Mutu 42
Manda Opanda Kanthu
KODI Mphunzitsi Wamkuruyo anaferadi pa mtengo wozunzirapowo?—Inde, iye anafadi. Anthu ambiri anachiona icho chikuchitika. Ena anaonadi pamene msilikari wina anadza nabaya ndi nthungo m’nthiti mwa Yesu. Iwo anauona mwazi ukuturuka. Inde, Mphunzitsi Wamkuruyo anafa.
Pambuyo pache, munthu wina wochedwa Yosefe anapita kwa kazembe Wachiromayo. Yosefe anamkhulupilira Mphunzitsi Wamkuruyo. Iye anati: ‘Kodi mudzandilola ine kuutsitsa mtembo wa Yesu pa mtengopo ndi kuuika uwo?’ Kazembeyo anati: ‘Inde. Uchotse uwo.’ Chotero Yosefe anautengera mtembo wa Yesu ku munda wina kumene kunali manda. Kodi inu mukudziwa chimene manda ali?—
Ndiwo malo kumene mitembo imaikidwa. Eya, mtembo wa Yesu unaikidwa m’kati mwa manda. Ndiyeno mwala waukulu wobulungira unagubudutsiridwa kumaso kwa khomo la mandawo. Mandawo anatsekedwa.
Yesu anali wakufa. Koma Yesu anali atawauza ophunzira ache kuti Mulungu akampangitsa iye kukhalanso ndi moyo. Liti? Yesu anali atanena kuti: ‘Pa tsiku lachitatu ine nditamwalira.’ Kodi zimenezo ndizo zimene zinachitika? Tiyeni tione.
Ndiwo mamawa kwambiri kusanache, dzuwa lisanaturuke. Chotero kuli chikhalirebe kwamdima. Asilikari ena ali komweko kumalondera mandawo. Akulu a ansembe anawatumiza iwo kuchita chimenecho. Chifukwa ninji? Kuti ophunzira a Yesu asafikepo. Koma tsopano kanthu kena koopsya kachitika.
Mwadzidzidzi nthaka ikuyamba kugwedezeka. Mu mdimawo pali kuwala kung’anima kwa mphezi. Taonani! Ndi mngelo wa Yehova! Asilikariwo ali oopsyedwa kwambiri iwo sangathe kusuntha. Mngeloyo akupita ku mandawo. Iye akuuchotsa mwalawo. Yang’anani m’katimo. Mandawo ali opanda kanthu.
Inde, Yehova Mulungu wamuukitsa Yesu. Koma Iye wamuukitsa Yesu ndi thupi longa lija limene Yesu anali nalo iye asandze ku dziko lapansi. Kodi inu mukukumbukira mtundu wa thupi umene ilo linali?—Ilo linali thupi longa limene angelo ali nalo, thupi lauzimu.—1 Petro 3:18.
Kodi inu mungathe kuliona thupi lauzimu?—Ai. Chotero, ngati mngelo anafuna kuti anthu amuone iye anafunikira kudzipangira yekha thupi longa lathu. Pamenepo anthu akatha kumuona iye. Pambuyo pache mngeloyo akazimilirika.
Tsopano dzuwa liri kuturuka. Asilikariwo achoka. Ndipo akazi ena amene anamkonda Yesu alinkudza ku mandawo. Iwo ali kumadzifunsa okha: ‘Kodi ndani amene ife tidzampeza kutichotsera ife mwala wolemera uja?’ Koma pamene iwo ayang’ana, mwalawo wagubuduzidwapo kale. Ndipo onani, mandawo ali opanda kanthu! Mtembo wa Yesu mulibe! Mmodzi wa akaziwo pomwepo akuthamanga kukawauza ena atumwi a Yesu.
Akazi enawo akukhala pafupi ndi mandawo. Iwo akuti: ‘Kodi mtembo wa Yesu ungakhale uli kuti?’ Mwadzidzidzi amuna awiri obvala zobvala zonyezimira akuonekera. Iwo ndiwo angelo! Iwo akuti kwa akaziwo: ‘Kodi nchifukwa ninji inu muli kumamfunafuna Yesu pano? Iye waukitsidwa. Pitani msanga ndi kuwauza ophunzira ache.’
Eya, inu mungathe kuyerekezera kufulumira kwache kumene akaziwo anathamangira! Ali pa njira mwamuna wina akukumana nawo. Kodi mukumdziwa ameneyo?—Ndi Yesu! Iyenso akuti kwa akaziwo: ‘Pitani ndi kuwauza ophunzira anga.’
