Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • te mutu 33 tsamba 135-138
  • “Zinthu za Kaisara kwa Kaisara”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Zinthu za Kaisara kwa Kaisara”
  • Kumamumvetsera Mphunzitsi Wamkuru’yo
  • Nkhani Yofanana
  • Kudziŵa Amene Uyenera Kumumvera
    Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso
  • Kodi Muyenera Kukhoma Misonkho?
    Galamukani!—2003
  • Kodi Ndinu ‘Okonzeka Kumvera’?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2023
  • Kodi Muyenera Kukhoma Misonkho?
    Nsanja ya Olonda—2011
Onani Zambiri
Kumamumvetsera Mphunzitsi Wamkuru’yo
te mutu 33 tsamba 135-138

Mutu 33

“Zinthu za Kaisara kwa Kaisara”

TIYENI titurutse ndarama ndi kuyang’ana pa iyo. Kodi nchiani chimene mumachiona pa ndaramayo?—Kodi ndani amene anaipanga ndarama imeneyi?—Boma linaipanga.

Kwa zaka zikwi zambiri maboma apanga ndarama zimene anthu amazigwiritsira nchito. Pamene Mphunzitsi Wamkuruyo anali pa dziko lapansi, boma Lachiroma linapanga ndarama. Ndipo kodi mukumdziwa amene anali wolamulira wa boma limenelo?—Iye anali kuchedwa Kaisara.

Boma Lachiromalo linachita zinthu zabwino zambiri kaamba ka anthuwo m’masiku amenewo. Ndipo maboma lero lino amachita zinthu zabwino zambiri kaamba ka ife. Iwo amaswa miseu yoyendamo. Iwo amalipira apolisi ndi anthu ozimitsa moto kutichinjirizira ife.

Zimalidyera ndarama boma kuchita zinthu zimenezi. Kodi inu mukukudziwa kumene boma limapezako ndaramazo?—Ilo limazipeza izo kuchokera kwa anthu. Ndarama zimene anthu amazilipira ku boma zimachedwa misonkho.

Anthu ambiri samakonda kukhoma misonkho. Pamene Yesu anali pa dziko lapansi, ena a Ayudawo sanafune kulipira misonkho iri yonse ku boma Lachiromalo. Iwo anaida misonkho yoteroyo. Chotero, tsiku lina anthu ena anadza kwa Mphunzitsi Wamkuruyo namfunsa iye kuti: ‘Kodi ife tifunikira kulipira misonkho kwa Kaisara kapena ai?’

Tsopano, anthu analifunsa funso limeneli kumtapa m’kamwa Yesu. Pakuti ngati Yesu akadayankha kuti, ‘Inde, inu muyenera kulipira misonkho,’ ambiri a Ayudawo sakadachikonda chimene Yesu adanena. Koma Yesu sakadanena kuti, ‘Ai, inu simufunikira kulipira misonkho.’ Kukadakhala kolakwa kunena chimenecho.

Chotero ichi ndicho chimene Yesu anachichita. Iye anati kwa anthu amenewo: ‘Ndisonyezeni ndarama.’ Pamene iwo anambweretsera ndaramayo, Yesu anawafunsa iwo kuti: ‘Kodi chithunzithunzi ndi dzina ziri pa iyo nzayani?’

Anthuwo anati: “Za Kaisara.”

Chotero Yesu anati: “Pamenepo, mwa njira iri yonse, bwezerani zinthu za Kaisara kwa Kaisara, koma zinthu za Mulungu kwa Mulungu.”—Luka 20:19-26, NW.

Kodi limenelo silinali yankho labwino kwambiri?—Palibe munthu ali yense amene akadatha kupeza kanthu kali konse kolakwa ndi limenelo. Ngati Kaisara amawachitira anthu zinthu, kuli kokha koyenera kugwiritsira nchito ndarama zimene Kaisara anazipanga kuti timlipire iye kaamba ka zinthu zimenezi. Chotero m’njira imeneyi Yesu anasonyeza kuti kuli koyenera kulipira misonkho ku boma kaamba ka zinthu zimene timazilandira.

Tsopano, inu simungakhale wamkulu mokwanira kulipira misonkho. Koma pali kanthu kena kamene inu muyenera kupereka ku boma. Kodi inu mukuchidziwa chimenecho?—Ndicho kumvera ku malamulo a boma.

