Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • te mutu 43 tsamba 175-178
  • Yesu Apereka Chizindikiro

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Yesu Apereka Chizindikiro
  • Kumamumvetsera Mphunzitsi Wamkuru’yo
  • Nkhani Yofanana
  • Zimene Zikutidziŵitsa Kuti Armagedo Ili Pafupi
    Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso
  • Chizindikiro—Sichiri Kokha Mbiri Yakale
    Nsanja ya Olonda—1988
  • Yesu Analosera Zinthu za M’tsogolo Zimene Zidzakhudze Dziko Lonse
    Kodi Baibulo Lili Ndi Uthenga Wotani?
  • Kodi Mukuchiona Chizindikiro cha Kukhalapo kwa Yesu?
    Nsanja ya Olonda—2005
Onani Zambiri
Kumamumvetsera Mphunzitsi Wamkuru’yo
te mutu 43 tsamba 175-178

Mutu 43

Yesu Apereka Chizindikiro

LERO tidzakamba za zizindikiro. Kuli bwino kudziwa kuwerenga zizindikiro. Izo zingathe kutithandiza ife.

Zizindikiro zina ziri ndi mau pa izo. Izo zimatiuza ife kumene ife tingathe kugula chakudya. Izo zingatichenjeze ife kusadutsa khwalala pamene magalimoto ali kubwera. Kodi ndi zizindikiro zotani zimene inuyo mwaziona?—

Pali zizindikiro za mtundu winanso. Izo sizingakhale ndi mau. Zina za izo zimanena za kusintha kwa kunja. Mitambo ingaliphimbe dzuwa. Mwinamwache mphepo imayamba kuomba. Mphezi ing’anima. Kuli bingu. Pamene inu mumazimva ndi kuziona zinthu zimenezi, kodi izo zimatanthauzanji?—Inde, mwinamwache kudzakhala mvula. Sikuli kobvuta kuziwerenga zizindikiro zimenezo, eti?—

Tsiku lina atumwi a Yesu anampempha iye chizindikiro. Iwo anali atamumva iye akunena kuti anthu sakamuona iye kachiwiri kufikira nthawi ina yamtsogolo. Iwo anafuna kudziwa pamene nthawi imeneyo ikakhala. Kodi kukakhala chizindikiro chotani chakuti nthawiyo inafika?

Mphunzitsi Wamkuruyo anadziwa kuti atsatiri ache akafunikira chizindikiro. Iye anali kubwelera kumwamba kukakhala ndi Mulungu. Pamene iye akabweranso kachiwiri iye sakakhala munthu. Iye akakhala mzimu. Ndipo kodi inu mungathe kuuona mzimu?—

Chotero, kodi ndi motani mmene munthu ali yense akadziwira kuti iye anali atabweranso kachiwiri?—Eya, Yesu anawauza iwo cha kuchiyembekezera. Iye anawauza iwo ponena za zinthu zimene zikachitika pa dziko lapansi pompano.

Pamene Yesu anali kumalankhula kwa iwo, iwo anali pafupi ndi ku Yerusalemu. Iwo ankatha kumuona iye modutsa chigwacho. Ndipo iwo ankatha kumuona kachisi wache wokongolayo. Chotero Yesu anawauza iwo ponena za zinthu zimene zikamchitikira Yerusalemu ndi kachisi wache. Ndipo zinthu zimenezo zinachitikadi!

Koma Yesu ananenanso kuti zinthu zimodzimodzizo zikachitikanso pambuyo pache. Nthawi imeneyi izo zikachitika kudziko lonse lapansi. Ndipo kodi chimenechi chikatanthauzanji?—Chikatanthauza kuti Kristu anali atabweranso. Chikatanthauza kuti iye anayamba kulambira mu ufumu wa Mulungu kuchokera kumwamba. Posakhalitsa iye akawaononga oipa. Moyo posachedwapa ukakhala bwino kwambiri pano pa dziko lapansi.

Kodi inu mwachiona chizindikiro chimene Yesu anachipereka?—Ine ndachiona. Kodi mungafune kumva za icho?—

Monga mbali ya chizindikirocho, Yesu anati: ‘Inu mudzamva za nkhondo ndi mbiri za nkhondo. Mtundu udzaukira mtundu ndi ufumu kuukira ufumu.’