Akaziwo ali okondwera. Iwo akuwapeza ophunzira ndi kuwauza iwo kuti: ‘Yesu ali ndi moyo! Ife tinamuona!’
Choyambilira ophunzirawo akuchipeza ichi kukhala chobvuta kuchikulupilira. Chikhalirechobe, iwo akudziwa kuti mandawo ali opanda kanthu. Petro ndi Yohane anali komweko ndi kuona kuti iwo ali opanda kanthu. Ophunzirawo akufuna kukhulupilira kuti Yesu ali ndi moyo kachiwiri. Koma zikuonekera kukhala zodabwitsa kwambiri kuti zikhale zoona. Kodi nchiani chimene chidzawapangitsa iwo kuchikhulupilira icho?—
Pambuyo pache Yesu akuonekera kwa ena a ophunzira amenewo. Pamene awiri a iwo ali kumayenda mu mseu, Yesu akuyamba kumayenda limodzi ndi iwo. Iye alankhula nawo ndipo kenako iye akuzimilirika. Iye akuonekeranso kwa Petro.
Ndiyeno pambuyo pache tsiku limodzimodzi lomwelo ophunzira ambiri asonkhana m’chipinda china. Zitsekozo ziri zokhomedwa loko, chifukwa chakuti iwo ali kuwaopa ansembe. Mwadzidzidzi Yesu ali momwemo m’chipindacho limodzi ndi iwo! Tsopano iwo akudziwadi kuti Mphunzitsi Wamkuruyo ali ndi moyo kachiwiri. Taganizirani mmene iwo aliri achimwemwe!—Mateyu 28:1-15; Luka 24:1-49; Yohane 19:38-20:21.
Pambuyo pa masiku ambiri, Yesu akuchoka pa dziko lapansi ndipo akubwelera kwa Atate wache kumwamba. Mwamsanga ophunzirawo ayamba kumamuuza ali yense kuti Mulungu anamuukitsa Yesu kuchokera kwa akufa. Anthu ambiri akukhulupilira ndi kukhala ophunzira.
Ichi chikuwakwiyitsa akulu a ansembewo. Iwo alamulira kuti atumwiwo agwidwe. Iwo akuwauza iwo kuti: ‘Lekani kumawaphunzitsa anthu zinthu zimenezi!’ Iwo akulamuliradi kuti atumwiwo amenyedwe ndi chikoti. Kodi iwo akuleka kuwaphunzitsa anthu? Kodi nchiani chimene inuyo mukadachichita?—
Atumwiwo sakuleka. Iwo sakuchita mantha tsopano. Iwo alidi ofunitsitsa kufa ngati iwo afunikira kutero. Iwo akudziwa kuti Mulungu anampangitsa Yesu kukhala ndi moyo kachiwiri. Iwo anamuona Yesu iye ataukitsidwa kuchokera kwa akufa. Iwo ali otsimikizira kuti Mulungu angathe kuwapangitsanso iwo kukhala ndi moyo ngati iwo afa okhulupirika kwa iye.—Machitidwe 1:3-11; 5:40-42.
Ha, ndi osiyana chotani nanga mmene iwo analiri ndi anthu ambiri lero lino! Anthu ena amaganizira kokha ponena za akalulu a Isitara (Easter) ndi mazira a Isitara amawangamawanga pamene iwo aganizira ponena za kuukitsidwa kwa Yesu. Koma Baibulo silimanena kanthu kali konse ponena za akalulu a Isitara ndi mazira. Ilo limanena za kumamtumikira Mulungu.
Ife tingathe kukhala ngati ophunzira a Yesu. Ife tingathe kuwauza anthu chinthu chodabwitsa chimene Mulungu anachichita pamene iye anampangitsa Mwana wache kukhala ndi moyo kachiwiri. Ife tingathe kumumvera Mulungu monga momwe Yesu anachitira. Koma bwanji ngati ife timwalira chifukwa cha kumamumvera Mulungu, monga momwe Yesu anafera?—Ife sitifunikira konse kuopa. Yehova angathe kutipangitsa ife kukhala ndi moyo kachiwiri pansi pa ufumu wache wolungama.
(Chikhulupiliro m’chiukiliro cha Yesu chiyenera kutipatsa ife chiyembekezo champhamvu ndi kuchipangitsa chikhulupiliro chathu kukhala champhamvu. Werengani 1 Akorinto 15:3-8; 20-23; Machitidwe 2:22-36; 4:18-20.)