—Salmo 145:21.
Kunali buthu lina Lachiisrayeli limene linagwiritsira nchito pakamwa pache m’njira imeneyo. Pamene ilo linali ndi moyo, mtundu wa Suriya ndi mtundu wa Israyeli inali pa udani. Tsiku lina Asuri anamenyana ndi Israyeli nalitenga buthu limenelo kukhala kapolo. Ilo linatumizidwa ku nyumba ya mkulu wa ankhondo, amene anali kuchedwa Namani. Kumeneko ilo linakhala mtumiki wa mkazi wa Namani.
Tsopano, Namani anali ndi nthenda yochedwa khate. Palibe ali yense wa adotolo anali wokhoza kumthandiza iye. Koma buthu la ku Israyelilo linali ndi chikhulupiliro chachikuru mwa Yehova. Ilo linadziwa kuti iye akatha kuchita zinthu zodabwitsa. Ndipo ilo linakhulupilira kuti mmodzi wa atumiki apadera a Mulungu, mneneri, akadatha kumthandiza Namani. Ndithudi, Namani ndi mkazi wache sanakhulupilire mwa Yehova. Iwo anali ndi chipembedzo china. Kodi buthulo linayenera kuwauza iwo chimene ilo linachidziwa? Mwinamwache iwo sakadafuna kumene kuchimva icho. Kodi nchiani chimene inuyo mukadachita?—
Ilo linadziwa kuti ilo liyenera kulankhula. Chikakhala chinthu chokoma mtima kuchita. Ndipo chikasonyeza chikondi chache kaamba ka Mulungu. Chotero ilo linati: ‘Ngati kokha Namani akadapita kwa mneneri wa Yehova m’Israyeli. Motero iye akadachiritsidwa khate lache.’
Namani anafuna kuchiritsidwa kwambirimbiri. Chotero iye analimvetsera buthulo. Iye anapita kwa mneneri wa Yehova. Pamene iye anachita chimene mneneriyo anamuuza iye kuchichita, iye anachiritsidwa. Ichi chinamchititsa Namani kukhala mlambiri wa Mulungu woona. Ha, ndi wokondwa chotani nanga mmene iye anayenera kukhalira kuti buthu lochokera ku Israyelilo silinakhale lamantha kumtamanda Yehova!—2 Mafumu 5:1-15.
Kodi inuyo mungafune kumthandiza munthu wina kuphunzira za Yehova monga momwe linachitira buthu limenelo?—Kodi ndani amene alipo amene inuyo mukatha kumthandiza?—
Ndithudi, poyamba iwo sangaganizire kuti iwo afunikira chithandizo. Koma inu mukatha kulankhula nawo ponena za zinthu zabwino zimene Yehova amazichita. Ndipo iwo anagamvetsere. Kodi sikukakhala kodabwitsa ngati iwo akanafikira pa kumkonda Yehova monga momwe inu mukuchitira?—Zinthu zonga ngati zimenezo zimachitika pamene inu mupagwiritsira nchito pakamwa panu kumtamanda Yehova.
Baibulo limasimbanso za mnyamata wina wochedwa Timoteo. Atate wache sanali wokhulupilira Yehova. Koma mai wache anali wokhulupilira, ndi agogo ache omwe. Timoteo anawamvetsera iwo. Ndipo kuyambira pa nthawi imene iye anali wamng’ono kwambiri iye analidziwa Baibulo. Ife tifunikira kulidziwa Baibulo m’malo mwakuti timtamande Yehova. Ndilo Baibulo limene limatiuza ife za iye.
Pamene Timoteo anakula, iye anakhala mnyamata wabwino kwambiri. Tsiku lina Paulo, mtumwi wa Yesu Kristu, anafika ku tauni imene Timoteo anakhala. Iye anaona mmene Timoteo anafunira kutumikira Yehova. Chotero iye anamuitana mnyamata ameneyu kudza limodzi ndi iye kutumikira Mulungu m’njira yokulirapodi. Iwo anawauza anthu ponena za ufumu wa Mulungu ndi ponena za Yesu.—Machitidwe 16:1-5.
Timoteo anaphunzira zochuruka ponena za kumtamanda Mulungu kuchokera kwa mtumwi Paulo. Iye anamuona Paulo akukamba nkhani zosiyanasiyana ku magulu akuru a anthu. Iye anaona mmene Paulo anapitira ku nyumba za anthu kukawaphunzitsanso iwo. Koma Timoteo sanangoyang’anitsa kokha. Iye anakhala ndi phande m’nchitoyo. Monga momwe Paulo ananenera kuti, “Timoteo ali kuchita nchito ya Yehova, monganso ine.’—1 Akorinto 16:10, NW.
Si munthu ali yense anakondwera pamene Timoteo analankhula za Mulungu. Koma iye sanaleke. Iye sananene kuti iye akufuna kupita ku nyumba. Iye anali wokondwa kuti iye anatha kugwiritsira nchito pakamwa pache kulankhula chitamando cha Yehova.
Tsopano, anthu ena anganene kuti chimenechi chiri kanthu kena kamene achikulire okha angachite. Koma kodi inuyo mukuchikhulupilira chimenecho?—Mphunzitsi Wamkuruyo anadziwa kuti chimenecho sichinali choncho. Tsiku lina pamene anthu ena anayesayesa kuwachititsa anyamata achichepere kuleka kutamanda Mulungu, Yesu anati: ‘Kodi inu simunawerenge m’Malemba kuti, “Pakamwa pa ana ang’ono padzaturuka chitamando”?’—Mateyu 21:16, NW.
Tonsefe tingathe kumtamanda Yehova ngati ife tikufunadi. Sikuli kobvuta. Mulungu anatipatsa ife pakamwa polankhulira napo. Ife sititofunikira kudziwa chinthu chiri chonse ponena za Baibulo ife tisanayambe. Ife tingathe kuwauza ena chabe zimene ife taziphunzira kale. Kodi mungafune kuchita chimenecho?—
(Malemba ena amene amawalimbikitsa ana kumtumikira Mulungu ndiwo Salmo 148:12, 13; Mlaliki 12:1; 1 Timoteo 4:12.)