Ndi Mulungu amene amatiuza ife chimenechi. Mau ache amati: ‘Khalani omvera ku maulamuliro akuru.’ Ndipo kodi ndani amene ali ‘maulamuliro akuruwo’?—Anthu amene ali ndi mphamvu m’boma. Chotero ife tiyeneradi kumvera lamulo. Mulungu amatero.—Aroma 13:1, 2.

Tachilingalirani chitsanzo. Pangakhale lamulo lakuti musaponye pepala kapena chinyansi china pa khwalala. Kodi inu muyenera kulimvera lamulo limenelo?—Inde, Mulungu amakufunani inu kulimvera ilo.

Kodi ife tiyenera kukhala omvera kwa apolisi?—Boma limawalipira apolisi kuwachinjirizira anthu. Kumawamvera iwo kuli chimodzimodzi ndi kumvera boma.

Chotero ngati inu muli pafupi kudutsa khwalala ndipo mpolisi akuti, ‘Yembekezani!” kodi nchiani chimene inu muyenera kuchita?—Bwanji ngati ena muli monse adutsa mothamanga, kodi inu muyenera kutero?—Ngakhale ngati inu muli munthu yekha amene akuyembekezera, inu muyenera kutero. Mulungu amatiuza ife kuti timvere.

Mungakhale bvuto m’malo oyandikira ndipo mpolisi anganene kuti, “Musakhale m’makwalala. Musaturuke kunja.” Koma inu mungamve kuchita phokoso ndipo mudabwa chimene chirinkumachitika. Kodi muyenera kuturuka kunja kuti mukaone?—Kodi kumeneku kukakhala kuwamvera ‘maulamuliro akuru’?—

Boma m’malo ambiri limamanganso masukulu. Ndipo ilo limawalipira aphunzitsi. Pamene ana amachita zimene mphunzitsi amanena, kumachititsa mtendere m’kalasi. Chotero kodi inu mukuganiza kuti Mulungu amakufunani inu kumumvera mphunzitsi?—

Mulibe lemba liri lonse m’Baibulo limene limati, “Mvera mphunzitsi wako.” Koma Baibulo limasonyeza kuti inu muyenera kumvera. Boma limamlipira mphunzitsi kuti aphunzitse, monga momwe ilo limamlipilira mpolisi kuwachinjirizira anthu. Chotero kumakhala womvera kaya kwa mpolisi kapena kwa mphunzitsi kuli ngati kumvera boma.

Kapena ife tingathe kukuona iko motere. Mulungu amawauza ana ‘kuwamvera atate ndi amai ao.’ Koma atate ndi amai anu akutumizani ku sukulu kuti mphunzitsi akusamalireni. Chotero kuli koyenera kumumvera mphunzitsi wanu, monga momwe inu mumawamvelera makolo anu pa nyumba.—Aef. 6:1.

Ine sindimakhala nanu masiku onse. Chotero ine sindingaone kaya inu mumamumvera mphunzitsi. Koma Mulungu amaona. Ndipo ndi Mulungu amene ife timafunadi kumkondweretsa, eti?—Ndiponso, ine sindingaone ngati inu mumamumvera mpolisi. Koma kodi ndani amene amaona?—Mulungu amaona. Masiku onse kumbukirani chimenecho.

Kumbukiraninso, kuti, Mulungu amadza poyambilira m’miyoyo yathu. Ife timalimvera boma chifukwa chakuti chimenecho ndicho chimene Mulungu amatifuna ife kuchichita. Koma bwanji ngati iwo atiuza ife kuchita chimene Mulungu amatiuza ife kuti sitiyenera kuchichita?—Ngati munthu ali yense atiuza ife kuti, “Inu simufunikira kumvera Mulungu,” kodi Mulungu amatifuna ife kumvetsera zimenezo?—

Chimenecho chinawachitikira atumwi a Yesu. Tsopano kodi nchiani chimene atumwiwo akadachichita? Kodi inuyo mukadachitanji?—Iwo anayankha kuti: “Ife tiyenera kumvera Mulungu monga wolamulira koposa anthu.”—Machitidwe 5:29, NW.

(Ulemu kaamba ka lamulo ukuphunzitsidwa m’Baibulo. Werengani chimene chalembedwa pa Tito 3:1, Mateyu 5:41 ndi 1 Petro 2:12-14.)

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena