Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • ts mutu 9 tsamba 74-79
  • Kodi Mungathe Kulankhula ndi Akufa?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mungathe Kulankhula ndi Akufa?
  • Kodi Moyo Uno Ndiwo Wokha Umene Ulipo?
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • CHOCHITIKA CHA MFUMU SAULI
  • Kodi Amalankhuladi Ndi Akufa?
    Nsanja ya Olonda—1988
  • Kodi Akufa Angathandize Amoyo?
    Nsanja ya Olonda—2010
  • Kukhulupirira Mizimu
    Galamukani!—2014
  • Kodi Akufa Angathandize Anthu Amoyo?
    Galamukani!—2012
Onani Zambiri
Kodi Moyo Uno Ndiwo Wokha Umene Ulipo?
ts mutu 9 tsamba 74-79

Mutu 9

Kodi Mungathe Kulankhula ndi Akufa?

M’MOYO, anthufe timaona kwambiri kufunika kwa kulankhula ndi awo amene timawakonda. Timafuna kudziwa kuti okondwedwa athu ali bwino ndi achimwemwe. Pamene zinthu ziri bwino lomwe kwa iwo, ife timalimbikitsidwa. Koma pamene timva kuti iwo akuyang’anizana ndi choopsya chachikulu chifukwa cha tsoka “lachilengedwe” kapena tsoka lina, timayamba kudera nkhawa. Ife mofunitsitsa timayembekezera kumva mau kuchokera kwa iwo. Mwamsanga pamene tamva mau akuti iwo ali bwino lomwe timamasuka

Chikhumbo cha kudziwa thanzi la okondedwa chasonkhezera ambiri kufuna kulankhula ndi akufa. Iwo amafuna kudziwa kaya ngati okondedwa ao akufa’wo ali achimwemwe ‘m’dziko lina’lo.’ Koma kodi n’kotheka kulankhula ndi akufa?

Ena amanena kuti iwo nthawi ndi nthawi aona kufika kwa wachibale kapena bwenzi lakufa ndipo amva mau ake. Ena akhala ndi zokumana nazo zofanana’zo mwa chithandizo cha olankhula ndi mizimu. Kupyolera mwa olankhula ndi mizimu amene’wa iwo amakhulupirira kuti iwo amva mau ochokera ku ‘dziko lina’lo.’ Kodi iwo amauzidwanji ndi mau otero’wo? Kwakukulu-kulu izi: ‘Akufa ali okondwa kwambiri ndi okhutira. Iwo akupitirizabe kukhala ndi chikondwerero cheni-cheni m’moyo wa okondedwa ao okhalabe ndi moyo ndipo angathe kuona ndi kumva chiri chonse chimene iwo amachita.’

Ponena za mauthenga otero’wo, François Grégoire, m’bukhu lake lotchedwa L’au-delà (Moyo wina’wo), akunena kuti: “Kodi Mizimu imene’yi inganenenji kwa ife? ‘Koposa zonse, iyo imaonekera kukhala yofunitsitsa kutsimikizira kudziwika kwao ndi kuti irikobe’ . . . koma ponena za mkhalidwe wa dziko lina’lo, palibe kanthu kali konse kofunika kwambiri, ngakhale chibvumbulutso chaching’ono kwambiri.”

Kodi mukaganizanji ndi mauthenga amene’wa? Kodi mumakhulupirira kuli akufa akulankhula kweni-kweni? Popeza kuti, monga momwe Baibulo limasonyezera, palibe moyo kapena mzimu umene umapulumuka imfa ya thupi kupitirizabe ndi kukhalako kozindikira, kodi mau amene’wa angakhale’di mau a akufa?

CHOCHITIKA CHA MFUMU SAULI

Ena pakati pa awo okhulupirira kuti akufa angathe kupereka mauthenga kwa amoyo amasonya ku Baibulo Loyera kukhala likutsimikizira lingaliro lao. Chitsanzo chimodzi chimene iwo amachula ndicho chochitika cholowetsamo Mfumu Sauli ya Israyeli wakale.

Chifukwa cha kusakhulupirika kwake kwa Yehova Mulungu, Mfumu Sauli anachotseredwa chitsogozo chaumulungu chochitira mathayo ake. Chifukwa cha chimene’cho, pamene Afilisti anadza kudzathirana naye nkhondo, motaya mtima iye anafuna-funa chithandizo kwa wolankhula ndi mizimu. Iye anam’pempha kum’tulutsira malemu mneneri Samueli. Ponena za chimene chinachitika pambuyo pake, Baibulo limalongosola kuti:

“Ndipo mkazi’yo [wolankhula ndi mizimu] pakuona Samueli anapfuula ndi mau akulu; ndi mkazi’yo analankhula ndi Sauli, nati, Munandinyengeranji? popeza inu ndinu Sauli. Ndipo mfumu’yo inanena naye, Usaope, kodi ulikuona nchiani? Mkazi’yo ananena ndi Sauli, Ndirikuona milungu irikukwera kutuluka m’kati mwa dziko. Ndipo ananena naye, Makhalidwe ake ndi otani? Nati iye Nkhalamba irikukwera yobvala mwinjiro. Pamenepo Sauli anazindikira kuti ndi Samueli, naweramitsa nkhope yake pansi, nam’gwadira. Ndipo Samueli ananena ndi Sauli, Wandibvutiranji kundikweretsa kuno?’”—1 Samueli 28:12-15.

Kodi Sauli, m’chochitika chimene’chi, analankhula kweni-kweni ndi mneneri Samueli? Kodi zimene’zi zikanakhala choncho motani, pakuti Baibulo limagwirizanitsa imfa ndi kukhala chete, osati kulankhula? Timawerenga kuti: “Akufa salemekeza Yehova, kapena ali yense wakutsikira kuli chete.”—Salmo 115:17.

Ndime zina za Malemba Oyera zimamveketsa bwino nkhani’yo. Choyamba, n’koonekera bwino kuti chimene Sauli anachita m’kufunsa wolankhula ndi mizimu chinali kuswa lamulo la Mulungu. Olankhula ndi mizimu ndi owafunsa omwe anapezedwa ndi liwongo la cholakwa chofunikira chirango cha imfa. (Levitiko 20:6, 27) Lamulo la Mulungu kwa Israyeli linati: “Musamatembunukira kwa obwebweta, kapena anyanga; musawafuna, ndi kudetsedwa nao.” (Levitiko 19:31) Mutakalowa m’dziko limene Yehova Mulungu wanu “akupatsani, musamaphunzira kuchita monga mwa zonyansa za amitundu aja. Asapezeka mwa inu . . . [wofunsa] wobwebweta, kapena wopenduza, kapena wofunsira akufa.”—Deuteronomo 18:9-11; Yesaya 8:19, 20.

Ngati olankhula ndi mizimu angalankhule’di ndi akufa, pamenepa, kodi n’chifukwa ninji, lamulo la Mulungu linacha kachitidwe kao kukhala kanthu kena ‘kodetsa,’ ‘konyansa’ ndi kofunikira imfa? Mwa chitsanzo, ngati kulankhulana’ko kunali ndi okondedwa akufa, kodi n’chifukwa ninji Mulungu wa chikondi akacha kumene’ku kukhala kuswa lamulo koopsya? Kodi n’chifukwa ninji iye akafuna kuletsa amoyo kupeza mauthenga otonthoza ochokera kwa akufa? Kodi lingaliro la Mulungu’lo silikusonyeza kuti anthu sakulankhula kweni-kwnei ndi akufa kusiyapo kuti chinyengo choopsya chiyenera kulowetsedwamo? Umboni Wamalemba umasonyeza kuti ziri’di choncho.

Mothandizidwa ndi zimene’zi, lingalirani chochitika cha Sauli. Ponena za kulankhula kwake ndi Mulungu Sauli anabvomereza kuti: “Mulungu anandichokera, osandiyankha’nso, kapena ndi aneneri, kapena ndi maloto; chifukwa chake ndakuitanani [Samueli], kuti mundidziwitse chimene ndiyenera kuchita.” (1 Samueli 28:15) Mwachionekere, Mulungu sakanalola wolankhula ndi mizimu kusintha kusalankhula ndi Mulungu kumene’ku mwa kulankhula ndi mneneri wakufa’yo ndi kum’chititsa kupereka kwa Sauli uthenga wochokera kwa Mulungu. Ndiyeno’nso, mkati mwa mbali yotsirizira ya moyo wake, Samueli Iye mwini, mneneri wokhulupirika wa Mulungu, anali atasiya kugwirizana kuli konse ndi Sauli. Chifukwa cha chimene’cho, kodi sikukanakhala kosamveka, kunena kuti Samueli anali wofunitsitsa kulankhula ndi Sauli mwa njira ya wolankhula ndi mizimu, kakonzedwe kamene kanatsutsidwa ndi Mulungu?

Mwachionekere, payenera kukhala panali chinyengo cholowetsedwamo, kanthu kena kodetsa kwambiri kamene olankhula ndi mizimu ndi awo owafunsa anayenerera nako chilango cha imfa. Chinyengo chofanana’cho chiyenera kukhala kutseri kochedwa kulankhula ndi akufa lero lino.

Chosonyeza chimene’chi ndicho cheni-cheni chakuti, mosonkhezeredwa ndi oyerekezeredwa kukhala “mau” ochokera ku dziko lina’lo, anthu ambiri adzipha. Iwo ataya chuma chao chamtengo wapatali kopambana—moyo—moyesa-yesa kugwirizana ndi okondedwa akufa’wo. Ena ayamba kuopa mau otero’wo, popeza kuti mauthenga’wo akhala osakondweretsa, osimba ngozi yoopsya kapena imfa yotsala pang’ono kuchitika. Kodi ndi motani m’mene mau otero’wo angachokerere ku magwero abwino? Kodi ndani kapena n’chiani chimene chingakhale kutseri kwa mau amene’wa?

[Chithunzi patsamba 77]

Kodi anali yani amene analankhula ndi Sauli mwa njira ya wolankhula ndi mizimu ku Endori?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena