Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • ts mutu 1 tsamba 4-9
  • Muli ndi Chifukwa Chokhalira Odera Nkhawa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Muli ndi Chifukwa Chokhalira Odera Nkhawa
  • Kodi Moyo Uno Ndiwo Wokha Umene Ulipo?
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • KODI IMFA IMAUMBA MIYOYO YATHU?
  • KUFUNIKA KWA KUKHALA WOTSIMIKIZIRA
  • Kodi Chimachitika N’chiyani Munthu Akamwalira?
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
  • Kodi Munthu Akafa Amapita Kuti?
    Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
  • Kufufuza Bwino Zikhulupiriro Zina Zopeka Zokhudza Imfa
    Nsanja ya Olonda—2002
  • “Imfayo Yamezedwa M’chigonjetso”
    Nsanja ya Olonda—2005
Onani Zambiri
Kodi Moyo Uno Ndiwo Wokha Umene Ulipo?
ts mutu 1 tsamba 4-9

Mutu 1

Muli ndi Chifukwa Chokhalira Odera Nkhawa

Kodi kudzakhala kotheka kwa munthu kukhala ndi moyo kosatha?

Mitengo ina tsopano iri ndi moyo kwa zaka mazana ambiri.

KODI moyo uli wamtengo wapatali kwa inu? Kodi mumakhumba moyo wa thanzi labwino kwa inu mwini ndi okondedwa anu? Anthu ochuluka adzayankha kuti, Inde.

Koma lero lino zinthu zambiri zimatikumbutsa mosalekeza za kusatsimikizirika kwa moyo—wa ife eni, wa anzanthu a mu ukwati ndi ana athu. Ngozi, maupandu, ziwawa, nkhondo ndi njala zimapha mamiliyoni ochuluka kuchiyambi kweni-kweni kwa moyo. Nthenda zimapha chiwerengero chachikulu kwambiri mosasamala kanthu kanthu za kupita patsogolo kwa mankhwala. Kuipitsa kukupereka chiopsyezo chachikulu kwambiri.

Pamenepo, si kodabwitsa kuti, anthu ambiri lero lino amafunsa kuti: ‘Kodi moyo uno ndiwo wokha umene ulipo? Kapena kodi kungakhale kwakuti chiyembekezo chathu chokondedwa kopambana chingapezedwe m’moyo pambuyo pa imfa? Kodi n’chiani kweni-kweni chimene chimachitika pamene munthu afa? Kodi mbali yake ina imakhalabe ndi moyo? Kodi iye amakhalabe wodziwa, wokhoza kuona, kumva, kulankhula—kuchita zinthu? Kodi pali chinthu chotero’cho chonga ngati chizunzo pambuyo pa imfa? Kweni-kweni, kodi imfa ndi bwenzi kapena mdani?’ Ndithudi n’kotipindulitsa kudziwa mayankho a mafunso amene’wa.

KODI IMFA IMAUMBA MIYOYO YATHU?

Mungakhale musanaziganize, koma miyoyo ya tonsefe imaumbidwa kwakukuku-kulu ndi lingaliro limene tiri nalo ponena za imfa. Limayambukira kusangalala kwathu ndi moyo ndi m’mene timagwiritsirira ntchito miyoyo yathu koposa kwambiri m’mene anthu ochuluka akudziwira. Ndicho chifukwa chake tifunikira kudziwa choonadi ponena za imfa.

Mwa chitsanzo, kodi mumazindikira, kuti zochuluka za zipembedzo za dziko ziri kweni-kweni zozikidwa pa imfa m’malo mwa kukhala zozikidwa pa moyo? Anthu mamiliyoni mazana ochuluka aphunzitsidwa kuti imfa idzawalowetsa m’dziko lina’lo, ‘dziko la akufa,’ kumene iwo amakumana kaya ndi chimwemwe kapena chizunzo. Mapemphero opempherera akufa, madzoma oonongetsa ndalama ochitiridwa iwo ndi nsembe zowatonthoza zimapanga mbali yofunika kwambiri ya zipembedzo zambiri zazikulu zokhala ndi ziwalo zochuluka kopambana.

Wina anganene kuti: ‘Mwina mwake ziri choncho, koma sindimaononga nthawi yanga ndikubvutika maganizo ndi imfa kapena chimene chimadza pambuyo pake. Bvuto langa ndiro kukhala ndi moyo ndi kupeza zochuluka monga momwe ndingathere m’moyo tsopano pamene ndingathe.’ Komabe ngakhale yankho limene’lo limasonyeza chiyambukiro choumba cha imfa pa miyoyo ya anthu. Ndi iko komwe, kodi sindiyo imfa imene imasintha utali wa nthawi imene iripo munthu asanati apeze chiri chonse m’moyo?

Chotero, ngakhale kuli kwakuti tingayese kuchotsa lingaliro la imfa m’maganizo mwathu, kuzindikira kuti utali wa moyo wathu uli, kwakukukulu-kulu, waufupi kwambiri kumapitirizabe kutibvutitsa maganizo. Kungalowetse munthu m’kuyesa-yesa kwamphamvu kwambiri kukhala wolemera pa usinkhu wachichepere—‘pamene iye angathe kusangalala ndi zinthu.’ Kufupika kwa moyo kumapangitsa anthu ambiri kukhala osadekha, amwano, ouma mtima kwa ena. Kumawachititsa kugwiritsira ntchito njira zosaona mtima kuti afikire zolinga zao. Iwo amalingalira kuti palibe nthawiya kuzichita m’njira yoyenera. Komabe, nthawi zonse iwo anganene kuti imfa iribe mbali m’kuumba miyoyo yao.