Chimenecho ndachiona m’kati mwa nthawi ya moyo wanga. Mitundu yathunthu yamenyana motsutsana ndi mitundu ina kuiononga iyo. Bvutolo linayambadi m’chaka cha 1914. Tsopano ife timawamva maripoti a nyuzi onena za nkhondo pafupifupi tsiku liri lonse. Kodi inu mwazimva mbiri zimenezo pa wailesi kapena pa wailesi yakanema?—

Nayi mbali ina ya chizindikirocho chimene Yesu anachipereka. Iye anati: ‘Kudzakhala kuperewera kwa zakudya m’malo ndi malo.’

Si munthu ali yense amene ali ndi chakudya chokwanira cha kuchidya. Kodi inu munachidziwa chimenecho?—Ine ndamva kuti tsiku liri lonse anthu zikwi khumi amafa chifukwa chakuti iwo samakhala ndi chakudya chokwanira. Kusoweka kwa chakudya kumachititsanso nthenda kapena mliri. Yesu ananena kuti kudzakhala kuperewera kwa zakudya ndi miliri.

Iyi ndi mbali ina ya chizindikiro chimene iye anachipereka: ‘Kudzakhala zibvomezi m’malo ndi malo.’

Kodi inu mumadziwa chimene chibvomezi chiri?—icho chimaipangitsa nthaka imene mwapondapo kugwedezeka. Nyumba zimagwa ndipo anthu kawiri kawiri amaphedwa. Chiyambire chaka cha 1914 kwakhala zibvomezi zambirimbiri chaka chiri chonse koposa ndi zimene zinaliko kale. Izo ndizo zinthu zimene zachitika m’nthawi ya moyo wanga.

Yesu ananena kuti mbali ina ya chizindikirocho ikakhala ‘kusaweruzika koonjezereka-onjezereka.’ Imeneyo iri kumachitikanso. Chimenecho ndicho chifukwa chache chimene anthu pafupifupi kuli konse amachitseka ndi loko chitseko pa nyumba zao. Iwo amaopa kuti wina wache angayeseyese kuswa ndi kulowa. Ndipo m’malo ambiri sikuli kwabwino kuyenda pa khwalala nokha usiku. Ndi kale lonse sikunakhale koipa monga momwe iko kuliri tsopano.—Mateyu 23:39-24:22.

Anthu ena anganene kuti zinthu zimenezi zachitika kale. Koma ndi kale lonse izo sizinachitika m’mbali yaikuru kwambiri ya dziko lapansi pa nthawi imodzi-modziyo. Zonsezi ziri ndi tanthauzo lapadera.

Kumbukirani kuti, Yesu ananena kuti zinthu zimenezi zikakhala chizindikiro. Kodi inu mungathe kuchiwerenga chizindikiro chimenecho? Kodi icho chimatanthauzanji?—

Anthu ochuruka amaona kokha bvuto. Ilo limawapangitsa iwo kukhala opanda chimwemwe. Koma ngati iwo akadadziwa chimene chizindikirocho chinatanthauza, iwo akadasangalala. Chifukwa ninji?—

Yesu anati: ‘Pamene zinthu izi ziyamba kuchitika, weramutsani mitu yanu, chifukwa chilanditso chanu chiri kuyandikira.’ Chimenecho chikutanthauza kuti ife tiyenera kukhala achimwemwe. Chifukwa m’nyengo yaifupi chabe Mulungu adzawathetsa mabvuto onse pa dziko lapansi ili. Moyo udzakhala chikondwelero chenicheni pa nthawi imeneyo.

Kodi inu simukubvomereza kuti imeneyo iri mbiri yabwino?—Ngati ife tiikhulupiliradi iyo, ife sitidzangokhala nayo tokha. Anthu ena afunikiranso kuidziwa iyo.

(Muli zambiri m’Baibulo zimene zimasonyeza kuti nthawi kaamba ka ufumu wa Mulungu yafika. Werengerani limodzi malemba awa: Luka 21:28-36; 2 Timoteo 3:1-5; 2 Petro 3:3, 4, 13.)

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena