Mutu 31
Madzi Alisesa Dziko
KODI INU mumakonda kuchita masewera?—Ine ndimakonda. Iwo angathe kukhala osangalatsa kwambiri, ati?—Koma kodi munadziwa kuti pali upandu m’kumakhala otanganitsidwa kwambiri kumakhala ndi zokondweretsa?—Inde, ulipo. Ife tingalephere kukhala ndi nthawi ya kumumvetsera Mulungu. Kodi inu munachidziwa chimenecho?—
Mphunzitsi Wamkuruyo anadziwa kuti chimenechi chinali chitachitika ku dziko lonse lapansi la anthu nthawi ina kalelo. Iye anati: ‘Anthu amenewo analinkudya. Iwo analinkumwa. Iwo analinkumakwatirana.’ Sikuli kolakwa kudya ndi kumwa kapena kukwatira. Koma iwo anali otanganitsidwa kwambiri kumazichita zinthu zimenezo chakuti iwo sanakhale ndi nthawi ya kumumvetsera Mulungu. Chimenecho chinali choipa.
Kodi nchiani chimene chinawachitikira anthu amenewo?—Yesu anati: “Iwo sanadziwe kufikira chigumula chinadza nichiwasesa iwo onse.” Yesu anali kumalankhula za anthu amene anafa m’masiku a Nowa. Pa nthawi imeneyo madzi a chigumula analikuta dziko lonse lapansi.—Mateyu 24:37-39, NW.
Yesu ananena kuti chimene chinawachitikira anthu amenewo chiri phunziro kaamba ka ife lero lino. Chotero kuli kofunika kuti ife tidziwe zonse ponena za chigumula cha tsiku la Nowa.
Choyamba, kodi nchifukwa ninji Yehova Mulungu anadzetsa Chigumulacho?—Chinali chifukwa chakuti anthu anali kumachita zinthu zoipa. Komabe panali munthu mmodzi amene anapeza chiyanjo ndi Mulungu. Kodi ameneyo anali ndani?—Anali Nowa. Nowa anamkonda Yehova Mulungu. Iye sanali konse wotanganitsidwa kwambiri kosamumvetsera nako Mulungu. Kodi mmenemo sindimo mmene ife tiyeneranso kukhalira?—
Tsiku lina Yehova anamuuza Nowa kuti Iye adzawaononga anthu onse amene anapitirizabe kumachita zinthu zoipa. Mulungu akaichititsa mvula kubvumba kwambiri kwakuti madziwo akalikuta dziko lonse lapansi, ngakhale mapiri.
Kodi Nowa akadafanso pamene madzi onsewo anagwa?—Ai; Yehova akampulumutsa iye. Yehova anamuuza Nowa kumanga chingalawa chachikuru. Chingalawa chiri ngati bwato, koma icho chimaoneka mofanana kwambiri ndi bokosi lalikuru ndi lalitali kapena chinyumba chonga libanda. Icho chimayandama pa madzi. Mulungu anamuuza Nowa kumanga chingalawa chachikuru mokwanira kotero kuti iye ndi banja lache ndi zochuruka za zinyama zikakhala zosungika m’kati mwache.
Tsopano, Nowa anali asanamange chingalawa ndi kale lonse. Koma Mulungu anamuuza iye kuchichita kwache icho. Nowa ndi banja lache anagwira nchito zolimba kwambiri. Iwo analikha mitengo yaikuru. Iwo anayamba kumachimanga chingalawacho ndi matabwa ochokera m’mitengo imeneyi. Ichi chinatenga zaka zambirimbiri, chifukwa chakuti chingalawacho chinali chachikuru kwambiri.
Kodi Yehova anawapatsa anthu ena mwai wa kulowa m’chingalawacho ndi kupulumutsidwa?—Inde, iye anawapatsa. Yehova anamuuza Nowa kulalikira. Chotero mkati mwa zaka zonsezo zimene chingalawacho chinali kumamamgidwa, Nowa anawachenjeza anthuwo ponena za chigumula chinalinkudzacho.
Kodi ali onse a iwo anamvetsera?—Banja la Nowa lokha linamvetsera. Ena onse anali ongotanganitsidwa kwambiri kumachita zinthu zina. Iwo sanaganize kuti iwo anali oipa kwambiri, ndipo iwo sanakhale ndi nthawi ya kumvetsera.
Potsirizira pache, nyama zonse zimene Yehova anafuna kuzipulumutsa zinalowetsedwa m’chingalawacho. Tsopano inali nthawi yakuti anthu alowe m’chingalawamonso. Nowa ndi banja lache analowa m’katimo. Ndiyeno Yehova anatseka chitsekocho. Kunali kochedwa kwambiri kuti wina wachenso alowemo.
Anthu kunjako sanakhulupilirebe kuti chigumula chikadza. Koma mwadzidzidzi madzi anayamba kugwa! Nowa anali atanena zoona!
Iyo sinali chabe mvula ya masiku onse. Iyo inali kukhuthuka! Mwamsanga madziwo anali ngati mitsinje yaikuru, akumapanga phokoso lambiri. Iyo inakokolola mitengo yaikuru ndi kukunkhuniza miyala yaikuru monga ngati iyo inali nkhulungo zazing’ono.
Bwanji ponena za anthuwo kunja kwa chingalawacho?—Yesu akuti: “Chigumula chinadza nichiwasesa iwo onse.” Ngakhale ngati iwo anakwera m’phiri, chimenecho sichinathandize. Kukhuthukako sikunaleke kwa masiku makumi anai ndi mausiku makumi anai. Posakhalitsa dziko lonse lapansi linakutidwa ndi madzi. Anthu onse kunja kwa chingalawacho tsopano anali atafa. Kodi nchifukwa ninji?—Monga momwe Yesu ananenera, ‘Iwo sanamvetsere!’
Koma chomayandama pa madzicho chinali chingalawa. Nowa, banja lache ndi zinyama anali bwino m’katimo. Yehova anawapulumutsa anthu amene anamvetsera kwa Iye.—Genesis 6:5-7:24.
Tsopano, kodi nchifukwa ninji ife tiyenera kudziwa ponena za chimene chinachitika m’tsiku la Nowa? Kodi mukuchikumbukira chimene Yesu anachinena?—Iye ananena kuti chimene chinachitika pa nthawi imeneyo chiri phunziro kaamba ka ife. Yehova kachiwirinso adzawaononga anthu onse oipa, koma nthawi ino iye sadzagwiritsira nchito chigumula. Nthawi yakuti iye achite chimenechi iri pafupi.
Pamene Mulungu achichita chimenechi, kodi ndani amene adzakhala anthu amene Mulungu adzawasunga amoyo?—Kodi adzakhala anthu amene anali otanganitsidwa kwambiri ndi zinthu zina chakuti iwo sanafune konse kuphunzira ponena za Mulungu? Kodi adzakhala anthu amene masiku onse anali otanganitsidwa kwambiri kosaphunzira nako Baibulo?—Kodi adzakhala awo amene sanafune konse kupita ku misonkhano kumene anthu anaphunzira chifuniro cha Mulungu? Kodi inu mukuganiza bwanji?—
Ife tikufuna kukhala pakati pa anthu awo amene Mulungu adzawasunga amoyo, ati?—Kodi sikukakhala kodabwitsa ngati banja lathu likadakhala ngati la Nowa kotero kuti Mulungu akadatipulumutsa tonsefe?—Tiyeni masiku onse tithandizane wina ndi mnzache kukhala okhulupirika kwa Mulungu kotero kuti iye adzatipulumutsa tonsefe.
(Ife tikufunikira kupeza nthawi m’miyoyo yathu kumumvetsera Mulungu. Werengani chimene chanenedwa ponena za ichi pa Hoseya 4:6, Mateyu 13:18-22 ndi Deuteronomo 30:15, 16.)