Kodi lingaliro lanu la inu mwini lonena za imfa ndi lotani? Kodi limachita mbali yotani m’maganizo anu a m’tsogolo, kapena, chifukwa cha chimene’cho, njira imene mukukhalira ndi moyo wanu pa tsopano lino?

KUFUNIKA KWA KUKHALA WOTSIMIKIZIRA

Bvuto n’lakuti pali kusiyana-siyana kwakukulu kwambiri pakati pa malingaliro a anthu onena za moyo ndi imfa. Kawiri-kawiri malingaliro’wo amakhala oombana, osemphana kweni-kweni.

Anthu ambiri amakhulupirira kuti imfa ndiyo mapeto otheratu a kanthu kali konse kapena, pafupi-fupi, kuti munthu anapangidwa kuti azifa. Kodi mumaona zimene’zo kukhala zobvomerezeka? Kodi ndi zomveka kwa inu kuti mitengo ina ingapitirire munthu wanzeru kukhala ndi moyo ndi zaka zikwi zochuluka? Kodi mukulingalira kuti zaka makumi asanu ndi awiri kapena makumi asanu ndi atatu za moyo ziri zochuluka mokwanira kwa inu kuti muchite zonse zimene mukufuna kuchita, kuphunzira zonse zimene mukufuna kuona ndi kukulitsa maluso ndi mphamvu zanu ku mlingo umene mukufuna?

Ndiyeno pali chiwerengero chachikulu kwambiri cha anthu amene amakhulupirira kuti moyo umapitirizabe pambuyo pa imfa chifukwa chakuti chinthu china—moyo kapena mzimu—umapulumuka imfa ya thupi. Komabe malingaliro ao amasiyana’nso kwambiri. Ndipo, ndithudi, zikhulupiriro zao zimaombana ndi lingaliro la awo amene amaganiza kuti moyo wonse umathera pa imfa. Malingaliro oombana onse sangakhale oona. Kodi ndi ati amene ali olondola? Kodi ziri n’kanthu? Inde, kwambiri. Talingalirani chifukwa chake.

Choyamba, ngati akufa angapindule kweni-kweni ndi mapemphero ndi madzoma ochitiridwa iwo. Kodi sitikanakhala opanda chifundo ngati tikanalephera kupereka zimene’zi? Koma bwanji ngati akufa ali akufa’di, osati n’kuthandizidwa ndi anthu amoyo? Zimene’zo kweni-kweni zikatanthauza kuti mamiliyoni mazana ochuluka a anthu ali onyengedwa koopsya. Zikatanthauza kuti magulu ambiri akulu achipembedzo adzilemeretsa ndi chinyengo, akumagwiritsira ntchito zinyengo ponena za akufa kuti alime pamsana amoyo m’malo mwa kuwachitira kanthu kena kopindulitsa.

Kodi ndi chitonthozo chotani chimene tingapereke pamene, tsiku lina, imfa ilowa m’banja lathu, kapena lija la bwenzi? Kodi kulingalira kumachirikiza lingaliro lakuti “choikidwiratu” chimalamulira zokumana nazo zathu ndi utali wa miyoyo yathu? Bwanji ngati munthu wakufa’yo anali mwana? Kodi Mulungu ‘anatenga mwana’yo kukakhala Naye,’ monga momwe ena akanenera?

Ndithudi pali zinthu zambiri-mbiri, zimene tifunikira kuzidziwa ponena za imfa, ndipo pamene tikukonda moyo ndi pamene’nso tiyenera kufuna kukhala otsimikizira kupeza mayankho oyenera. Koma kodi kuti—maka-maka popeza kuti pali chisokonezo chochuluka kwambiri ndi kuombana?

Pali mabukhu ambiri achipembedzo amene amalongosola moyo ndi imfa, ena a iwo akale kwambiri. Koma pali bukhu limodzi lakale kwambiri limene limapereka lingaliro losiyana kotheratu ndi lija a ena onse. Kunena zoona, lingaliro limene iro limapereka liri losiyana modabwitsa ndi limene unyinji waukulu wa anthu umalingalira kuti liri nalo. Bukhu limene’lo ndiro Baibulo.

Iro limanena za anthu eni-eni, anthu amene amakumana ndi mabvuto akulu amodzi-modzi amene ife tikukumana nawo lero lino. Iwo, nawo’nso, anasinkha-sinkha chifuno chonse cha kukhalira moyo, akumafunsa kuti: “Munthu ali ndi chiani m’ntchito zake zonse, ndi m’kusauka kwa mtima wake amasauka nazo’zo kunja kuno?” “Akakhala ndi moyo zaka zikwi ziwiri, koma osakondwera; kodi onse sapita ku malo amodzi?” (Mlaliki 2:22; 6:6) Iwo, nawo’nso, anadzutsa funso lakuti: “Atafa muntu, adzakhala’nso ndi moyo kodi?” (Yobu 14:14) Kodi mukudziwa mayankho?

M’bukhu limene tsopano lino liri m’manja mwanu’li mudzapezamo mukulongosoledwa, osati kokha zoyesa-yesa zambiri zofala za kuyankha mafunso amene afunsidwa kufikira tsopano lino’wa, koma’nso njira yofunika kopambana imene Baibulo limayankhira liri lonse la amene’wa. Mungaphunzire chiyembekezo chapadera chimene iro limapereka kwa awo okumana ndi imfa kapena amene agwidwa nayo. Kuzindikira kumene chidziwitso chimene’chi chingapereke kungaonjezere zochuluka ku chimwemwe ndi mtendere wanu wa maganizo za tsopano lino ndi m’tsogolo.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena