Mutu 36
Mfarisi Wodzitama
KODI kumatanthauzanji kukhala wodzitama? Kodi inu mukudziwa?—Nachi chitsanzo. Kodi inu munayamba mwayesa kuchita kanthu kena kamene inu simunali wokhoza bwino kwambiri kukachita? Mwinamwache inu munayesa kumenya mpira. Kapena mwinamwache inu munayesa kulumpha chingwe. Kodi winawache anayamba wanena kuti, “Ha! Ha! Ha! ine ndingathe kuchita chimenecho bwino kwambiri koposa iwe”?—Eya, munthu ameneyo anali kudzitama. Iye anali kumadzitamandira yekha.
Kodi inu mumamva bwanji pamene ena achita chimenecho? Kodi inu mumachikonda?—Pamenepo, kodi mukuganiza kuti ena akamva bwanji pamene inu mudzitama?—Kodi nkwabwino kumuuza munthu wina wache kuti, “Ine ndiri bwinopo koposa iwe”?—Kodi Yehova amawakonda anthu amene amachita chimenecho?
Mphunzitsi Wamkuruyo anawadziwa anthu ena amene anachita zinthu zonga zimenezo. Tsiku lina iye anawauza iwo mwambi. Uwo unali wonena za Mfarisi wina ndi wosonkhetsa msonkho wina.
Afarisi anali aphunzitsi achipembedzo onyada. Iwo kawirikawiri anachita monga ngati kuti iwo anali olungama kwambiri kapena oyera kwambiri koposa anthu ena. Mfarisi wa m’mwambi wa Yesu anakwera ku kachisi wa Mulungu m’Yerusalemu kukapemphera.
Yesu ananena kuti wosonkhetsa msonkho anakweranso komweko kukapemphera. Tsopano, anthu ochuruka sanawakonde osonkhetsa msonkho. Iwo analingalira kuti osonkhetsa msonkhowo anali otsutsana nawo. Ndipo, kuphatikiza pa chimenecho, osonkhetsa msonkho ena sanali masiku onse oona mtima.
Pa kachisipo Mfarisiyo anayamba kupemphera kwa Mulungu motere: ‘O Mulungu, ndikukuthokozani kuti ine sindiri wochimwa ngati anthu ena. Ine sindimawanyenga anthu kapena kuchita zinthu zina zoipa. Ine sindiri ngati wosonkhetsa msonkho uja ali ukoyo. Ine ndine munthu wolungama. Ndimakhala wosadya kawiri pa mlungu kotero kuti ndiri ndi nthawi yochuruka ya kuganizira za inu. Ndipo ine ndimapereka ku kachisi chachikhumi cha zinthu zonse zimene ine ndimazipeza.’ Mfarisi ameneyo anaganiziradi kuti iye anali wolungama, kodi sichoncho?—Ndipo iye anamuuzanso Mulungu ponena za iko.
Koma wosonkhetsa msonkhoyo sanali wotero. Iye sanalingalire kuti iye anali wabwino kwambiri ngakhale kudza pafupi ndi kachisi wa Mulungu. Iye sakadakweza maso ache ngakhale kumwamba. Chotero iye anaimabe chapatali atazolitsa mutu wache. Iye anali ndi chisoni ndi machimo ache. Ndipo iye anaguguda chifukwa chache mwachisoni. Iye sanayese kumuuza Mulungu mmene iye analiri wabwino. Koma iye anapemphera kuti: ‘O Mulungu, khalani wokoma mtima kwa ine wochimwa.’
Kodi ndi uti wa anthu amenewo amene inu mukuganizira kuti anali wokondweretsa kwa Mulungu? Kodi anali Mfarisi wodzitamayo, uyo amene anaganizira kuti iye anali wabwino kwambiri? Kapena kodi anali wosonkhetsa msonkhoyo, amene anamva chisoni ndi machimo ache?—
Yesu anati: ‘Kwa Mulungu, wosonkhetsa msonkhoyo anali wolungama kwambiri koposa Mfarisiyo. Chifukwa chakuti munthu ali yense amene amayesayesa kudzionetsa ngati iye ali wabwino kwambiri koposa anthu ena adzatsitsidwa. Koma iye amene ali wodzichepetsa m’maso mwache mwa iye mwini adzakwezedwa.’—Luka 18:9-14.
Kodi mwalimvetsa phunziro limene Yesu anali kuliphunzitsa?—Iye anali kumasonyeza kuti kuli kolakwa kuganizira kuti ife tiri abwino kwambiri koposa anthu ena. Tiyeni tione mmene phunziro limeneli limayeneranira ndi miyoyo yathu.
Mwinamwache inu ndi mwana wina muli kumafunsidwa mafunso ku sukulu. Bwanji ngati inu muli wokhoza kupereka yankho mwamsanga, koma mwana winayo ali wochedwerapo? Ndithudi, inu mumamva bwino pamene inu mukuwadziwa mayankhowo. Koma kodi kukakhala kokoma mtima kumuuza wophunzira winayo kuti iye ali mbewewe?—Kodi kuli koyenera kuyesa kudzipanga nokha kuoneka abwino mwa kumampanga munthu winayo kuoneka woipa?—
Chimenecho ndicho chimene Mfarisiyo anachichita. Iye anadzitamandira kuti iye anali wabwino kwambiri koposa wosonkhetsa msonkhoyo. Koma Mphunzitsi Wamkuruyo ananena kuti iye anali wolakwa.
Nzoona kuti munthu wina angakhale wokhoza kuchita bwino kwambiri kanthu kena koposa wina ali yense. Koma kodi chimemecho chimatanthauza kuti iye ali munthu wabwino kwambiri?—
Taganizirani za icho. Ngati ife tidziwa zambiri, kodi ife tiyenera kudzitamanda?—Kodi ife tinapanga ubongo wathu wa ife eni?—Ai, Mulungu ndiye Amene anampatsa munthu ubongo. Ndipo zinthu zonse zimene ife tikuzidziwa tinaziphunzira kuchokera kwa munthu winanso. Mwinamwache timaziwerenga m’bukhu. Kapena mwinamwache munthu wina anatiuza ife. Ngakhale ngati tinachiturukira icho tokha, kodi ndi motani mmene ife tinachichitira icho? Mwa kumayang’ana zinthu zimene Mulungu anazipanga. Chinthu chiri chonse chimene ife tiri nacho chinachokera kwa munthu winanso.
Anthu ena ali amphamvu. Kodi chimenecho chimawapanga iwo kukhala abwino kwambiri koposa munthu wina ali yense?—Iwo sanawapange matupi ao a iwo eni, kodi iwo anatero?—Mulungu ndiye Amene anapereka minofu kwa munthu. Ndipo Mulungu ndiye Amene amapangitsa zakudya kukula kotero kuti ife tingathe kudya ndi kukhala amphamvu.
Chotero, kodi ali yense wa ife ali ndi chifukwa chokwanira kudzitama? Kodi ife tiri abwino kwambiri koposa anthu ena?—M’malo mwa kuwauza ena mmene ife tiliri abwino, ife tiyeneradi kumawauza iwo mmene Yehova aliri wodabwitsa, kodi ife sitiyenera kutero?—Chifukwa chakuti iye ndiye Amene amakupangitsa kukhala kothekera kaamba ka ife kuchita zinthu bwino lomwe.
Pamene munthu wina amayesayesa zolimba, chinthu chokoma mtima ndicho kunena kanthu kena kamene kamampangitsa iye kumva bwino. Muuzeni iye kuti inu mukuchikonda chimene iye anachichita. Mwinamwache inu mungathedi kumthandiza iye kuchita bwino kwambiri. Chimenecho ndicho chimene inu mukadakonda anthu kukuchitirani, eti?—Eya, Yesu anati: ‘Monga momwedi inu mumawafunira anthu ena kukuchitirani inu, chitani njira imodzimodziyo kwa iwo.’ Limenelo liri lamulo labwino kulitsatira, ati?— —Luka 6:31.
Ngati ife tichita chimenecho, ife sitidzadzitamandira kapena kudzitama. Ife sitidzakhala ngati Mfarisi wodzitama uja.
(Kunyada ndi kudzitamandira ziri zinthu zimene ziyenera kupewedwa. Werengani chimene malemba awa amachinena: Miyambo 16:5, 18; 1 Akorinto 4:7; 13:4.)