Mutu 30
TAnthu Amene Anasunga Masiku a Kubadwa
KODI INU mumakonda kukhala ndi mapwando?—Ngati iwo ali mapwando abwino, iwo angathe kukhala okondweretsa kwambiri.
Koma si mapwando onse ali abwino. Mapwando ena ali aphokoso kwambiri chakuti anthu oyandikana nawo nyumba amakwiya. Ndipo pali mapwando ena amene ngakhale Mulungu samawabvomereza. Kodi munadziwa chimenecho?—Kodi inu mukafuna kukhala pa phwando ngati inu mukadadziwa kuti Mulungu sanalibvomereze ilo?—
Baibulo limatiuza ife ponena za mapwando. Mphunzitsi Wamkuruyo anapita ku phwando pa nthawi ina, ndi atumwi ache omwe Linali phwando limene linachitidwa pamene munthu wina anakwatira Kodi inu munayamba mwakhala ku mtundu umenewo wa phwando?—
Baibulo limatiuzanso za mapwando awiri a tsiku la kubadwa Kodi limodzi la ilo linali kuchita phwando la tsiku la kubadwa la Mphunzitsi Wamkuruyo?—Ai Mapwando a tsiku la kubadwa awiri onsewa anali a anthu amene sanamtumikire Yehova.
Limodzi la mapwando a tsiku la kubadwa linali la Mfumu Herode Antipa Iye anali wolamulira wa boma la Galileya pamene Yesu anakhala kumeneko.
Mfumu Herode anachita zinthu zambiri zoipa Iye anatenga mkazi wa mbale wache kukhala mkazi wache Dzina lache linali Herodia Mtumiki wa Mulungu Yohane Mbatizi anamuuza Herode kuti kunali kolakwa kwa iye kuchita chimenecho Herode sanachikonde chimenecho Chotero iye analamulira kuti Yohane atsekeredwe m’ndende.—Luka 3:19, 20.
Pamene Yohane anali m’ndendemo, tsiku linafika la kukumbukira kubadwa kwa Herode Herode anakonza phwando lalikuru Iye anawaitana anthu ambiri odziwika Iwo onse anadya namwa nasangalala.
Ndiyeno mwana wamkazi wa Herodia anafika nawabvinira iwo Munthu ali yense anali wokondweretsedwa kwambiri ndi kubvina kwache chakuti Mfumu Herode anafuna kumpatsa iye mphatso yaikuru Iye anamuitana mtsikanayo nati: ‘Chiri chonse chimene undipempha ine, ndidzachipereka icho kwa iwe, kufikira theka la ufumu wanga.’
Kodi iye akapempha chiani? Kodi zikakhala ndarama? zobvala zokongola? nyumba yachifumu kaamba ka iye mwini? Mtsikanayo sanadziwe chimene angachinene Chotero iye anapita kwa mai wache Herodia nati:“Ndidzapempha chiani?”
Tsopano, Herodia anamuda Yohane Mbatizi kwambiri Chotero iye anamuuza mwana wache wamkaziyo kupempha mutu wache Mtsikanayo anabweleranso kwa mfumu nati:‘Ndikufuna mundipatse tsopano apa m’mbale mutu wa Yohane Mbatizi.’
Mfumu Herode sanafune kumupha Yohane, chifukwa chakuti iye anadziwa kuti Yohane anali munthu wabwino Koma Herode anali atapanga lonjezo, ndipo iye anachita mantha ndi chimene ena pa phwandolo akachiganizira ngati iye akadasintha maganizo ache Chotero iye anatumiza munthu ku ndende kukadula mutu wa Yohane Mwamsanga munthuyo anabwera Iye anali ndi mutu wa Yohane m’mbale, ndipo iye anaupereka uwo kwa mtsikanayo Pamenepo mtsikanayo anathamanga nakaupereka kwa mai wache Kodi chimenecho sichinali choopsa?—Marko 6:17-29.
Koma bwanji ponena za phwando lina la tsiku la kubadwa limene Baibulo limasimba za ilo? Kodi ilo linali labwino?—
Phwandolo linali la mfumu ya Igupto Pa phwando lache iyenso analamulira mutu wa munthu wina kudulidwa Ndiyeno iye anampachika munthuyo kuti mbalame zimudye.—Genesis 40:20-22.
Kodi mukuganiza kuti Mulungu anawabvomereza mapwando amenewa?—Kodi inuyo mukadafuna kukhala pa iwo?—
Tsopano, ife tikudziwa kuti chinthu chiri chonse chimene chiri m’Baibulo chirimo kaamba ka chifukwa Ilo limatiuza ife ponena za anthu abwino kotero kuti ife tingathe kuwatsanzira iwo Ndipo ilo limatiuza ife ponena za anthu oipa kotero kuti ife sitidzachita chimene iwo anachichita Baibulo limatiuza ponena za mapwando a tsiku la kubadwa awiri okha, ndipo awiri onsewo anali oipa Chotero, kodi nchiani chimene inu mukanena kuti Mulungu ali kumatiuza ife ponena za mapwando a tsiku la kubadwa?Kodi Mulungu amatifuna ife kuchita mapwando a masiku a kubadwa?—
Nzoona kuti pa mapwando oterowo lero lino anthu samadula mutu wa munthu wina Koma lingaliro lonse la kuchita phwando la masiku a kubadwa linayamba ndi anthu amene anachita zinthu zonga zimenezo Iwo anali akunja Iwo anali anthu amene sanamtumikire Yehova Kodi ife tikufuna kukhala ngati iwo?—
Bwanji ponena za Mphunzitsi Wamkuruyo?Kodi iye anachita phwando la tsiku lache la kubadwa?—Ai Palibe malo m’Baibulo amene amanena kanthu kali konse ponena za phwando la tsiku la kubadwa la Yesu.
Ngakhale Yesu atamwalira, atsatiri ache oona sanachite phwando la tsiku lache la kubadwa Iwo sanafune kukhala ngati akunjawo Koma pambuyo pache panali anthu amene anafuna kuchita phwando la tsiku la kubadwa la Yesu Iwo sanathe kugwiritsira nchito deti lenileni la kubadwa kwa Yesu, chifukwa chakuti Baibulo silimanena pamene ilo linali Chotero iwo anasankha deti pamene akunjawo anali ndi chuthi Ilo linali December 25 Ngakhale lero lino, limenelo ndilo limene anthu amachita phwando la Krisimesi Kodi inu mukuganiza kuti Mulungu amalibvomereza limenelo?—
Anthu ochuruka amadziwa kuti Krisimesi siri tsiku la kubadwa la Yesu Koma ambiri amalichitirabe ilo phwando Iwo samasamaladi chimene Mulungu amaganiza Koma ife timafuna kumkondweretsa Yehova, ati?—
Chotero, pamene ife tikhala ndi mapwando tifuna kutsimikizira kuti iwo ali mapwando abwino Ife tingathe kukhala nawo nthawi iri yonse ya chaka Ife sitimafunikira kuyembekezera tsiku lapadera Ife tingathe kudya chakudya china chapadera ndi kukhala ndi chikonwelero kumachita masewera Kodi inu mukanakonda kuchita chimenecho?—Koma ife tisanawapange malinganizidwe athu, tiyeni titsimikizire kuti ilo liri mtundu wa phwando umene Mulungu akanaubvomereza.
(Kufunika kwa kumachita masiku onse chimene Mulungu amachibvomereza kwasonyezedwanso pa Yohane 8:29, Aroma 12:2, Miyambo 12:2 ndi 1 Yohane 3:22.)